Nkhani yonyamula manja popanga du'ā pakutha pa swalāh
Lero ndi: Friday, Shawwal 5, 1446 7:12 AM | Omwe awerengapo: 530
Ndimamva kuti kunyamula manja popanga du'aa ndi bid'ah, koma pali ma ahādīth ena ofotokoza za kunyamula manja, nde ndimakhala osokonezeka kwambiri ndi ziwiri zimenezi. Tsopano ndimafuna munditambasulire kuti kodi ndi swalah ziti komanso ndi nthawi ziti zimene zikuloledwa kupanga du'aa utanyamula manja?
Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
Kupanga du’ā pa Swalāh kunakhazikitsidwa ndi Mtumiki wa Allāh (ﷺ) ndipo ife tikuyenera kutsatira zomwe zidakhazikitsidwa ndi iyeyo. Abū Hurayrah adafotokoza kuti Mtumiki (ﷺ) adati:[1]
أَقْرَبُ مَا يَكُونُ الْعَبْدُ مِنْ رَبِّهِ وَهُوَ سَاجِدٌ فَأَكْثِرُوا الدُّعَاءَ.
Nthawi yomwe kapolo amakhala woyandikira kwa Mbuye wake ndi pamene ali pa Sajdah, choncho chulukitsani Ad-Du’ā (kumupempha Allāh).
Palinso malo ena pa Swalāh amene Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adaphunzitsa kuti munthu utha kupanga du’ā monga pa Jalsah yomalizira (kukhala komaliza ukamapanga Tashahhud). Werengani ma ahādīth awa: Swahīh Muslim, #589, #2697b, #2705a; Sunan Abī Dāwūd, #1481; Sunan an-Nasā’ī, #1299; Al-Adab Al-Mufrad, #690; komanso Sunan Ibn Mājah, #923.
Pamene munthu wapanga salām, pamenepo Swalāh yatha ndipo munthu ukuyenera kuchita m’menenso Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adachitira. Iye amapanga ma adhkār – kupatulapo Swalāh ya Fajr yomwe amati akapanga salām, amachita du’ā yotsatirayi koma samakweza manja ake. Umm Salamah adati:[2]
أَنَّ النَّبِيَّ صلى الله عليه وسلم كَانَ يَقُولُ إِذَا صَلَّى الصُّبْحَ حِينَ يُسَلِّمُ: اللَّهُمَّ إِنِّي أَسْأَلُكَ عِلْمًا نَافِعًا، وَرِزْقًا طَيِّبًا، وَعَمَلاً مُتَقَبَّلاً.
Mtumiki wa Allāh (ﷺ) amakonda kuyankhula akapemphera Swalāh ya Subh pamene wachita salām kuti: “Oh Allāh! Ndikukupemphani maphunziro opindulitsa, ma rizq abwino, komanso ntchito zolandiridwa.”
Koma Umm Salamah sadanene kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) amapempha du’ā imeneyi atakweza manja.
Zikufotokozedwa mu Al-Lajnah Ad-Dā’imah kuti:[3]
ليس الدعاء بعد الفرائض بسنة إذا كان برفع الأيدي، سواء كان من الإمام وحده أو المأموم وحده، أو منهما جميعا، بل ذلك بدعة؛ لأنه لم ينقل عن النبي صلى الله عليه وسلم ولا عن أصحابه رضي الله عنهم، أما الدعاء بدون ذلك فلا بأس به، لورود بعض الأحاديث في ذلك.
Kupanga du’ā pakutha pa Swalāh iliyonse ya Faradh sizili mu Sunnah ngati zingachitidwe uku manja atakwezedwa; kaya zimenezo akupanga ndi Imām yekha, kapena m’modzi mwa anthu amene amapempheretsedwa, kapenanso onse pamodzi (Imām ndi gulu lonse). Mwachidule, imeneyi ndi Bid’ah chifukwa sizikufotokozedwapo kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) kapena m’modzi wa ma Swahābah ake, Allāh asangalale nawo, kuti adachitapo. Koma ngati kuli kupanga du’ā posakweza manja vuto palibe; chifukwa pali ma ahādīth amene akufotokoza zimenezi.
Ndipo ma ahādīth ofotokoza kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) amanyamula manja popanga du’ā sakukamba za pambuyo pa kumaliza Swalāh.
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.
[1] Swahīh Muslim, #482; Sunan Abī Dāwūd, #875; Sunan an-Nasā’ī, #1137
[2] Sunan Ibn Mājah, #925
[3] Fatāwā Al-Lajnah Al-Dā’imah, Vol. 7, tsamba 103