Ndili pa banja ndi mwamuna wochita zinthu za Bid'ah
Lero ndi: Friday, Shawwal 5, 1446 7:09 AM | Omwe awerengapo: 303
Kodi ndikololedwa kukhala ndi munthu wa bid’ah ngati banja? Komanso ndi kumakuuza kuti mnyumba mwanga muno ma ulaliki a mashaykh omwe amadzudzula za bid’ah ayi kupanda kutero ndiye kuti udzatuluka.
Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
Choyambirira tidziwe kuti Bid’ah ndi chiyani.
Tikabwera pa Sharī’ah, Bid’ah ndi chinthu chomwe chili chokhudza nkhani ya 'ibādah imene Allāh pamodzi ndi Mtumiki Wake (ﷺ) sadatilamule. Ntchitoyi imachitidwa ndi chiyembekezo choti munthu apeza malipiro kuchokera kwa Allāh.
Adayankhula Imām Ash-Shātwibī kuti:[1]
الْبِدْعَةُ طَرِيقَةٌ فِي الدِّينِ مُخْتَرَعَةٌ، تُضَاهِي الشَّرْعِيَّةَ) يَعْنِي أَنَّهَا تُشَابِهُ الطَّرِيقَةَ الشَّرْعِيَّةَ مِنْ غَيْرِ أَنْ تَكُوْنَ فِي الْحَقِيقَةِ كَذَلِكَ(، يُقْصَدُ بِالسُّلُوْكِ عَلَيْهَا مَا يُقْصَدُ بِالطَّرِيْقَةِ الشَّرْعِيَّةِ.
Bid’ah ndi chinthu chatsopano chimene chabweretsedwa mu chipembedzo, chomwe chimafanana ndi Sharī’ah; chimene kuyandikira kwa Allāh kumachitidwa (kudzera mu icho) koma chimakhala chopanda potsamira (umboni) kuchokera mu Njira ya Sharī’ah.
Chachiwiri ndi kudziwa magulu a Bid’ah.
Bid’ah ili pawiri: Bid’ah yaikulu yomwe mkati mwake muli Shirk komanso kutsutsana kwambiri ndi chiphunzitso cha Mtumiki wa Allāh (ﷺ). Monga omwe amapempha mizimu amachita Bid’ah yaikulu; amene amaika zithumwa mnyumba; omwe amaonjezera zinthu zina pamwamba pa zimene Allāh ndi Mtumiki Wake (ﷺ) adakhazikitsa ngati kuswali Jumu’ah kenako ndi kudzaswali Dhuhr; omwe amapungula zina mu ntchito zokhazikitsidwa mu Chisilamumu monga kuvala hijab yosakwanira pomaonetsa zigawo zina za thupi kapena maonekedwe a thupilo chifukwa cha kuthina kwa chovala; ngakhalenso omwe amakana zilamulo za Allāh ndi Mtumiki Wake (ﷺ) ndi kutenga maganizo a ena ngati omwe amakana mkazi kuti sangazinge nyama. Bid’ah yaikulu imeneyi imamutulutsa munthu mu Chisilamu ngati akuichita mozindikira.
Ndiye pali Bid’ah yaing’ono imene mkati mwake mulibe Shirk iliyonse komanso siitsutsana kwambiri ndi ziphunzitso za Mtumiki wa Allāh (ﷺ). Monga, kupuputa ku nkhope pambuyo pomaliza Swalāh; kukweza manja popanga du’ā pambuyo pa Swalāh; kapena kunena kuti “fī amanillāh mukamasiyana wina ndi mnzake.”
Tikaiona Bid’ah, chimene imatanthauza nchakuti: chisilamu ndi chosakwanira mpaka titapanga izi. Pomwe Allāh adachikwaniritsa kale Chisilamuchi Mtumiki Wake (ﷺ) asanamwalire. Ichi ndi chifukwa chake Allāh samalandira ntchito za munthu wa Bid’ah, monga momwe akuyankhulira Hishām Ibn Hassān adati:[2]
لَا يَقْبَلُ اللَّهُ مِنْ صَاحِبِ بِدْعَةٍ صِيَامًا، وَلَا صَلَاةً، وَلَا زَكَاةً، وَلَا حَجًّا، وَلَا جِهَادًا، وَلَا عُمْرَةً، وَلَا صَدَقَةً.
Allāh salandira kuchokera kwa munthu wa Bid’ah kusala kwake, swalāh yake, zakāh yake, Hajj yake, Jihad yake, ‘Umrah yake komanso swadaqah yake.
Ma Swahābah adali akumawachenjeza ophunzira awo zokhudzanso Bid’ah. Akuyankhula Abū Wā’il kuti:[3]
عَنْ حُذَيْفَةَ بْنِ الْيَمَانِ: أَنَّهُ أَخَذَ حَجَرَيْنِ فَوَضَعَ أَحَدَهُمَا عَلَى الْآخَرِ ثُمَّ قَالَ لِأَصْحَابِهِ: هَلْ تَرَوْنَ مَا بَيْنَ هَذَيْنِ الْحَجَرَيْنِ مِنَ النُّورِ؟ قَالُوا: يَا أَبَا عَبْدِ اللَّهِ، مَا نَرَى بَيْنَهُمَا مِنَ النُّورِ إِلَّا قَلِيلًا، قَالَ: وَالَّذِي نَفْسِي بِيَدِهِ، لَتَظْهَرَنَّ الْبِدَعُ حَتَّى لَا يُرَى مِنَ الْحَقِّ إِلَّا قَدْرُ مَا تَرَوْنَ مَا بَيْنَ هَذَيْنِ الْحَجَرَيْنِ مِنَ النُّورِ، وَاللَّهِ لَتَفْشُوَنَّ الْبِدَعُ حَتَّى إِذَا تُرِكَ مِنْهَا شَيْءٌ قَالُوا: تُرِكَتِ السُّنَّةُ.
Hudhayfah Ibnil Yamān adatenga miyala iwiri ndipo adatsamiridwa mwala wina pamwamba pa mwala unzake kenako adati kwa ophunzira ake: “Kodi mukuonapo kuwala pakati pa miyala iwiriyi?” Iwo adati: “Eh iwe Abū Abdur-Rahmān! Sitikuonapo pakati pa miyala iwiriyo kupatula kuwala kochepa kwambiri.” Iye adati: “Ndikulumbira mwa Yemwe mzimu wanga uli M’Dzanja Lake! Idzaonekera poyera Bid’ah mpaka simudzaona kuchokera mu Chilungamo (Sunnah) kupatulapo ngati m’mene mwakwaniritsira kuona kuwala komwe kuli pakati pa miyala iwiriyi. Ndikulumbira mwa Allāh! Idzafalikira Bid’ah mpaka zidzafika poti ngati wina angadzaisiye imodzi mu ntchito za Bid’ah, zidzayankhulidwa kuti: Wasiya Sunnah.”
Anthu ochita Bid’ah ndi adani a Allāh pamodzi ndi Mtumiki Wake (ﷺ) malinga ndi m’mene akuyankhulira Anas Ibn Mālik kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[4]
إِنَّ اللَّهَ حَجَبَ التَّوْبَةَ عَنْ صَاحِبِ كُلِّ بِدْعَةٍ.
Ndithudi Allāh amatseka kulapa kwa munthu aliyense wa Bid’ah (mu nthawi yomwe akuchita Bid’ah yakeyo).
Ayyūb As-Sakhtiyānī adati:[5]
مَا ازْدَادَ صَاحِبُ بِدْعَةٍ اجْتِهَادًا إِلَّا ازْدَادَ مِنَ اللَّهِ بُعْدًا.
Samachulukitsa munthu wa Bid’ah kuchilimika kwambiri (mu Bid’ah yake), kupatula kuti amaonjezera kutalikirana kwambiri ndi Allāh.
Pa chifukwa ichi, mkazi kukwatiwana ndi mwamuna wa Bid’ah ndi zinthu zoletsedwa; komanso mwamuna kukwatira mkazi wa Bid’ah ndi zoletsedwa. Izi zili choncho potengera ndi ma ahādīth amene Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adaunikiramo za munthu woyenerera kukhala naye pa banja.
Mu kuyankhula kwake Thawbān, iye adati Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adatiuza kuti:[6]
لِيَتَّخِذْ أَحَدُكُمْ زَوْجَةً مُؤْمِنَةً تُعِينُ أَحَدَكُمْ عَلَى أَمْرِ الآخِرَةِ.
“M’modzi wa inu apeze mkazi wokhulupirira amene angamuthandize iye ku za moyo womwe uli mkudza.”
Palibe mwamuna amene ali ndi mkazi wochita za Bid’ah ndi kukhala wothandizidwa ku zinthu za ku Ākhirah. Chifukwa mkazi wa Bid’ah zochita zake zimakhala zosemphana ndi moyo umene uli mkudza. Iye samamuthandiza mwamuna wake pa zabwino ndipo samamuletsa ku zoipa.
Womuyang'anira mkazi (walī) akuyenera kupeza kapena kuvomera mwamuna wodziwa bwino chipembedzo chake komanso wotsatira, tsiku ndi tsiku, malamulo a chisilamu (Sharī’ah). Yemwe sakwaniritsa zomwe walamulidwa ndi Allāh ndi zosavuta kwa iye kusakwaniritsanso zofuna za ena. Wokhulupirira weniweni sapondereza mkazi wake komanso samuchitira nkhanza mkaziyo mu njira ina iliyonse ndipo samamukokera ku Bid’ah.
Abū Hurayrah akufotokoza kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[7]
إِذَا أَتَاكُمْ مَنْ تَرْضَوْنَ خُلُقَهُ وَدِينَهُ فَزَوِّجُوهُ إِلاَّ تَفْعَلُوا تَكُنْ فِتْنَةٌ فِي الأَرْضِ وَفَسَادٌ عَرِيضٌ.
Akakufikirani mwamuna amene ali ndi khalidwe labwino komanso ochilimika pa chipembedzo chake, mukwatitseni (kwa ana anu aakazi); chifukwa ngati simuchita zimenezo, padzakhala mayesero pa dziko komanso uchimo udzachuluka.
Mwamuna wodziwa bwino chipembedzo chake ndi amene amakonza banja lake kuti liyende molingana ndi chiphunzitso cha Qur’ān komanso Sunnah osati maganizo ake kapena za agogo ake. Amamuletsa mkazi wake kuchita zinthu zosemphana ndi Sharī’ah ndipo salola kuti zilakolako za mkaziyo zikhale pamwamba pa Sharī’ah. Iye amakhala mtsogoleri weniweni.
Pa chifukwa ichi, Al-Fudhwayl Ibn ‘Iyādhw adati:[8]
ومن زَوَّجَ كَريمتَهُ مبتدع فقدْ قطَعَ رَحِمَهَا.
Ndipo aliyense amene wakwatitsa mwana wake wa mkazi kwa mwamuna wa Bid’ah, ameneyo wadula ubale ndi mwanayo.
Mwamuna ameneyo muchenjezeni kuti asiye Bid’ah. Ndipo ngati sakufuna kusiya, auzeni anthu ena amuunikire za kuopsa kwa Bid’ah. Akakanika kusiya, zabwino zake ndi kumuuza kuti akusiyeni banja chifukwa pamenepo zikhala zoletsedwa kwa inu kukhala mu banja ndi mwamuna wotereyu.
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.
[1] Al-I’tiswām li Ash-Shātwibī, Vol. 1, tsamba 47
[2] Al-Bid’ wan Nahy ‘anha, tsamba 62, hadīth #68
[3] Al-Bid’ wan Nahy ‘anha, tsamba 144, hadīth #151
[4] Al-Mu’jamal Awsat, #4202; Swahīh At-Targhīb wa At-Tarhīb, #54
[5] Al-Bid’ wan Nahy ‘anha, tsamba 62, hadīth #67
[6] Sunan Ibn Mājah, #1856
[7] Sunan Ibn Mājah, #1967
[8] Sharh As-Sunnah lil Barbahārī, #137