Ndimafuna kudziwa ubwino wa Kupirira
Lero ndi: Friday, Shawwal 5, 1446 7:08 AM | Omwe awerengapo: 274
Ndifotokozereni ubwino wokhala munthu wopirira. Izi ndayankhula potengera ndi zomwe ndimakumana nazo mu umoyo wangawu.
Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
Allāh adaupanga umoyo wa padziko lapansi kukhala wa mayesero ochuluka. Ndipo aliyense amayesedwa malinga ndi chikhulupiriro chake.
Allāh adati:[1]
أَحَسِبَ النَّاسُ أَنْ يُتْرَكُوٓا أَنْ يَقُوْلُوٓا ءَامَنَّا وَهُمْ لَا يُفْتَنُوْنَ.
Kodi akuganiza anthu kuti angosiidwa basi chifukwa choti ayankhula kuti; “Takhulupirira,” ndiye iwowo osayesedwa?
Mu kuyankhula kwina Allāh adati:[2]
لَقَدْ خَلَقْنَا الْإِنسٰنَ فِي كَبَدٍ.
Ndithudi, Tamulenga munthu mu mavuto.
Ndipo tikaonanso mu āyah ina, Allāh akutitsimikizira kuti:[3]
أَمْ حَسِبْتُمْ أَنْ تَدْخُلُوا الْجَنَّةَ وَلَمَّا يَأْتِكُمْ مَثَلُ الَّذِينَ خَلَوْا مِنْ قَبْلِكُمْ مَسَّتْهُمُ الْبَأْسَآءُ وَالضَّرَّآءُ وَزُلْزِلُوا حَتَّى يَقُولَ الرَّسُولُ وَالَّذِينَ آمَنُوا مَعَهُ مَتى نَصْرُ اللَّهِ أَلَآ إِنَّ نَصْرَ اللَّهِ قَرِيبٌ.
Kapena akuganiza kuti akalowa ku Jannah pamene zisanawafikire iwowo zofanana ndi zomwe zidawafikira omwe anadutsa m’mbuyo mwawo? Iwowotu anakhudzidwa ndi umphawi komanso mavuto ndipo adagwedezeka mpaka kufikira poti mtumiki (wawo) pamodzi ndi omwe adakhulupirira naye limodzi adati: “Kodi ndi liti limene chidzafike chithandizo cha Allāh?” Musakaikire, chithandizo cha Allāh chili pafupi.
Sa’d Ibn Abī Waqqāsw adati:[4]
قُلْتُ يَا رَسُولَ اللَّهِ أَىُّ النَّاسِ أَشَدُّ بَلاَءً قَالَ: الأَنْبِيَاءُ ثُمَّ الأَمْثَلُ فَالأَمْثَلُ فَيُبْتَلَى الرَّجُلُ عَلَى حَسَبِ دِينِهِ فَإِنْ كَانَ دِينُهُ صُلْبًا اشْتَدَّ بَلاَؤُهُ وَإِنْ كَانَ فِي دِينِهِ رِقَّةٌ ابْتُلِيَ عَلَى حَسَبِ دِينِهِ. فَمَا يَبْرَحُ الْبَلاَءُ بِالْعَبْدِ حَتَّى يَتْرُكَهُ يَمْشِي عَلَى الأَرْضِ مَا عَلَيْهِ خَطِيئَةٌ.
Ndidati: Eh iwe Mtumiki wa Allāh (ﷺ)! Kodi ndi anthu ati amene amayesedwa kwambiri? Iye adati: “Atumiki, kenako owatsatira awo, kenako owatsatira awo. Munthu amayesedwa malinga ndi kuchilimika kwake pa chipembedzo; ngati ali wochilimika kwambiri, mayesero ake amakhalanso okhwima; ndipo ngati ali wokhwefula pa chipembedzo chake, iye amayesedwa malinga ndi mmene alili mu chipembedzo chake. Kapolo adzakhala akuyesedwa kufikira kuti iye adzakhala akuyenda padziko wopanda machimo.”
‘Ā’ishah akufotokoza kuti Mtumiki wa Allāh ﷺ adati:[5]
يَا أَيُّهَا النَّاسُ أَيُّمَا أَحَدٍ مِنَ النَّاسِ - أَوْ مِنَ الْمُؤْمِنِينَ - أُصِيْبَ بِمُصِيْبَةٍ فَلْيَتَعَزَّ بِمُصِيْبَتِهِ بِي عَنِ الْمُصِيْبَةِ الَّتِي تُصِيْبُهُ بِغَيْرِي؛ فَإِنَّ أَحَدًا مِنْ أُمَّتِي لَنْ يُصَابَ بِمُصِيْبَةٍ بَعْدِي أَشَدَّ عَلَيْهِ مِنْ مُصِيْبَتِي.
Eh inu anthu! Aliyense mwa anthu – kapena mwa okhulupirira – amene lamugwera vuto, basi adzitonthoze pokumbukira masautso amene adandigwera ine omwe sanamugwerepo aliyense kupatulapo ine. Ndithudi, palibe kuchokera mu Ummah wanga amene adzagweredwe vuto lowawa kwambiri kuposa vuto limene lidandigwera ine.
Apa tikuona kuti munthu ngati ali wokhulupirira mwa choonadi, iye ayembekezere kuti apatsidwa mayesero ambiri. Ndipo mayesero amenewa cholinga chake ndi chimene Mtumiki wa Allāh (ﷺ) wachinena kumapeto kwa hadīth ya Sa’d kuti munthu amakhululukidwa machimo ake akapirira pa mayeserowo. Choncho, iye akamakumana ndi mavuto, adzitonthoze pokumbukira mavuto amene anakumana nawo Mtumiki wa Allāh ﷺ.
Mu hadīth imene adaifotokoza Abū Sa’īd Al-Khudrī pamodzi ndi Abī Hurayrah, Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[6]
مَا يُصِيْبُ الْمُسْلِمَ مِنْ نَصَبٍ وَلاَ وَصَبٍ وَلاَ هَمٍّ وَلاَ حُزْنٍ وَلاَ أَذًى وَلاَ غَمٍّ حَتَّى الشَّوْكَةِ يُشَاكُهَا، إِلاَّ كَفَّرَ اللَّهُ بِهَا مِنْ خَطَايَاهُ.
Palibe vuto limene limamugwera msilamu; kaya ndi kutopa, matenda, masautso, kudandaula, kuvulazidwa, kapena kulira; mpaka minga yomwe imamubaya mu nsewu, kupatula kuti Allāh amamukhululukira machimo ake pa chimenecho.
Akuyankhula Ka’b kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[7]
مَثَلُ الْمُؤْمِنِ كَالْخَامَةِ مِنَ الزَّرْعِ؛ تُفَيِّئُهَا الرِّيحُ مَرَّةً، وَتَعْدِلُهَا مَرَّةً. وَمَثَلُ الْمُنَافِقِ كَالأَرْزَةِ؛ لاَ تَزَالُ حَتَّى يَكُونَ انْجِعَافُهَا مَرَّةً وَاحِدَةً.
Chitsanzo cha wokhulupirira chili ngati mtengo wauwisi wofewa umene umapindidwa ndi mphepo nthawi zina ndipo nthawi zina umaongoka. Ndipo chitsanzo cha Munāfiq (mtema kuwiri) chili ngati mtengo wa paini umene sugwedezeka (ndi mphepo) kufikira poti umazulidwa wonse ndi mphepo pa kamodzi.
Choncho, kupirira kwa munthu wokhulupirira kumapangitsa kuti Allāh asangalale naye, ndipo amamulipira malipiro abwino. Ndichifukwa chake munthu amene wadzipha mwadala kaamba kosapirira adzalangidwa ndipo adzamanidwa Jannah.
Jundub Ibn ‘Abdullāh Al-Bajalī adafotokoza kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[8]
كَانَ بِرَجُلٍ جِرَاحٌ فَقَتَلَ نَفْسَهُ فَقَالَ اللَّهُ بَدَرَنِي عَبْدِي بِنَفْسِهِ حَرَّمْتُ عَلَيْهِ الْجَنَّةَ.
Padali mwamuna wina yemwe adavutika ndi mabala (omwe adawapeza ku nkhondo), choncho iye adadzipha yekha (chifukwa cha ululu wa mabalawo). Allāh adati: “Wafulumira kapolo Wanga kuchotsa mzimu wake, ndaipanga Jannah kukhala yoletsedwa kwa iye.”
Tizindikire kuti Allāh amalola choipa (sharr) kuti chichitike pa akapolo Ake m’magulu awiri: Sharr al-Mutwlaq komanso Sharr An-Nasbī.
Abul Fat-h Muhammad Ibn ‘Abdul-Karīm Ash-Shahristānī adati:[9]
وأما الشر المطلق، فهو شر لا خير فيه.
Tsopano Ash-Sharr Al-Mutwlaq ndi choipa chomwe mkati mwake mulibe chabwino chilichonse.
Sharrul Mutwlaq imawachitikira anthu osakhulupirira mwa Allāh. Pomwe Sharrun Nasbī ndi choipa chimene chimachitika kwa wokhulupirira ndi cholinga choti apeze chabwino kutsogolo kwakeko.
Taonani Abī Tamīmah akufotokoza kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[10]
إِنَّ الْمُسْلِمَ إِذَا مَرِضَ أَوْحَى الله عَزَّ وَجَلَّ إِلَى مَلَائِكَتَهِ فَيَقُولُ: يَا مَلَائِكَتِي أَنَا قَيَّدْتُ عَبْدِي بِقَيْدٍ مِنْ قُيُودِي؛ فَإِنْ قَبَضْتُهُ أَغْفِرُ لَهُ، وَإِنْ عَافَيْتُهُ فَجَسَدٌ مَغْفُورٌ لَهُ لَا ذَنْبَ لَهُ.
Ndithudi msilamu pamene wadwala, Allāh Wapamwambamwamba amayankhula kwa Angelo Ake kuti: “Eh inu Angelo Anga! Ndamusunga kapolo wanga (kuti asachite ntchito zina) kudzera mu Cholepheretsa changa (chomwe ndi nthendayo). Ndikamutenga (kumuchotsa mzimu wake) ndimukhululukira; ndipo ndikamupatsa thanzi (akachira) ndimukhululukiranso ngati kuti analibe tchimo lililonse.”
Mu nthawi yomwe mavuto amugwera wokhulupirira, Allāh adamulamula iye kuti adziyankhula mawu oti: “Ife tidachokera kwa Allāh, ndipo kwa Iye ndi kumene tidzabwerere.” Izi tikuzipeza mu kuyankhula kwa Umm Salamah, mkazi wa Mtumiki (ﷺ):[11]
أَنَّ رَسُولَ اللَّهِ صَلَّى اللَّهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ قَالَ: مَنْ أَصَابَتْهُ مُصِيبَةٌ فَقَالَ كَمَا أَمَرَ اللَّهُ (إِنَّا لِلَّهِ وَإِنَّا إِلَيْهِ رَاجِعُونَ) اللَّهُمَّ أْجُرْنِي فِي مُصِيبَتِي وَأَعْقِبْنِي خَيْرًا مِنْهَا. إِلَّا فَعَلَ اللَّهُ ذَلِكَ بِهِ. قَالَتْ أُمُّ سَلَمَةَ: فَلَمَّا تُوُفِّيَ أَبُو سَلَمَةَ قُلْتُ ذَلِكَ، ثُمَّ قُلْتُ: وَمَنْ خَيْرٌ مِنْ أَبِي سَلَمَةَ؟ فَأَعْقَبَهَا اللَّهُ رَسُولَهُ صَلَّى اللَّهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ فَتَزَوَّجَهَا.
Ndithudi Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati: “Yemwe mavuto amugwera ndipo wayankhula malinga ndi mmene adalamulira Allāh (ponena kuti: Ife tidachokera kwa Allāh, ndipo kwa Iye ndi kumene tidzabwerere) kenako namupempha Allāh kuti: Eh Inu Allāh! Ndilipireni mu masautso angawa, ndipo mundipatse chabwino kuposa icho pambuyo pake. Allāh adzamuchitira iyeyo chimenecho.” Kenako Umm Salamah adati: ‘Pamene adamwalira Abū Salamah ndidayankhula zimenezi kenako ndidati: Ndindaninso wabwino kuposa Abū Salamah?’ Allāh adamupatsa Umm Salamah Mtumiki Wake (ﷺ) ndipo iye (Mtumiki ﷺ) adamukwatira mkaziyu.
Kupirira ndi chinthu chopambana chimene munthu angapatsidwe pano pa dziko lapansi kuchokera kwa Allāh. Ndipo okhawo amene ali ndi chikhulupiriro cholondola ndi amene amapirira ndi kuyedzamira mwa Mbuye Wawo.
Pa chifukwa ichi, ma Salaf adali anthu opirira mpaka ena mwa akazi amawalangiza amuna awo kuti asapeze ndalama mu njira ya harām poopa Moto. Zinali zabwino kwa iwowo kumagona ndi njala ndipo adali opirira.
Adayankhula Ibn Qudāmah kuti:[12]
القناعة، وعلى هذا كان النساء فى السلف، كان الرجل إذا خرج من منزله يقوله له أهله: إيَّاكَ وَكَسْبَ الْحَرَامِ؛ فَإِنِّي أَصْبِرُ عَلَى الْجُوعِ، وَلَا أَصْبِرُ عَلَى النَّارِ.
Al-Qanā’ah (kukhala wakhutitsidwa): umo ndi momwe ankachitira akazi a ma Salaf: pamene mwamuna akutuluka mnyumba, iye amayankhulidwa ndi mkazi wake kuti: “Kapewe kupeza zinthu za harām. Chifukwa ife tikhonza kupirira ndi njala, koma sitingadzapirire ndi chilango cha Moto.”
Mudzapeza kuti ambiri mwa akazi masiku ano sali okhutitsidwa pa zimene amuna awo amawachitira. Zonsezi ndi kupanda Âqīdah Yolongosoka. Chifukwa amene ali ndi Âqīdah Yolongosoka, amakhala wokhutitsidwa ndipo amapirira pa zochepa zimene Allāh akumupatsa.
Abū Sa’īd Al-Khudrī adapereka uthenga kuchokera kwa Mtumiki wa Allāh (ﷺ) kuti:[13]
وَمَنْ يَتَصَبَّرْ يُصَبِّرْهُ اللَّهُ، وَمَا أُعْطِيَ أَحَدٌ عَطَاءً خَيْرًا وَأَوْسَعَ مِنَ الصَّبْرِ.
Aliyense amene angapirire, Allāh adzampanga kukhala wopirira; ndipo palibe chinthu chimene munthu angapatsidwe chabwino komanso chopambana kuposa kupirira.
Abū Ad-Dardā’ adati:[14]
ثَلاثَةٌ مِنَ الصَّبْرِ: لا تُحَدِّثْ بِمَعْصِيَتِكَ، وَلا بِوَجَعِكَ، وَلا تُزَكِّ نَفْسَكَ بلسانك.
Zinthu zitatu ndi zochokera mu kupirira: kuti munthu usakambe zokhudza machimo ako, kapena zokhudza mavuto ako, kapena kudziyeretsa mwini wako (pamaso pa anthu).
Allāh ndi Mwini kuzindikira.
[1] Sūrah Al-'Ankabūt 29:2
[2] Sūrah Al-Balad 90:4
[3] Sūrah Al-Baqarah 2:214
[4]Jāmi’at Tirmidhī, #2398; Sunan Ibn Mājah, #4023; Musnad Ahmad, #1555
[5] Sunan Ibn Mājah, #1599 (hadīth ya swahīh – Silsilat As-Swahīhah #1106)
[6] Swahīh Al-Bukhārī, #5641, #5642
[7] Swahīh Al-Bukhārī, #5643
[8] Swahīh Al-Bukhārī, #1363
[9] Al-Milal wa An-Nihal, Vol. 3, tsamba 40
[10] Al-Mu’jamal Kabīr li At-Twabarānī, #7701 (swahīh potengera Shaykh Al-Albānī – Silsilat As-Swahīhah #1611)
[11] Muwattwa’ Mālik, Vol. 1, tsamba 236, hadīth #42
[12] Mukhtaswar Minhāj Al-Qāswidīn, tsamba 81
[13] Swahīh al-Bukhārī, #1469
[14] Hilyatul Awliyā’, Vol. 1, tsamba 224 komanso Vol. 6, tsamba 389