Kuwapempha omwe ali kumanda chifukwa iwowo ali moyo

Lero ndi: Friday, Shawwal 5, 1446 7:11 AM | Omwe awerengapo: 331

Funso:

25 January, 2025

Ndidawamva ena akutsindika kuti Mtumiki wa Allaah komanso ena mu gulu la anthu olungama ali moyo m'manda mwawo ndipo amatimva tikamayankhula. Pa chifukwa ichi, palibe vuto kuwapempha iwowo kuti atipemphere kwa Allaah mavuto athu. Kodi izizi ndi zoona?

Yankho:

Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
 
Anthu amenewa adanamiza mitundu ya asilamu osazindikira kuti palibe vuto kupempha thandizo kudzera mwa anthu olungama amene adamwalira ali okondedwa kwambiri ndi Allāh. Iwo amapereka hadīth kuchokera kwa Anas Ibn Mālik, Abū Ayyūb Al-Answārī komanso Jābir Ibn ‘Abdullāh omwe akufotokoza kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[1]
 
إِنَّ أَعْمَالَكُمْ تُعْرَضُ عَلَى أَقَارِبِكُمْ ‌وَعَشَائِرِكُمْ ‌مِنَ ‌الْأَمْوَاتِ، ‌فَإِنْ ‌كَانَ ‌خَيْرًا، اسْتَبْشَرُوا بِهِ، وَإِنْ كَانَ غَيْرَ ذَلِكَ، قَالُوا: اللهُمَّ لَا تُمِتْهُمْ حَتَّى تَهْدِيَهُمْ كَمَا هَدَيْتَنَا.
 
Ndithudi ntchito zanu zimaonetsedwa kwa abale anu komanso kwa omwe mumakhala nawo mu gulu la omwalira. Zikapezeka kuti ntchitozo ndi zabwino, iwo amasangalala nazo. Koma zikapezeka kuti sizili choncho (ndi zoipa), iwo amayankhula kuti: “Oh Allāh! Musawamwaliritse mpaka ataongoka ngati momwe mudationgolera ife.”  
 
Hadīth imeneyi ndi yofooka chifukwa cha kupezeka kwa Maslamah Ibn ‘Ulayy Al-Khushanī Ash-Shāmī yemwe anthu odziwa ma ahādīth adamupanga kuti ndi wofooka ndipo ma ahādīth ake sakuyenera kugwiritsidwa ntchito.
 
Yahyā Ibn Ma’īn adati:[2]
 
‌مَسْلَمَةُ ‌بْنُ ‌عُلَيٍّ ‌الْخُشَنِيُّ لَيْسَ بِشَيْءٍ.
 
Maslamah Ibn ‘Ulayy Al-Khushanī alibe ntchito (siwofunikira ku nkhani ya ma ahādīth).
 
Pa chifukwa ichi, hadīth yoti ntchito zathu zimaonetsedwa kwa omwalira ndi yosalondola. Ndipo ma Sūfiyyah amakakamirabe kuti hadīth imeneyi ndi yabwinobwino ndipo amaigwiritsira ntchito.
 
Abū Hurayrah adayankhula kuti:[3]
 
‌تُرْفَعُ ‌لِلْمَيِّتِ ‌بَعْدَ ‌مَوْتِهِ ‌دَرَجَتُهُ. ‌فَيَقُولُ: ‌أَيْ ‌رَبِّ، ‌أَيُّ ‌شَيْءٍ ‌هَذِهِ؟ ‌فَيُقَالُ: ‌وَلَدُكَ ‌اسْتَغْفَرَ ‌لَكَ.
 
Amakwezedwa darajah (kukhala wa pamwamba) munthu womwalira pambuyo pa imfa yake. Choncho iye amayankhula kuti: “Mbuye wanga, zakhala bwanji chonchi?” Ndiye zimayankhulidwa kuti: “Mwana wako wakupemphera chikhululuko.”
 
Apa hadīth imeneyi ikutiphunzitsa kuti munthu womwalira alibe mphamvu yoti angamayankhulane ndi munthu wa moyo. Zikanati zili choncho, onse omwalira bwenzi akudziwa kuti ana awo akuwapemphera chikhululuko ndipo sibwenzi akumamufunsanso Allāh zinthu zoti akuzidziwa kale. Palinso hadīth ina yomwe akuifotokoza Jābir Ibn ‘Abdullāh kuti:[4]
 
لَمَّا قُتِلَ عَبْدُ اللَّهِ بْنُ عَمْرِو بْنِ حَرَامٍ يَوْمَ أُحُدٍ لَقِيَنِي رَسُولُ اللَّهِ صلى الله عليه وسلم فَقَالَ:‏ يَا جَابِرُ! مَا لِي أَرَاكَ مُنْكَسِرًا‏؟ قُلْتُ: يَا رَسُولَ اللَّهِ! اسْتُشْهِدَ أَبِي قُتِلَ يَوْمَ أُحُدٍ وَتَرَكَ عِيَالاً وَدَيْنًا.‏ قَالَ:‏ أَفَلاَ أُبَشِّرُكَ بِمَا لَقِيَ اللَّهُ بِهِ أَبَاكَ؟‏ قَالَ قُلْتُ: بَلَى يَا رَسُولَ اللَّهِ!‏ قَالَ:‏ مَا كَلَّمَ اللَّهُ أَحَدًا قَطُّ إِلاَّ مِنْ وَرَاءِ حِجَابٍ، وَأَحْيَا أَبَاكَ فَكَلَّمَهُ كِفَاحًا؛ فَقَالَ: يَا عَبْدِي! تَمَنَّ عَلَىَّ أُعْطِكَ.‏ قَالَ: يَا رَبِّ! تُحْيِينِي فَأُقْتَلَ فِيكَ ثَانِيةً.‏ قَالَ الرَّبُّ عَزَّ وَجَلَّ: إِنَّهُ قَدْ سَبَقَ مِنِّي أَنَّهُمْ إِلَيْهَا لاَ يُرْجَعُونَ.‏ قَالَ يَا رَبِّ! فَأَبْلِغْ مَنْ وَرَائِي.‏ قَالَ فَأَنْزَلَ اللَّهُ تَعَالَى ‏{وَلاَ تَحْسَبَنَّ الَّذِينَ قُتِلُوا فِي سَبِيلِ اللَّهِ أَمْوَاتًا بَلْ أَحْيَاءٌ عِنْدَ رَبِّهِمْ يُرْزَقُونَ}‏‏.‏
 
Pamene anaphedwa ‘Abdullāh Ibn ‘Amr Ibn Harām (bambo ake a iyeyu Jābir), Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adakumana nane ndipo adati: “O iwe Jābir! Ndichifukwa chiyani ndikukuona ngati wasweka mtima?” Ine ndidati: ‘O iwe Mtumiki wa Allāh (ﷺ)! Bambo anga aphedwa ku nkhondo ya Uhud ndipo asiya ana amasiye komanso ngongole.’ Iye adati: “Kodi ukufuna ndikuuze nkhani yosangalatsa yomwe bambo akowo akakumanirana nayo ndi Allāh?” Ine ndidati: ‘Inde, O iwe Mtumiki wa Allāh (ﷺ)!’ Iye adati: “Allāh sadayankhulanepo ndi aliyense kupatula kudzera mu chotchinga, koma wayankhula ndi bambo ako maso ndi maso ndipo amawayankhula kuti: ‘O iwe kapolo Wanga! Takhumba china chake kwa Ine ndipo ndikupatsa.’ Iwo adati: ‘O Mbuye wanga! Ndibwenzeretseninso ndi moyo kuti ndikaphedwe kachiwiri.’ Allāh adayankha kuti: ‘Ndinakhazikitsa kale kuti iwowo sadzabwereranso (ku umoyo pambuyo pa imfa – Sūrah 21:91)’ Iwo adati: ‘O Mbuye wanga! Kawafotokozereni izi kwa amene ndawasiya m’mbuyomu.’ Choncho Allāh adavumbulutsa āyah iyi: “Ndipo musayese kuti amene aphedwa mnjira ya Allāh amwalira. Sichoncho! Iwowo ali moyo ndi Mbuye wawo ndipo akupatsidwa ma rizq (Sūrah 3:169).””
 
Kukhala moyo kukunenedwa mu āyah imeneyi sizikusonyeza kuti omwalirawo amamva ma du’ā a anthu a moyo. Akuyankhula Masrūq kuti:[5]
 
عَنْ عَبْدِ اللَّهِ بْنِ مَسْعُودٍ، أَنَّهُ سُئِلَ عَنْ قَوْلِهِ‏:‏ ‏(‏وَلَاَ تَحْسَبَنَّ الَّذِينَ قُتِلُوا فِي سَبِيلِ اللَّهِ أَمْوَاتًا بَلْ أَحْيَاءٌ عِنْدَ رَبِّهِمْ يُرْزَقُونَ‏)‏ فَقَالَ أَمَا إِنَّا قَدْ سَأَلْنَا عَنْ ذَلِكَ فَأُخْبِرْنَا أَنَّ أَرْوَاحَهُمْ فِي طَيْرٍ خُضْرٍ تَسْرَحُ فِي الْجَنَّةِ حَيْثُ شَاءَتْ وَتَأْوِي إِلَى قَنَادِيلَ مُعَلَّقَةٍ بِالْعَرْشِ.
 
Adafunsidwa ‘Abdullāh Ibn Mas’ūd zokhudza āyah yoti: {Ndipo musayese kuti amene aphedwa mnjira ya Allāh amwalira. Sichoncho! Iwowo ali moyo ndi Mbuye wawo ndipo akupatsidwa ma rizq – Sūrah 3:169}. Iye adati: “Tikakhala ife (ma Swahābah), tidafunsanso izi (kwa Mtumiki wa Allāh (ﷺ)) ndipo adatifotokozera kuti mizimu yawo (ya anthu ofera mnjira ya Allāh) imakhala mu mbalame zobiriwira ndipo imazungulira ku Jannah momwe yafunira, kenako imabwerera ku nyali zomwe zazendewera ‘Arsh.”
 
Mu buku la Kashfu Shubhāt As-Sūfiyyah, tipezamo mawu oti:[6]
 
أن قول الرسول صلى الله عليه وآله وسلم: «أرواحهم في جوف طير» ‌يَدُلُّ ‌عَلَى ‌أَنَّهَا ليست في الْأَجْسَادِ ‌الْمَدْفُونَةِ فِي الأرض.
 
Tsopano mawu a Mtumiki wa Allāh (ﷺ) oti: “Mizimu yawo (ya anthu ofera mnjira ya Allāh) imakhala mu mbalame,” akutiunikira kuti iyoyo siili mu matupi a omwe ali m’manda pano pa dziko.
 
Ndipo mu buku lomweli zikufotokozedwa kuti:[7]
 
‌‌)هل الأموات يسمعون؟( الراجح في هذه المسألة هو أن الأصل في الأموات أنهم لا يسمعون ‌إلَّا ‌مَا ‌وَرَدَ ‌الدَّلِيلُ ‌بِخُصُوصِهِ.
 
(Kodi akufa amamva?) Zomwe zili zolondola pa nkhani imeneyi ndi zakuti phata pa zokhudza anthu akufa ndi lakuti iwowo samamva (zomwe a moyo akuyankhula) kupatulapo pomwe pabwera umboni wopatulika.
 
Monga hadīth ya ‘Abdullāh Ibn ‘Umar yemwe akufotokoza kuti:[8]
 
اطَّلَعَ النَّبِيُّ صلى الله عليه وسلم عَلَى أَهْلِ الْقَلِيبِ فَقَالَ: وَجَدْتُمْ مَا وَعَدَ رَبُّكُمْ حَقًّا؟‏ فَقِيلَ لَهُ: تَدْعُو أَمْوَاتًا؟ فَقَالَ:‏ مَا أَنْتُمْ بِأَسْمَعَ مِنْهُمْ وَلَكِنْ لاَ يُجِيبُونَ.‏
 
Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adayang’ana Ahlul Qalīb (ma Mushrikūn amene adaphedwa pa nkhondo ya Badr ndipo adaponyedwa mu chitsime cha Al-Qalīb) ndipo adati: “Kodi mwazipeza zomwe adakulonjezani Mbuye wanu kuti ndi zoona?” Choncho anthu adayankhula kwa iye: “Kodi ukuyankhula kwa anthu akufa?” Iye adati: “Inuyo simungamve bwino kuposa iwowo, koma iwowo sangayankhe.”
 
Pa chifukwa ichi, sizoyenera kuwatenga anthu omwalira kukhala mikhalapakati yathu kwa Allāh. Ndipo sitikuyenera kuwalemekeza manda awo mu njira yopyola malire monga kumangapo mzikiti kapena nyumba. Ndipo sitikuyenera kumapita ku manda kwawo ndi cholinga chofunako madalitso. Izizi Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adaletsa.
 
Jundub Ibn ‘Abdullāh akufotokoza kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[9]
 
أَلَا ‌وَإِنَّ ‌مَنْ ‌كَانَ ‌قَبْلَكُمْ ‌كَانُوا ‌يَتَّخِذُونَ ‌قُبُورَ ‌أَنْبِيَائِهِمْ ‌وَصَالِحِيهِمْ ‌مَسَاجِدَ، أَلَا فَلَا تَتَّخِذُوا الْقُبُورَ مَسَاجِدَ! إِنِّي أَنْهَاكُمْ عَنْ ذَلِكَ.
 
Zindikirani, ndithudi amene anabwera m’mbuyo mwanu ankatenga manda a atumiki awo komanso anthu olungama mwa iwowo kukhala mizikiti; choncho musawatenge manda kukhala mizikiti. Ndakuletsani zimenezo.
 
‘Ā’ishah akufotokoza kuti:[10]
 
أَنَّ أُمَّ حَبِيبَةَ وَأُمَّ سَلَمَةَ ذَكَرَتَا كَنِيسَةً رَأَيْنَهَا بِالْحَبَشَةِ فِيهَا تَصَاوِيرُ، فَذَكَرَتَا لِلنَّبِيِّ صلى الله عليه وسلم، فَقَالَ: إِنَّ أُولَئِكَ إِذَا ‌كَانَ ‌فِيهِمُ ‌الرَّجُلُ ‌الصَّالِحُ ‌فَمَاتَ، ‌بَنَوْا ‌عَلَى قَبْرِهِ مَسْجِدًا، وَصَوَّرُوا فِيهِ تِلْكَ الصُّوَرَ، فَأُولَئِكَ شِرَارُ الْخَلْقِ عِنْدَ اللهِ يَوْمَ الْقِيَامَةِ.
 
Umm Habībah pamodzi ndi Umm Salamah adatchula za tchalitchi chomwe adachiona ku Habash (Abyssinia – Ethiopia) chomwe chidali ndi zithunzi mkati mwake. Choncho adakafotokoza izi kwa Mtumiki wa Allāh (ﷺ) yemwe adati: “Ndithudi amenewo, amati akamwalira mwa iwowo munthu wolungama, amamanga pa manda pake mzikiti ndipo amajambula zithunzi zimenezi mkatimo (mwa mzikitiwo). Amenewotu adzakhala oipitsitsa kwa Allāh pa Tsiku la Chiweruzo.”
 
Ibn ‘Abdul-Barr adatambasula motere zokhudza hadīth imeneyi:[11]
 
وَكَانَ رَسُولُ اللَّهِ صلى الله عليه وسلم ‌يُحَذِّرُ ‌أَصْحَابَهُ ‌وَسَائِرَ ‌أُمَّتِهِ مِنْ سُوءِ صَنِيعِ الْأُمَمِ قَبْلَهُ الَّذِينَ صَلَّوْا إِلَى قُبُورِ أَنْبِيَائِهِمْ وَاتَّخَذُوهَا قِبْلَةً وَمَسْجِدًا كَمَا صَنَعَتِ الْوَثَنِيَّةُ بِالْأَوْثَانِ الَّتِي كَانُوا يَسْجُدُونَ إِلَيْهَا وَيُعَظِّمُونَهَا وَذَلِكَ الشِّرْكُ الْأَكْبَرُ؛ فَكَانَ النَّبِيُّ صلى الله عليه وسلم يُخْبِرُهُمْ بِمَا فِي ذَلِكَ مِنْ سُخْطِ اللَّهِ وَغَضَبِهِ وَأَنَّهُ مِمَّا لَا يَرْضَاهُ خَشْيَةً عَلَيْهِمُ امْتِثَالَ طُرُقِهِمْ.
 
Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adachenjeza ma Swahābah ake komanso Ummah wonse za ntchito yoipa ya mibadwo yomwe inabwera m’mbuyomu yomwe imapemphera pa manda a atumiki awo ndi kuwapanga mandawo kukhala Qiblah komanso mizikiti; ngati momwe adachitiranso ma Mushrikūn pa mafano awo amene adali kuwagwadira ndi kuwalemekeza. Imeneyo idali Shirk yaikulu. Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adawauza kuti izi zimamunyasa Allāh, Iye amakwiya nazo, ndipo sasangalala nazo; amayankhula izi poopa kuti iwo (ma Swahābah pamodzi ndi asilamu onse) atha kuwatsatira anthu amenewa mnjira zawozi.
 
Mtumiki wa Allāh (ﷺ), kudzera mwa ‘Abdullāh Ibn Mas’ūd, adati:[12]
 
إِنَّ مِنْ شِرَارِ النَّاسِ مَنْ يَتَّخِذُ الْقُبُورَ مَسَاجِدَ.
Ndithudi, oipitsitsa mu gulu la anthu ndi awo amene atenga manda kukhala mizikiti.
 
Anas Ibn Mālik akufotokoza kuti:[13]
 
أَنَّ النَّبِيَّ صَلَّى اللَّهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ نَهَى أَنْ يُصَلَّى بَيْنَ الْقُبُورِ.
 
Ndithudi Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adaletsa kupempherera ku manda.
 
Popereka malangizo kwa Ibn ‘Abbās, Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[14]
 
يَا غُلَامُ احْفَظِ اللَّهَ يَحْفَظْكَ، احْفَظِ اللَّهَ تَجِدْهُ تُجَاهَكَ؛ وَإِذَا سَأَلْتَ فَاسْأَلِ اللَّهَ؛ وَإِذَا اسْتَعَنْتَ فَاسْتَعِنْ بِاللَّهِ.
 
Eh iwe mnyamata! Musunge Allāh (udzimukumbukira nthawi zonse) ndipo Iye adzakusunganso. Musunge Allāh, udzamupeza ali patsogolo pako (akukuchitira zambiri). Ndipo pamene wafuna kupempha, mupemphe Allāh. Ndipo ukafuna thandizo, funa kudzera mwa Allāh.
 
Kwa msilamu wokhulupiriradi mwa Allāh komanso mwa Mtumiki Wake (ﷺ); izizi zidzamukwanira ndipo sadzapempha mizimu komanso kupita kwa omwe ali m’manda ndi kumakapempha thandizo lililonse.
 
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.


[1] Musnad Ahmad, #12683; Musnad Ash-Shāmiyyīn, #1544; Al-Mu’jamal Awsatw, Vol. 1, tsamba 53, hadīth #148 (Shaykh Al-Albānī adaitcha hadīth imeneyi kuti ndi yofooka mu Silsilat Al-Ahādīth Adh-Dhwa’īfah, ‌‌#863)


[2] Adh-Dhwu’afā’ul Kabīr, Vol. 4, tsamba 211, hadīth #1798


[3] Al-Adab Al-Mufrad, #36 (hadīth ya hasan)


[4] Sunan Ibn Mājah, #190 (hadīth ya hasan swahīh)


[5] Swahīh Muslim, #1887; Sunan at-Tirmidhī, #3011, #3283


[6] Kashfu shubhāt As-Sūfiyyah, tsamba 64


[7] Kashfu shubhāt As-Sūfiyyah, tsamba 64


[8] Swahīh Al-Bukhārī, 1370


[9] Swahīh Muslim, #532


[10] Swahīh Al-Bukhārī, #427; Muslim, #528


[11] At-Tamhīd, Vol. 5, tsamba 45


[12] Musnad Ahmad, #4132


[13] Swahīh Ibn Hibbān, #1698


[14] Musnad Ahmad, #2669; Sunan At-Tirmidhī, #2516