Kutsatira ma Swahaabah ndi kofunikira bwanji?
Lero ndi: Friday, Shawwal 5, 1446 7:07 AM | Omwe awerengapo: 284
Ndimafuna kudziwa kuti kodi ma Swahaabah ndi ofunikira bwanji mu chipembedzomu? Nanga pali ena amene amanena kuti ma Swahaabah si ofunikira kuwatsatira chifukwa nawonso anali anthu ngati ife tomwe. Akuti iwowo analinso ndi kamvetsetsedwe kawo ka chipembedzochi malingana ndi nthawi yawoyo. Kodi izizi ndi zoona?
Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
Tikawaona ma Swahābah, iwo adali zitsanzo zabwino pambuyo pa Mtumiki (ﷺ). Allāh adawasankha kuti amutsate Mtumiki (ﷺ) kenako atenge chiphunzitso chake ndi kuphunzitsa mibadwo ya kutsogolo. Wina aliyense amene sangawatenge iwowa ngati anthu ofunikira, oyenera kutsatiridwa komanso kunyadiridwa; ameneyo ndi mdani wa Allāh.
Ma Swahābah adali anthu olimbikira pomutsatira Mtumiki (ﷺ) mu chikhulupiriro chake, mu ntchito ndi zoyankhula zake; komanso mu zilolezo ndi ziletso zimene adapereka.
Abū Mūsā Al-‘Ash’arī akufotokoza kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adayang’ana kumwamba ndipo adati:[1]
النُّجُومُ أَمَنَةٌ لِلسَّمَاءِ؛ فَإِذَا ذَهَبَتِ النُّجُومُ أَتَى السَّمَاءَ مَا تُوعَدُ. وَأَنَا أَمَنَةٌ لأَصْحَابِي فَإِذَا ذَهَبْتُ أَتَى أَصْحَابِي مَا يُوعَدُونَ. وَأَصْحَابِي أَمَنَةٌ لأُمَّتِي فَإِذَا ذَهَبَ أَصْحَابِي أَتَى أُمَّتِي مَا يُوعَدُونَ.
Nyenyezi ndi gawo la chitetezo cha kumwambaku. Zikapita nyenyezi, kumabwera kumwambaku zomwe zidalonjezedwa (kutanthauza mdima). Ndipo ine ndi chitetezo cha ma Swahābah anga; pamene ine ndapita (kumwalira), zidzabwera pa ma Swahābah anga zomwe adalonjezedwa. Ndipo ma Swahābah anga ndi chitetezo ku Ummah wanga; pamene ma Swahābah anga apita (amwalira onse), zidzabwera pa Ummah wanga zomwe zidalonjezedwa (mayesero ndi kusochera).
Al-Barbahārī adati:[2]
فقد بين رسول الله صلى الله عليه وسلم لأمته السنة وأوضحها لأصحابه وهم الجماعة، وَهُمُ السَّوَادُ الْأَعْظَمُ؛ والسواد الأعظم الحق وأهله. فمن خالف أصحاب رسول الله صلى الله عليه وسلم في شيء من أمر الدين فقد كفر.
Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adatambasula zokhudza Sunnah ku Ummah wake ndipo adaifotokoza momveka bwino kwa ma Swahābah ake. Iwowo ndi Jamā’ah. Iwowo ndi As-Sawād Al-A’dham ndipo As-Sawād Al-A’dham ndi chilungamo pamodzi ndi anthu ake (omwe akuwatsatira iwowo). Tsopano yemwe wasemphana ndi ma Swahābah a Mtumiki wa Allāh (ﷺ) mu chilichonse kuchokera mu zinthu za Chipembedzo, ameneyo wakanira.
Pa chifukwa ichi, ngati munthu akufuna kukhala woongoka mu kachitidwe kake ka chisilamu, atenge ndondomeko zimene ma Swahābah amagwiritsa ntchito. Ngati munthu satenga zimene Mtumiki (ﷺ) ndi ma Swahābah ake adatisiira, ameneyo ali mu gulu la osochera. ‘Abdullāh Ibn ‘Amr akufotokoza kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[3]
وَتَفْتَرِقُ أُمَّتِي عَلَى ثَلَاثٍ وَسَبْعِينَ مِلَّةً، كُلُّهُمْ فِي النَّارِ إِلَّا مِلَّةً وَاحِدَةً. قَالُوا: وَمَنْ هِيَ يَا رَسُولَ اللَّهِ؟ قَالَ: مَا أَنَا عَلَيْهِ الْيَوْمَ وَأَصْحَابِي.
“Ndipo Ummah wanga (wa asilamu) udzagawanikana mu magulu 73; magulu onse adzalowa ku Moto kupatula gulu limodzi.” Ma Swahābah adati: “Kodi gulu limodzilo nde ndi liti, eh iwe Mtumiki wa Allāh (ﷺ)?” Iye adati: “Amene adzakhale pa zimene ine ndi ma Swahābah anga tikugwiritsa ntchito lero lino (omwe adzatenge njira ya Mtumiki ﷺ pamodzi ndi ma Swahābah ake).”
Akuyankhula Ibn Mas’ūd kuti:[4]
أَنْتُمُ الْيَوْمَ أَكْثَرُ صَلاةً وَأَشَدُّ عِبَادَةً مِنْ أَصْحَابِ رَسُولِ اللَّهِ صَلَّى اللهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ وَكَانُوا خَيْرًا مِنْكُمْ، قِيلَ: لِمَ؟ قَالَ: كَانُوا أَزْهَدَ فِي الدُّنْيَا، وَأَرْغَبَ فِي الآخِرَةِ مِنْكُمْ.
“Inuyo lero lino mukuchulukitsa kupemphera komanso kuchita ma ‘ibādah ambiri kuposa ma Swahābah a Mtumiki wa Allāh (ﷺ); komatu iwowo adali anthu abwino kwambiri kuposa inu.” Zidafunsidwa kwa iye kuti: “Zili choncho chifukwa chani?” Iye adati: “Iwo adali kudzitalikitsa kwambiri ku za dziko lapansi, ndipo amakhumba kwambiri umoyo womwe uli nkudza kuposa inu.”
Mu kuyankhula kwina iye (Ibn Mas’ūd) adati:[5]
مَنْ كَانَ مُسْتَنًّا فَلْيَسْتَنَّ بِمَنْ قَدْ مَاتَ، أُولَئِكَ أَصْحَابُ مُحَمَّدٍ صَلَّى اللهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ، كَانُوا خَيْرَ هَذِهِ الأُمَّةِ، أَبَرَّهَا قُلُوبًا، وَأَعْمَقَهَا عِلْمًا، وَأَقَلَّهَا تَكَلُّفًا، قَوْمٌ اخْتَارَهُمُ اللَّهُ لِصُحْبَةِ نَبِيِّهِ صَلَّى اللهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ، وَنَقْلِ دِينِهِ، فَتَشَبَّهُوا بِأَخْلاقِهِمْ وَطَرَائِقِهِمْ، فَهُمْ كَانُوا عَلَى الْهَدْيِ الْمُسْتَقِيمِ.
Aliyense amene akufuna kutsatira chitsanzo, atsatire omwe adamwalira; amene ali ma Swahābah a Muhammad (ﷺ). Iwo adali anthu opambana kwambiri mu Ummah uno, adali ndi mitima yoyera, ozama kwambiri pa maphunziro, komanso osakakamula pochita zinthu. Iwowa adali anthu amene Allāh adawasankha kuti akhale otsatira a Mtumiki Wake (ﷺ), komanso kuti afalitse chipembedzo Chake; choncho atsatireni mu machitidwe awo ndi chikhalidwe chawo – chifukwa ndithu iwowo adali pa Njira Yoongoka.
Lero alipo ena mwa anthu amene amanyoza ma Swahābah, ndipo amadziona ngati ndi opambana kuposa iwo. Kufikira poti amawayang’anira pansi ma Swahābah a Mtumiki wa Allāh (ﷺ). Zindikirani kuti aliyense amene angawanyoze iwo, ameneyo ndi munthu wosochera yemwe Âqīdah yake ndi yosokonekera.
Abū Sa’īd Al-Khudrī akufotokoza kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[6]
لَا تَسُبُّوا أَصْحَابِي، فَوَالَّذِي نَفْسِي بِيَدِهِ، لَوْ أَنَّ أَحَدَكُمْ أَنْفَقَ مِثْلَ أُحُدٍ ذَهَبًا، مَا أَدْرَكَ مُدَّ أَحَدِهِمْ وَلَا نَصِيفَهُ.
Musawatukwane ma Swahābah anga; ndithudi ndikulumbira mwa Yemwe mzimu wanga uli m’manja Mwake; m’modzi wa inu atati apereke golide wochuluka ngati phiri la Uhud, sizingafanane ndi Mudd[7] yomwe adapereka m’modzi wa iwowo ndipo sizingayandikirenso (ku Mudd).
Adayankhula Ahmad Ibn Hanbal kuti:[8]
إذا رَأَيْتَ رَجُلاً يَذْكُرُ أَحَداً مِنْ أَصْحابِ رسولِ اللهِ صلى الله عليه وسلم بسُوْءٍ، فَاتَّهِمْهُ عَلىَ الإسلامِ.
Mukamuona munthu akukamba za m’modzi wa ma Swahābah a Mtumiki wa Allāh (ﷺ) moipa, kaikirani chisilamu chake.
Mukuyankhula kwina iye (Ahmad) adati:[9]
ومَنْ تَنَقَّصَ أَحَدًا من أَصْحابِ رَسُوْل اللَّه صلى الله عليه وسلم أَو أبغضَه لحَدَثٍ كَان مِنْهُ، أَوْ ذَكَرَ مَساوِيه، كانَ مُبْتَدِعًا، خارجًا عن الجَماعَةِ حَتَّى يَتَرَحَّمَ عَلَيْهِمْ جَمِيْعًا، ويَكُوْن قَلْبُهُ لَهُمْ سَلِيْمًا.
Aliyense amene angayankhule zosayenera zokhudza m’modzi wa ma Swahābah a Mtumiki wa Allāh ﷺ kapena kunyasidwa ndi chimene adachita m’modzi wa iwo (chomwe chili chabwino), kapena kumakamba zofooka zake (za m’modzi wa iwo); ameneyo ndi munthu woukira, watuluka mu Chilungamo mpaka atawakonda iwowo pamodzi; komanso mtima wake pa iwowo utagonjera.
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.
[1] Swahīh Muslim, #2531
[2] Sharh As-Sunnah, tsamba 37
[3] Jāmi’at Tirmidhī, #2641 (hadīth ya hasan); Al-Ibānah Al-Kubrā li Ibn Battwah, Vol. 1, tsamba 369, hadīth #265
[4] Sharh As-Sunnah lil Baghawiy, Vol. 14, tsamba 242-243
[5] Sharh As-Sunnah lil Baghawī, Vol. 1, tsamba 214
[6] Musnad Ahmad, #11516
[7] Mudd ndi 625g ya chinthu
[8] Manāqib Al-Imām Ahmad, tsamba 216
[9] Usūl As-Sunnah, tsamba 54, #29