Anthu okwatira koma oonera mafilimu olaula

Lero ndi: Friday, Shawwal 5, 1446 7:12 AM | Omwe awerengapo: 685

Funso:

14 January, 2025

Kodi ndi chifukwa anthu ena oti ali pa banja lawo labwino kwambiri komanso chikondi chilichose cha pa banja chilipo; koma iwowo kumakonda kuonela ma video olaula? Ngati ndalakwisa mafusidwe mundikhululukira Insha Allah.

Yankho:

Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
 
Zinthu zolaula zonse; kaya zili mu mabweredwe a mafilimu, mabuku, zithunzi, nyimbo, kapena kanema, zonsezi ndi harām (zoletsedwa) popanda kukaikira kulikonse. Iyi ndi ntchito yonyasa yomwe Allāh adailetsa tikaona mu Sūrah An-Nūr:[1]
 
قُل لِّلْمُؤْمِنِينَ يَغُضُّوا مِنْ أَبْصٰرِهِمْ وَيَحْفَظُوا فُرُوجَهُمْ ذٰلِكَ أَزْكَىٰ لَهُمْ.
 
Nena kwa okhulupirira achimuna kuti atsitse maso awo komanso asunge maliseche awo; (chifukwa) zimenezo ndi zowayeretsa iwowo.
 
Komanso tikaona mu āyah yotsatirayi, Allāh akuti:[2]
 
وَقُل لِّلْمُؤْمِنٰتِ يَغْضُضْنَ مِنْ أَبْصٰرِهِنَّ وَيَحْفَظْنَ فُرُوجَهُنَّ.
 
Ndipo nena kwa akazi okhulupirira kuti atsitse maso awo ndi kusunga maliseche awo.
 
Ndipo Mtumiki wa Allāh (ﷺ), kudzera mwa Abū Sa’īd Al-Khudrī, adati:[3]
 
لاَ تَنْظُرِ الْمَرْأَةُ إِلَى عَوْرَةِ الْمَرْأَةِ وَلاَ يَنْظُرِ الرَّجُلُ إِلَى عَوْرَةِ الرَّجُلِ.
 
Mkazi asaone umaliseche wa mkazi mnzake, ndipo mwamuna asaone umaliseche wa mwamuna mnzake.
 
Mu āyah yoyamba ija (Sūrah An-Nūr 24:30), Ibn Kathīr adapereka hadīth yomwe akufotokoza Zayd Ibn Aslam kuti:[4]
 
هَذَا أَمْرٌ مِنَ اللَّهِ تَعَالَى لِعِبَادِهِ الْمُؤْمِنِينَ أَنْ يَغُضُّوا مِنْ أَبْصَارِهِمْ عَمَّا حَرَّمَ عَلَيْهِمْ، فَلَا يَنْظُرُوا إِلَّا إِلَى مَا أَبَاحَ لَهُمُ النَّظَرَ إِلَيْهِ.
 
Ichi ndi chilamulo chochokera kwa Allāh kupita kwa akapolo Ake achimuna okhulupirira kuti atsitse maso awo pa zimene zaletsedwa pa iwo (maliseche a mkazi yemwe sadamukwatire kapena mwamuna mnzake); ndipo iwo asayang’ane aliyense kupatulapo amene alolezedwa pa iwowo kuti awayang’ane.
 
Jarīr Ibn 'Abdullāh Al-Bajalī adati:[5]
 
سَأَلْتُ النَّبِيَّ صَلَّى اللَّهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ، عَنْ نَظْرَةِ الْفَجْأَةِ، فَأَمَرَنِي أَنْ أَصْرِفَ بَصَرِي.
 
Ndidamufunsa Mtumiki wa Allāh (ﷺ) za kuona kwa ngozi (chinthu cha harām) ndipo iye adandilamula kuti nditsitse maso anga.
 
Izi zikusonyeza kuti munthu ngati waona mkazi yemwe umaliseche wake ukuonekera mu nthawi yomwe ukuyenda pa nsewu, ukuyenera kutsitsa maso. Nanga mukuona bwanji za munthu yemwe wachita kukhala ndi zithunzi kapena mafilimu amene amuna ndi akazi akuonetsa maliseche awo?
 
Ibn Kathīr adati:[6]
 
وَلِذَلِكَ أَمَرَ اللَّهُ بِحِفْظِ الْفُرُوجِ كَمَا أَمَرَ بِحِفْظِ الْأَبْصَارِ الَّتِي هِيَ بَوَاعِثُ إِلَى ذَلِكَ.
 
Pa chifukwa ichi, Allāh adalamula kusunga maliseche ngati momwe ukuyenera kusunganso maso omwe ndi njira yomupitsira munthu ku zimenezo (za harām).
 
Zinthu zolaula sizithandiza banja mu njira ina iliyonse, kupatula kuti zimaliononga. Mwamuna kapena mkazi akamaonera zinthu zoterezi, amakodwa mu msampha waukulu ndipo zimakhala zovuta kuti atulukemo. Mu nthawi yomwe mwamuna ndi mkazi akuonera zoterezi, zimakhala zovuta pa iwowa kuti abweremo mu chilakolako mpakana ataonera maliseche a anthu ena. Iwo amakanika kudzutsidwa ndi akubanja kwawo.
 
Ichi ndi chifukwa chake akatswiri oona za maganizidwe a munthu (psychologists) mu nthawi yathu ino akufotokoza kuti kusakhutitsidwa ndi kugonana kumene mwamuna ndi mkazi amakhala nako kumabwera nthawi zambiri kudzera mu njira yoonera zolaula. Iwo amafuna kuti ayesere zomwe aziona mu zinthu zolaulazo, ndipo zimapangitsa mwamuna kukhala ndi chithunzithunzi cholakwika pa mkazi wake. Apa ndi pamene munthu akuyenera kuzindikira kuti Allāh pamodzi ndi Mtumiki Wake (ﷺ) saletsa chinthu pokhapokha chimakhala kuti chili ndi mavuto ambiri pa umoyo wathu.
 
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.


[1] Sūrah An-Nūr 24:30


[2] Sūrah An-Nūr 24:31


[3] Sunan Ibn Mājah, #661; Jāmi’at Tirmidhī, #2793


[4] Tafsīr Ibn Kathīr, Vol. 6, tsamba 41


[5] Swahīh Muslim, #2159; Jāmi’at Tirmidhī, #2776; Sunan Al-Kubrā, Vol. 7, tsamba 144, #13514


[6] Tafsīr Ibn Kathīr, Vol. 6, tsamba 42