Kodi ndizololedwa kumupempha Mtumiki wa Allaah kapena anthu olungama omwe adamwalira
Lero ndi: Friday, Shawwal 5, 1446 7:08 AM | Omwe awerengapo: 294
Ndimafuna kudziwa nawo ngatidi zili zololedwa kupempha kwa anthu omwe adamwalira monga Mtumiki wa Allaah komanso ma Swahaabah ngakhalenso anthu olungama amene anabwera pambuyo pawo. Izizi zili choncho chifukwa tikumva ena akuti izizi ndi zololedwa ndipo vuto palibe pomwe ena akuti izizi ndi Shirk. Chonde tiunikireni.
Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
Pali hadīth yomwe imakamba za mwamuna wa khungu imene ma Sūfiyyah (anthu opempha omwe ali m’manda) amaigwiritsira ntchito kuti ndi chilolezo chawo chomupemphera Mtumiki wa Allāh (ﷺ) mavuto awo.
‘Uthmān Ibn Hunaif akufotokoza kuti:[1]
أَنَّ رَجُلاً، ضَرِيرَ الْبَصَرِ أَتَى النَّبِيَّ صلى الله عليه وسلم فَقَالَ: ادْعُ اللَّهَ أَنْ يُعَافِيَنِي. قَالَ: "إِنْ شِئْتَ دَعَوْتُ وَإِنْ شِئْتَ صَبَرْتَ فَهُوَ خَيْرٌ لَكَ." قَالَ: فَادْعُهُ. قَالَ: فَأَمَرَهُ أَنْ يَتَوَضَّأَ فَيُحْسِنَ وُضُوءَهُ وَيَدْعُوَ بِهَذَا الدُّعَاءِ: "اللَّهُمَّ إِنِّي أَسْأَلُكَ وَأَتَوَجَّهُ إِلَيْكَ بِنَبِيِّكَ مُحَمَّدٍ نَبِيِّ الرَّحْمَةِ إِنِّي تَوَجَّهْتُ بِكَ إِلَى رَبِّي فِي حَاجَتِي هَذِهِ لِتُقْضَى لِي اللَّهُمَّ فَشَفِّعْهُ فِيَّ."
Mwamuna wina wosaona anabwera kwa Mtumiki (ﷺ) ndipo adati: “Ndipangire du’ā kwa Allāh kuti andichize.” Iye (ﷺ) adati: “Ngati ukufuna ndikupangira du’ā, ndipo ngati ukufuna, utha kupirira, chifukwa zimenezo zikhala zabwino kwa iwe.” Mwamuna uja adati: “Basi mpemphe Iye (Allāh).” Uthmān adati: Choncho Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adamulamula mwamunayo kuti apange wudhū’ ndipo apange mwa dongosolo, ndipo apange du’ā yotsatirayi: Allāhumma innī as’aluka wa atawajjahu ilaika binabiyyika Muhammadin nabiyyir-rahmati, innī tawajjahtu bika ilā rabbī fī hājatī hādhihī lituqdhwā lī, Allāhumma fashaffi`hu fīyya [O Allāh, ndikukupemphani Inu ndi kutembenukira kwa Inu kudzera mwa Mtumiki Wanu Muhammad (ﷺ), Mtumiki wa chisoni. Ndithudi, ndatembenukira kudzera mwa Inu kwa Mbuye wanga, mu vuto langali, ndi cholinga choti lichotsedwe. O Allāh, mvomereni (Mtumikiyo) pempho lake pa ine].
Mu hadīth ya Ahmad, ‘Uthmān adati:[2]
فَأَمَرَهُ أَنْ يَتَوَضَّأَ، فَيُحْسِنَ وُضُوءَهُ، وَيُصَلِّيَ رَكْعَتَيْنِ، وَيَدْعُوَ بِهَذَا الدُّعَاءِ: اللهُمَّ إِنِّي أَسْأَلُكَ، وَأَتَوَجَّهُ إِلَيْكَ بِنَبِيِّكَ مُحَمَّدٍ نَبِيِّ الرَّحْمَةِ، يَا مُحَمَّدُ، إِنِّي تَوَجَّهْتُ بِكَ إِلَى رَبِّي فِي حَاجَتِي هَذِهِ، فَتَقْضِي لِي، اللهُمَّ شَفِّعْهُ فِيَّ.
Choncho [Mtumiki wa Allāh (ﷺ)] adamulamula mwamunayo kuti apange wudhū’ ndipo apange wudhū’ mwa dongosolo, ndipo aswali kenako apange du’ā yotsatirayi: Allāhumma innī as’aluka wa atawajjahu ilaika binabiyyika Muhammadin nabiyyir-rahmati, yā Muhammad, innī tawajjahtu bika ilā rabbī fī hājatī hādhihī lituqdhwā lī, Allāhumma fashaffi`hu fīyya [O Allāh, ndikukupemphani Inu ndi kutembenukira kwa Inu kudzera mwa Mtumiki Wanu Muhammad (ﷺ), Mtumiki wa chisoni. Eh iwe Muhammad! Ine ndatembenukira kudzera mwa iwe kwa Mbuye wanga, mu vuto langali, ndi cholinga choti lichotsedwe. O Allāh, mvomereni (Mtumikiyo) pempho lake pa ine].
Kuchokera mu hadīth imeneyi, tipezamo zinthu zokwanira zisanu ndi mphambu imodzi (6) malingana ndi kufotokoza kwa Shaykh Al-Albānī (Allāh awachitire chisoni):[3]
1. Mwamuna wosaonayu anabwera kwa Mtumiki (ﷺ) pa chifukwa chimodzi basi. Iyeyu adamupempha Mtumiki (ﷺ) kuti apange du'aa kwa Allaah kuti amuchize iyeyu - pamene munthuyu adati: “Ndipangire du’ā kwa Allāh kuti andichize.” Iyi ndi taqarrub (kudziyandikitsa) kwa Allāh kudzera mu du'aa ya Mtumiki Wake (ﷺ). Mwamunayu amadziwa kuti du’ā ya Mtumiki (ﷺ) imayankhidwa poyerekeza ndi du’ā ya wina aliyenseyo. Ngati mwamunayu amafuna kuchita Tawassul yomwe anthu awawa amainena ija, panalibenso chifukwa chopitira kwa Mtumiki (ﷺ) ndi kukamupempha kuti apange du'ā. Akanangopanga zimenezo kwawoko popanga du’ā kuti: Oh Allāh, ndichizeni kudzera mwa Mtumiki Wanu (ﷺ).
2. Mtumiki (ﷺ) adalonjeza kuti amupangira mwamunayu du'aa pamene adayankhula kuti: “Ngati ukufuna ndikupangira du’ā (kwa Allaah), ndipo ngati ukufuna, utha kupirira, chifukwa zimenezo zikhala zabwino kwa iwe.”
3. Mwamunayu adaumirirabe kuti Mtumiki (ﷺ) apangebe du’ā pamene adayankhula kuti: “Basi mupemphe Iye (Allāh).” Izi zikutisonyezera kuti Mtumiki (ﷺ) adapangadi du'aa ija chifukwa iyeyo (Mtumikiyo) adali pamwamba pa anthu omwe amakwaniritsa malonjezo awo. Atapanga du’ā, adamuuza mwamunayu tawassul yovomerezeka yomwe ndi yodzera mu ntchito zabwino. Adamuuza kuti apange wudhu' ndipo apemphere ma raka’āt awiri ngati momwe Ahmad adasungira hadīth imeneyi mu Musnad yake[4]. Ndipo adamuuza mawu amene atayankhule pa swalapo.
4. Mfundo yachitatuyi ikutsindika zoti Allāh adalandira du’ā ya munthuyu kudzera mu du’ā imene adapanga Mtumiki (ﷺ) kumayambiriroko. Pamenepo ndi pamene pakubwera mawu oti: "binabiyyika Muhammadin."
5. Tawassul imeneyi siikutanthauza kupempha kudzera mwa munthu. Koma ikutanthauza kupempha kudzera mu du'aa ya munthu amene ali moyo. Pofuna kutambasula momveka bwino, mwamuna uja adamupempha Allaah kuti: "Allaah ndichizeni kudzera mu du’ā imene wakupemphani Mtumiki Wanu Muhammad (ﷺ)."
6. Imām Al-Bayhaqī pamodzi ndi ena, adaisunga hadīth imeneyi pa Bāb (Gawo) yofotokoza zizindikiro za utumiki (dalā’il an-Nubuwwah). Izi zikutitsimikizira kuti kuchizika kumene adachizika wosaonayu ndi chifukwa cha Du’ā imene adapanga Mtumiki wa Allāh (ﷺ).
Mfundo zimenezi zikutiunikira kuti mwamunayu sadamupemphe Mtumiki wa Allāh (ﷺ) atamwalira. M’malo mwake adachita izizi Mtumikiyo ali moyo. Ndipo pambuyo pa kuchita zimenezi, sitidamvepo hadīth ya Swahīh (ya mphamvu) imene ikutifotokozera kuti kunabweranso munthu wina amene adamupempha Mtumiki wa Allāh (ﷺ) m’manda mwake kuti amupemphere kwa Allāh za kusaona kwake ndi cholinga choti achizidwe.
Tikabwera mu chiyankhulo cha chi Arab, mawu amatha kukhala kuti alimo mu chiganizo ngakhale asatchulidwemo. Mwachitsanzo, tikabwera mu Qur’ān, tipeza mawu oti:[5]
وَاسْأَلِ الْقَرْيَةَ الَّتِي كُنَّا فِيهَا وَالْعِيْرَ الَّتِي أَقْبَلْنَا فِيهَا وَإِنَّا لَصَادِقُونَ.
Ufunseni mzindawo womwe ife tinali, komanso gulu la amalonda lomwe tabwerera nalo; ndithudi ife tikunena zoona.
Muona kuti ndi zosatheka kufunsa mzinda kupatulapo kuti mawu amenewa mkati mwakemo muli liwu loti “anthu”. Ndiye potambasula, tinena kuti: “Muwafunse anthu a mu mzinda umene tinali.”
Chimodzimodzinso mu hadīth imeneyi muli mawu oti: “Ndikukupemphani Allāh kudzera mu du’ā imene wapanga Mtumiki Wanu.”
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.
[1] Sunan at-Tirmidhī, #3578 (hadīth ya swahīh malinga ndi Shaykh Al-Albānī)
[2] Musnad Ahmad, #17240
[3] At-Tawassul Anwā‘uhu wa Ahkāmuhu, tsamba 70-75
[4] Musnad Ahmad, #17240
[5] Sūrah Yūsuf 12:82