Kodi Âqīdah ndi chiyani?

Lero ndi: Friday, Shawwal 5, 1446 7:10 AM | Omwe awerengapo: 263

Funso:

23 January, 2025

Ndimafuna kudziwa tanthauzo la Âqīdah.

Yankho:

Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
 
Liwu lakuti Âqīdah limachokera ku tsinde la mawu a chi ‘Arab otchedwa ‘aqada “adamangitsa.” Ndipo liwuli (Âqīdah) lili ndi matanthauzo awiri: pa chiyankhulo komanso pa Sharī’ah[1]. Tikabwera pa chiyankhulo, Âqīdah imafotokozedwa kuti ndi:[2]
 
‌مَا ‌عقد ‌عَلَيْهِ ‌الْقلب.
 
“Chomwe chamangidwa mu mtima.”
 
Mu kuyankhula kwawo Shaykh Ibn Jibrīn adati:[3]
 
ما ‌عقد ‌عليه ‌القلب وتمسك به. فالعقد أصله ‌انْعِقادُ القلب على الشيء.
 
“Chomwe chamangidwa mu mtima ndi kumatsatiridwa.” Tsopano Al-‘Aqd (mgwirizano) tsinde lake ndi chikhulupiriro cha mtima pa china chake.
 
Ena mwa ma ‘ulamā’ adati:[4]
 
العَقِيْدَةُ فِيْ اللُّغَةِ: مِنَ الْعَقْدِ؛ وَهُوَ الرَّبْطُ،... وَالشَّدُّ بِقُوَّةِ، والتَّمَاسُكُ...
 
Âqīdah pa chiyankhulo: liwuli limachokera ku Al-‘Aqd; yomwe ndi Kumangitsa,… komanso kumanga mwa mphamvu, kugwiritsa…
 
Tsopano tikayang’ana mu kafotokozedwe kena kapaderadera, Âqīdah ndi:[5]
 
وَالْعَقِيدَةُ فِي الاصْطِلاح: الْإِيمَانُ الْجَازِمُ بِاللَّهِ تَعَالَى، وَبِمَا يَجِبُ لَهُ مِنَ التَّوْحِيدِ، وَالْإِيمَانُ بِمَلَائِكَتِهِ وَكُتُبِهِ، وَرُسُلِهِ، وَالْيَوْمِ الْآخِرِ، وَالْقَدَرِ خَيْرِهِ وَشَرِّهِ، وَبِمَا يَتَفَرَّعُ عَنْ هَذِهِ الْأُصُولِ وَيُلْحَقُ بِهَا مِمَّا هُوَ مِنْ أُصُولِ الدِّينِ.
 
 
Ndipo Âqīdah mu kufotokoza kwa paderadera: (ndi) Chikhulupiriro chokhazikika mwa Allāh Wapamwambamwamba, komanso ndi zomwe zili zokakamizika mu chikhulupirirochi kuchokera mu Tawhīd. Komanso kukhulupirira mwa Angelo Ake, Mabuku Ake, Atumiki Ake, Tsiku la Chiweruzo, komanso mu Qadar – zabwino zake ndi zoipa zake (zomwe zimadza ndi Qadar). Ndi chilichonse chimene chimatuluka kuchokera mu masinde amenewa komanso chatsamira masindewo; chimenecho ndi chochokera mu masinde a Chipembedzo.
 
Tikabwera pa Sharī’ah, tipeza kuti Âqīdah ndi:[6]
 
أَمَّا الْعَقِيدَةُ الإِسْلَامِيَّةُ: فَهِيَ تَعْنِي: الْيَقِينَ وَالتَّسْلِيمَ وَالْإِيمَانَ الْجَازِمَ بِاللهِ، وَمَا يَجِبُ لَهُ مِنَ التَّوْحِيدِ وَالْعِبَادَةِ وَالطَّاعَةِ، ثُمَّ بِمَلَائِكَتِهِ وَكُتُبِهِ وَرُسُلِهِ وَالْيَوْمِ الْآخِرِ وَالْقَدَرِ وَسَائِرِ أُصُولِ الإِيمَانِ، ثُمَّ أَرْكَانِ الْإِسْلَامِ، وَالْقَطْعِيَّاتِ الْأُخْرَى، وَهِيَ كَثِيرَةٌ؛ كَالشَّفَاعَةِ وَالرُّؤْيَةِ، وَالأُمُورِ الْعَمَلِيَّةِ الَّتِي هِيَ مِنْ قَطْعِيَّاتِ الدِّينِ؛ كَالْأَمْرِ بِالْمَعْرُوفِ وَالنَّهْيِ عَنِ الْمُنْكَرِ وَالْجِهَادِ، وَالْحُبِّ فِي اللَّهِ وَالْبُغْضِ فِي اللهِ، وَنَحْوِ ذَلِكَ مِمَّا يَنْدَرِجُ فِي الْوَاجِبَاتِ، وَفِي الْعِلَاقَاتِ بَيْنَ الْمُسْلِمِينَ كَحُبِّ الصَّحَابَةِ رضي الله عنهم، وَحُبِّ السلفِ الصالحِ، وَحُبِّ الْعُلَمَاءِ، وَحُبِّ الصَّالِحِينَ، وَنَحْوِ ذَلِكَ مِمَّا هُوَ مُنْدَرِجٌ فِي أُصُولِ الِاعْتِقَادِ وَثُوَابَتِهِ.
 
Tsopano Âqīdah ya Chisilamu; imeneyo imatanthauza: Al-Yaqīn (Kusakaikira), komanso At-Taslīm (Kugonjera) komanso Chikhulupiriro Chokhazikika mwa Allāh, ndi (kuphatikizanso) zomwe zili zokakamizidwa kuchokera mu At-Tawhid, Al-‘Ibādah ndi At-Twā’ah. Kenako kukhulupiriranso mwa angelo Ake, mabuku Ake, atumiki Ake, ndi Tsiku la Chiweruzo komanso Qadar ndi masinde onse a Chikhulupiriro. Pambuyo pake (ugwiritse mu) nsanamira za Chisilamu ndi zigawo zina zomwe zilipo zochuluka monga; Ash-Shafā’ah, Ar-Ru’yah, ndi Ntchito zomwe zili zidutswa za Chipembedzo monga; Kulamula Zabwino ndi Kuletsa Zoipa, Jihad, Kukonda chifukwa cha Allāh komanso Kunyasidwa chifukwa cha Allāh, ndi zina kuchokera mu zinthu zokakamizidwa. Komanso ndi ubale umene ulipo pakati pa asilamu monga chikondi pa ma Swahābah (Allāh asangalale nawo), kukonda ma Salaf, kukonda ma ‘ulamā’, kukonda anthu olungama, ndi zina zotero zimene zikugwera mu mapata a Zikhulupiriro ndi zomwe zikuyenera kukhazikika (ku mbali ya Zikhulupirirozo).
 
Mwachidule, pa Sharī’ah, Âqīdah ndi:[7]
 
‌هي ‌الأمور ‌التي ‌تُصَدِّقُ ‌بِهَا ‌النفوس، وَتَطْمَئِنُّ ‌إِلَيْهَا القلوب، وتكون يقينًا عند أصحابها، لا ‌يُمازِجُها رَيْبٌ، ولا ‌يُخَالِطُهَا شَكٌّ.
 
Ikuimira zinthu zimene mizimu imakhulupirira, ndipo mitima imakhutitsidwa ndi izo, komanso ziwalo sizikhala zokaikira pa izo, ndipo zinthuzi sizionongedwa ndi chikaiko chilichonse kapena kupenekera kwina kulikonse.
 
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.


[1] Sharī’ah imatanthauza malamulo ochokera kwa Allāh amene Iye adawapereka kwa ife ndi cholinga chotiteteza pa dziko pano komanso mu umoyo womwe uli nkudza.


[2] Qawā’id Al-Fiqh, tsamba 383


[3] Fatāwā ash-Shaykh Ibn Jibrīn, Vol. 63, tsamba 162


[4] It-hāfu dhawil ‘Uqūlir Rashīdah bi sharhil Bidāyah fil Âqīdah, tsamba 24


[5] It-hāfu dhawil ‘Uqūlir Rashīdah bi sharhil Bidāyah fil Âqīdah, tsamba 25


[6] It-hāfu dhawil ‘Uqūlir Rashīdah bi sharhil Bidāyah fil Âqīdah, tsamba 25


[7] Usūl Ad-Da’wah wa turquha, tsamba 60