Kupita kwa asing'anga kukatengako mankhwala a chikondi

Lero ndi: Friday, Shawwal 5, 1446 7:05 AM | Omwe awerengapo: 283

Funso:

09 January, 2025

Kodi ndi zololedwa mkazi wa chisilamu kupita kwa asing’anga kuti akapeze mankhwala achikondi ndi cholinga choti akondedwe ndi mwamuna wake?

Yankho:

Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
 
Choyamba: sizili zoyenera kuti msilamu akhulupirire mu njira yotereyi ndi cholinga choti akondedwe ndi munthu wina. Amene amaika chikondi mu mtima mwa munthu ndi Allāh ndipo anthu awiri akakhala kuti akondana, mizimu yawo imakhala kuti idayanjanitsidwa kale isanaikidwe mu matupi ake.
 
Mu kuyankhula kwake ‘Ā’ishah adafotokoza kuti Mtumiki wa Allāh ﷺ adati:[1]
 
 الأَرْوَاحُ جُنُودٌ مُجَنَّدَةٌ، فَمَا تَعَارَفَ مِنْهَا ائْتَلَفَ، وَمَا تَنَاكَرَ مِنْهَا اخْتَلَفَ.
                                                     
“Mizimu ili ngati asilikali amene alembedwa ntchito; (mizimu) yomwe ili ndi zizindikiro zofanana imayanjana (imakhala pa ubwenzi); ndipo imene ili ndi zizindikiro zosiyana imadana (sizigwirizana).”
 
Mu kuyankhula kwina, ‘Amrat bint ‘Abdur-Rahmān kuti:[2]
 
كَانَ بِمَكَّةَ امْرَأَةٌ مَزَّاحَةٌ فَنَزَلَتْ عَلَى امْرَأَةٍ مِثْلِهَا، فَبَلَغَ ذَلِكَ عَائِشَةُ، فَقَالَتْ: ‌صَدَقَ ‌حِبِّي، ‌سَمِعْتُ رَسُولَ اللَّهِ صَلَّى اللهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ يَقُولُ: «الْأَرْوَاحُ جُنُودٌ مُجَنَّدَةٌ، فَمَا تَعَارَفَ مِنْهَا ائْتَلَفَ، وَمَا تَنَاكَرَ مِنْهَا اخْتَلَفَ».
 
Ku Makkah kudali mkazi wina wochita nthabwala (amakonda kuyankhula zoseketsa); ndipo iyeyu anabwera (ku Madīnah) komwe amakhala ndi mkazi wina wofanana mu zochitika ndi iyeyu (wa nthabwalanso). Izi zidamufikira ‘Ā’ishah ndipo iye adati: ‘Adanenadi zoona wachikondi wanga, ndidamumva Mtumiki wa Allāh ﷺ akufotokoza kuti, “Mizimu ili ngati asilikali amene alembedwa ntchito; (mizimu) yomwe ili ndi zizindikiro zofanana imayanjana; ndipo yomwe ili ndi zizindikiro zosiyana imadana.”’
 
Ibn Hajar (Allāh asangalale naye) pochitira ndemanga hadīth imeneyi adati:[3]
 
قَالَ الْخَطَّابِيُّ: ‌يُحْتَمَلُ ‌أَنْ ‌يَكُونَ ‌إِشَارَةً ‌إِلَى ‌مَعْنَى ‌التَّشَاكُلِ فِي الْخَيْرِ وَالشَّرِّ وَالصَّلَاحِ وَالْفَسَادِ وَأَنَّ الْخَيِّرَ مِنَ النَّاسِ يَحِنُّ إِلَى شَكْلِهِ وَالشِّرِّيرَ نَظِيرُ ذَلِكَ يَمِيلُ إِلَى نَظِيرِهِ فَتَعَارُفُ الْأَرْوَاحِ يَقَعُ بِحَسَبِ الطِّبَاعِ الَّتِي جُبِلَتْ عَلَيْهَا مِنْ خَيْرٍ وَشَرٍّ فَإِذَا اتَّفَقَتْ تَعَارَفَتْ وَإِذَا اخْتَلَفَتْ تَنَاكَرَتْ وَيُحْتَمَلُ أَنْ يُرَادَ الْإِخْبَارُ عَنْ بَدْءِ الْخَلْقِ فِي حَالِ الْغَيْبِ عَلَى مَا جَاءَ أَنَّ الْأَرْوَاحَ خُلِقَتْ قَبْلَ الْأَجْسَامِ وَكَانَتْ تَلْتَقِي فَتَتَشَاءَمُ فَلَمَّا حَلَّتْ بِالْأَجْسَامِ تَعَارَفَتْ بِالْأَمْرِ الْأَوَّلِ فَصَارَ تَعَارُفُهَا وَتَنَاكُرُهَا عَلَى مَا سَبَقَ مِنَ الْعَهْدِ الْمُتَقَدِّمِ وَقَالَ غَيْرُهُ الْمُرَادُ أَنَّ الْأَرْوَاحَ أَوَّلُ مَا خُلِقَتْ خُلِقَتْ عَلَى قِسْمَيْنِ وَمَعْنَى تَقَابُلِهَا أَنَّ الْأَجْسَادَ الَّتِي فِيهَا الْأَرْوَاحُ إِذَا الْتَقَتْ فِي الدُّنْيَا ائْتَلَفَتْ أَوِ اخْتَلَفَتْ عَلَى حَسَبِ مَا خُلِقَتْ عَلَيْهِ الْأَرْوَاحُ فِي الدُّنْيَا إِلَى غَيْرِ ذَلِكَ بِالتَّعَارُفِ.
 
Adayankhula Al-Khattwābī: “Apa zikutanthauza kufanana kwa mizimuyo ku mbali ya ubwino ndi kuipa; kulungama ndi kusochera. Anthu abwino amayedzamira mwa abwino anzawo, ndipo oipa amayedzamiranso mwa oipa anzawo. Mizimu imagwirizana ndi mizimu inzake potengera mmene idalengedwera; yabwino kapena yoipa. Ngati chilengedwe cha mizimu imeneyo chili chofanana, basi iyoyo siisemphana mu zochitika; apo ayi (ngati ili yosiyana) ndiye kuti siikhala bwino ndi wina ndi mnzake. Zikhonza kumvetsetsedwa kuti zomwe zimatanthauza apa ndi chiyambi cha chilengedwe ku dziko losaoneka; Zinafotokozedwa kuti: mizimu idalengedwa matupi asanalengedwe, ndipo inkakumana ndi ikumakambira za kutsogolo. Pamene mizimu yaikidwa m’matupi; iyoyo imadziwana wina ndi mnzake, ndipo imakhala pa ubwenzi kapena ayi potengera zomwe zidachitika m’mbuyo (isanaikidwe mu matupi).” Wina (mu gulu la ma Salaf) adati: “Zomwe zikutanthauza apa ndi zakuti pamene mizimu yalengedwa, imapangidwa mu zigawo ziwiri. Ndipo pamene yaikidwa mu matupi amene mizimu imakhalamo (matupi athuwa), iyoyo imakumana padziko lapansi pano. Choncho, iyoyo imakhala pa ubwenzi kapena pa udani, potengera ndi njira imene mizimu imeneyi yalengedwera pano pa dziko lapansi.”
 
Ibn Al-Jawzī (Allāh asangalale naye) adati:[4]
 
وَيُسْتَفَادُ مِنْ هَذَا الْحَدِيثِ أَنَّ الْإِنْسَانَ إِذَا وَجَدَ مِنْ نَفْسِهِ نُفْرَةً مِمَّنْ لَهُ فَضِيلَةٌ أَوْ صَلَاحٌ فَيَنْبَغِي أَنْ يَبْحَثَ عَنِ الْمُقْتَضِي لِذَلِكَ لِيَسْعَى فِي إِزَالَتِهِ حَتَّى يَتَخَلَّصَ مِنَ الْوَصْفِ الْمَذْمُومِ وَكَذَلِكَ الْقَوْلُ فِي عَكْسِهِ.
 
“Chomwe tikuphunzira kuchokera mu hadīth imeneyi ndi chakuti: pamene munthu akumva mu mtima mwake kusasangalatsidwa ndi wina wake yemwe amadziwika kuti ndi wolungama; ayesetse kupeza chifukwa chimene chikumupangitsa kuti amve choncho ndi cholinga choti achotse mwa iye mwini chinthu chosayenera. Chimodzimodzinso pa zomwe zili zosemphana ndi izi (ngati akukonda munthu amene ali wochita zoipa).”
 
Chomwe mukuyenera kudziwa ndi chakuti, ngati mumakonda kumayambiriro; pakadali pano ndi chiti chimene chasintha pakati pa awirinu? Nkutheka kuti vuto ndinu kapena vuto ndi iwowo. Ngati vuto muli inu, dzikonzeni. Ndipo mukadzikonza, yang’anani tsopano chomwe chasintha mwa mwamuna wanuyo ndipo chimenechonso chikonzeni mu njira yoyenerera potsatira malamulo a chisilamu (Sharī’ah).
 
Chachiwiri: ufiti, maula komanso matsenga pa chisilamu ndi kufr (kukanira). Aliyense amene wapita kwa asing’anga kukaombedza, kuchita maula, kufuna mankhwala a banja, a mwayi, a malonda, otsirikira munda ndi zina zotero ameneyo wakanira mu zomwe Allāh adavumbulutsa kwa Mtumiki Wake ﷺ. Abū Hurayrah akupereka uthenga kuti Mtumiki wa Allāh ﷺ adati:[5]
 
‌مَنْ ‌أَتَى ‌كَاهِنًا، أَوْ عَرَّافًا، فَصَدَّقَهُ بِمَا يَقُولُ، فَقَدْ كَفَرَ بِمَا أُنْزِلَ عَلَى مُحَمَّدٍ.
 
“Aliyense amene wapita kwa sing’anga kapena bimbi; ndipo wakhulupirira mu zimene wauzidwa (kapena kupatsidwa) kumeneko, ameneyo wakanira mu zomwe zidavumbulutsidwa kwa Muhammad (ﷺ).”
 
Tikaona mu kufotokoza kwa Zaynab bint Abī Mu’āwiyah Ath-Thaqafiyyah, mkazi wake wa ‘Abdullāh Ibn Mas’ūd, iye adati:[6]  
 
كَانَتْ عَجُوزٌ تَدْخُلُ عَلَيْنَا تَرْقِي مِنَ الْحُمْرَةِ، وَكَانَ لَنَا سَرِيرٌ طَوِيلُ الْقَوَائِمِ، وَكَانَ عَبْدُ اللَّهِ إِذَا دَخَلَ تَنَحْنَحَ وَصَوَّتَ، فَدَخَلَ يَوْمًا فَلَمَّا سَمِعَتْ صَوْتَهُ احْتَجَبَتْ مِنْهُ، فَجَاءَ فَجَلَسَ إِلَى جَانِبِي فَمَسَّنِي فَوَجَدَ مَسَّ خَيْطٍ فَقَالَ: مَا هَذَا؟ فَقُلْتُ: رُقًى لِي فِيهِ مِنَ الْحُمْرَةِ فَجَذَبَهُ وَقَطَعَهُ فَرَمَى بِهِ وَقَالَ: لَقَدْ أَصْبَحَ آلُ عَبْدِ اللَّهِ أَغْنِيَاءَ عَنِ الشِّرْكِ، سَمِعْتُ رَسُولَ اللَّهِ صَلَّى اللهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ يَقُولُ: ‌إِنَّ ‌الرُّقَى، وَالتَّمَائِمَ، وَالتِّوَلَةَ شِرْكٌ.
 
Padali mayi wina wokalamba amene amalowa mnyumba mwathu ndipo amatichitira Ruqyah ku nthenda ya Al-Humrah (nthenda ya pa khungu imene imatenthetsa thupi ndipo imapangitsa khungu kuti lifiire). Ndipo ife tidali ndi kama (bed) lalitali miyendo. ‘Abdullāh amati akalowa mnyumba mwathu amayeretsa kukhosi kwake ndi kutulutsa mawu. Choncho, tsiku lina analowa mnyumba mwathu ndipo mayi okalamba aja atamva mawu ake adadziphimba (kuti asaonedwe ndi ‘Abdullāh). Kenako iye (‘Abdullāh) adafika ndi kukhala pambali pa ine ndipo adandigwira mondisisita ndikupeza chingwe (pa mkono panga). Iye adati: “Ichi ndi chiyani?” Ine ndidati: “Chibangiri chodzitetezera ku Al-Humrah.” Adachichotsa, ndi kuchidula kenako anachitaya ndipo adati: “Ndithudi, banja la ‘Abdullāh silifuna Shirk. Ndidamumva Mtumiki wa Allāh ﷺ akuyankhula kuti: ‘Ndithudi, Ar-Ruqā (Ruqyah yopanga potchula maina a mafano ndi ma satana), At-Tamā’im (zodzikoleka pa thupi monga zibangiri, mikanda kapena zingwe pofuna kudziteteza ku matsenga kapena ufiti), komanso At-Tiwalah (mankhwala a chikondi, chikoka kapena mwayi) ndi Shirk.’”
 
Kuchokera mu hadīth imeneyi komanso yomwe yaperekedwa kuchokera kwa Abī Hurayrah, ndi zachidziwikire kuti munthu amene wapita kwa asing’anga ndi kukatenga mankhwala oterewa wachita Kufr (wakanira) ndipo iyeyu amatuluka mu chisilamu ngati izizi wapanga mozindikira. Ngati munthu wachita mosazindikira, iyeyu amakhala kuti wachita Shirk koma sanatuluke mu chisilamu ndipo pambuyo pozindikira za kuipa kwa Shirk, akuyenera kulapa kwa Allāh ndi kudzitalikitsa ku mchitidwe woterewu.
 
Allāh ndiye Mwini kuzindikira


[1] Swahīh Al-Bukhārī, #3336


[2] Musnad Abī Ya’lā, Vol. 7, tsamba 344, hadīth #4381


[3] Fat-hul Bārī, Vol. 6, tsamba 369


[4] Fat-hul Bārī, Vol. 6, tsamba 370


[5] Musnad Ahmad, #9536


[6] Swahīh Ibn Mājah, #3530