Ndapeza mwamuna yemwe kwathu sakumufuna

Lero ndi: Thursday, Shawwal 4, 1446 11:36 AM | Omwe awerengapo: 359

Funso:

10 February, 2025

Makolo anga akuonetsa kuti sakusangalatsidwa ndi mwamuna amene ndidapeza pa chifukwa choti iyeyo ndi wosauka. Iwowo akufuna mwamuna woti adzandisamale ndipo uyuyu chifukwa cha umphawi wake, iwo akuti sadzakwanitsa kundisamala. Kodi pamenepa ndikuyenera kuwamvera?

Yankho:

Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
 
Choyamba:
 
Malingana ndi Sharii'ah, ngati mkazi akufuna mwamuna, iye akuyenera kudutsira mwa omwe akumuyang'anira monga bambo ake, achimwene awo a bambo ake, mchimwene wake, agogo ake akuchimuna, ndipo ngati mkaziyu adali woti adakwatiwapo ndipo ukwati udatha kapena mwamunayo adamwalira, iye atha kumuuza mwana wake wamwamuna kuti amuyang'anire mwamuna wina malingana ndi zimene mayiwo angafotokoze zoti zipezeke mwa mwamunayo. Kapenanso ngati alipo achibale oyandikira kwambiri kwa mkaziyu ochokera kuchimuna akuyenera kukhala patsogolo poyendetsa nkhani ya ukwati komanso kufufuza mwamuna amene mkaziyo akumufuna.
 
Mu chisilamu, mwamuna amene ali wakhalidwe labwino komanso wotsatira zimene chipembedzo cha Chisilamu chikumuuza, ameneyo ndiye mwamuna woyenera kukwatiwana naye. Ngati makolo anuwo akukukanizani kuti musakwatiwane ndi mwamuna yemwe inu mwauzidwa kuti ndi wakhalidwe labwino komanso wodziwa bwino chipembedzo chake ngakhale ali mphawi, iwowo akukulakwirani kwambiri chifukwa choti, Allāh adatilangiza mu Sūrah 2:221 kuti:
 
وَلَعَبْدٌ مُّؤْمِنٌ خَيْرٌ مِّن مُّشْرِكٍ وَلَوْ أَعْجَبَكُمْ
 
''Kapolo yemwe ali wokhulupirira ali wabwino kwambiri kusiyana ndi mfulu wopembedza mafano, ngakhale kuti atakusangalatsani kwambiri.''
 
Tikaona mu hadīth ya Sahl imene adaisunga Al-Bukhārī mu Swahiih yake (buku 67, hadīth 29) timva kuti:
 
مَرَّ رَجُلٌ عَلَى رَسُولِ اللَّهِ صلى الله عليه وسلم فَقَالَ: مَا تَقُولُونَ فِي هَذَا.؟ قَالُوا: حَرِيٌّ إِنْ خَطَبَ أَنْ يُنْكَحَ، وَإِنْ شَفَعَ أَنْ يُشَفَّعَ، وَإِنْ قَالَ أَنْ يُسْتَمَعَ‏.‏ قَالَ: ثُمَّ سَكَتَ فَمَرَّ رَجُلٌ مِنَ فُقَرَاءِ الْمُسْلِمِينَ، فَقَالَ:‏ مَا تَقُولُونَ فِي هَذَا؟‏ قَالُوا: حَرِيٌّ إِنْ خَطَبَ أَنْ لاَ يُنْكَحَ وَإِنْ شَفَعَ أَنْ لاَ يُشَفَّعَ، وَإِنْ قَالَ أَنْ لاَ يُسْتَمَعَ‏.‏ فَقَالَ رَسُولُ اللَّهِ صلى الله عليه وسلم:‏ هَذَا خَيْرٌ مِنْ مِلْءِ الأَرْضِ مِثْلَ هَذَا ‏"‏‏.‏
 
Mwamuna wina anadutsa pamene Mtumiki wa Allāh (ﷺ) ndi ma Swahābah ake adakhala ndipo Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adafunsa nati: ''Mukuganiza bwanji za munthu uyu?'' Iwo adati: ''Ngati angafune kukwatira mkazi, iye atha kupatsidwa (mosavuta); ndipo atati amuikire kumbuyo munthu wina, anthu atha kumuvomera; ndipo atati ayankhule, aliyense atha kumumvera.'' Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adakhala chete, kenako mwamuna wina wochokera mu gulu la asilamu osauka anadutsa. Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adawafunsa ma Swahābah ake kuti: ''Mukuganiza bwanji za munthu uyu?'' Iwo adati: ''Atati apemphe banja kwa mkazi, iyeyu sakuyenera kupatsidwa mkaziyo; ndipo atati amuikire kumbuyo munthu wina, anthu sakuyenera kuvomereza; komanso atati ayankhule, anthu sakuyenera kumumvera.'' Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati: ''Munthu ameneyu ndi wabwino kuposa omwe adzadzitsa dziko lapansi ochokera mu munthu woyambirira uja.''
 
Apa tikuona kuti mwamuna yemwe makolo anuwo akumukana ndi munthu amene wanenedwa kuti ndi wabwino. Ndipo mu hadīth ina imene adaisunganso Al-Bukhārī mu Swahīh yake (buku 64, hadīth 65), akufotokoza Al-Miswar bin Makhramah kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:
 
فَأَبْشِرُوا وَأَمِّلُوا مَا يَسُرُّكُمْ، فَوَاللَّهِ مَا الْفَقْرَ أَخْشَى عَلَيْكُمْ، وَلَكِنِّي أَخْشَى أَنْ تُبْسَطَ عَلَيْكُمُ الدُّنْيَا كَمَا بُسِطَتْ عَلَى مَنْ قَبْلَكُمْ، فَتَنَافَسُوهَا كَمَا تَنَافَسُوهَا، وَتُهْلِكَكُمْ كَمَا أَهْلَكَتْهُمْ‏‏.‏
 
“Basi khalani osangalala ndipo yembekezerani zomwe zingakusangalatseni inu (kuchokera kwa Allāh). Ndikulumbira mwa Allāh, sindikukuoperani inu kuti mudzakhala osauka, koma ndikukuoperani inu kuti chuma chapadziko chidzapatsidwa kwa inu ngati momwe chidaperekedwera kwa omwe adalipo m’mbuyo mwanu. Choncho, inu mudzayamba kupikisana pakati panu kuti muchipeze chumacho, ngati momwe adapikisirirana iwowo (am’mbuyowo), ndipo chidzakuonongani inu ngati m’mene chidawaonongera iwowo.”
 
Ili ndi chenjezo loti tisakhale tikuwakwatitsa ana athu aakazi kwa olemera pa chifukwa choti anthu atiseka ngati tingawakwatitse kwa osauka. Makolo ambiri lero lino akumafuna mwana wawo akwatitsidwe kwa mwamuna wochita bwino ngakhale kuti mwa iyeyo mulibe chipembedzo.
 
Chachiwiri:
 
Tikaona malangizo a Mtumiki wa Allāh (ﷺ) kwa Fātwimah Bint Qays (Muslim, buku 18, hadīth 60) mu nthawi yomwe adabwera kudzafunsa za amuna atatu (Mu’āwiyah, Abu Jahm ndi Usāmah Ibn Zayd) omwe ankafuna kuti amukwatire iyeyu, Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:
 
أَمَّا مُعَاوِيَةُ فَرَجُلٌ تَرِبٌ لاَ مَالَ لَهُ وَأَمَّا أَبُو جَهْمٍ فَرَجُلٌ ضَرَّابٌ لِلنِّسَاءِ وَلَكِنْ أُسَامَةُ بْنُ زَيْدٍ.‏ فَقَالَتْ بِيَدِهَا هَكَذَا أُسَامَةُ أُسَامَةُ فَقَالَ لَهَا رَسُولُ اللَّهِ صلى الله عليه وسلم:‏ طَاعَةُ اللَّهِ وَطَاعَةُ رَسُولِهِ خَيْرٌ لَكِ.‏ قَالَتْ فَتَزَوَّجْتُهُ فَاغْتَبَطْتُ.‏
 
“Tsopano tikakamba za Mu’āwiyah, iyeyu ndi mwamuna wosauka yemwe alibe chuma. Ndipo tikakamba za Abuu Jahn, iyeyu nde ndi mwamuna womenya akazi, koma Usāmah Ibn Zayd….” Fātwimah Bint Qays adaloza ndi chala chake (kusonyeza kusasangalatsidwa ndi kukwatiwa ndi) Usāmah. Koma Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati: “kukhala womvera Allāh komanso womvera Mtumiki Wake (ﷺ) ndi zabwino kwa iwe.“ Fātwimah Bint Qays adati: “Choncho ndidakwatiwana ndi Usāmah, ndipo anthu adayamba kundida (pachifukwa cha madalitso amene Allāh adapereka kwa ife).
 
Mu malangizo awa, Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adafuna kuwauza akazi kuti mwamunayo asakhale mphwawi ngati mmene adalili Mu’aawiyah. Choncho, mwamunayo akhale oti atha kumudyetsa mkaziyu, kumuveka komanso kumupatsa malo ogona. Choncho zili zokwanira kuti mwamuna akhale ndi chomupezetsa ndalama zothandizira banja lake kusiyana ndikuti akhale munthu wopemphetsa.
 
Ngati zomwe makolo anu akukuoperani pa mwamunayo ndi zakuti simudzatha kukhala munthu omuopa Allāh choti mwamunayo alibe chipembedzo komanso ndi wambiri ya nkhadza, iwowo amvereni. Zikhonza kukhala zokondweretsa kwa inu ngati mwamuna angakupezereni makolowo ndi wochita bwino, wodziwa chipembedzo, wosamenya mkazi komanso wakhalidwe labwino.
 
Mwamuna wabwino akhale wosamenya mkazi ngati Abū Jahm, komanso ndizabwino kuti akhale wolidziwa buku la Allāh (Qur’ān) komanso Sunnah ya Mtumiki Wake Muhammad (ﷺ). Ngati sangapezeke wodziwa Qur’ān ndi Sunnah, akhale woti atha kufunsa malangizo a chipembezo kwa omwe ali ndi maphunziro. Chifukwa nthawi zambiri, ngati mkazi ali wodziwa bwino chipembedzo ndipo mwamuna sali wodziwa bwino, amatha kumanyozera malangizo a chipembedzo amene mkaziyo akupereka.
 
Zili bwino kwa omuyang’anira mkaziyu kuti afune mwamuna amene ali ndi zomuyenereza zomwe zili mu Sharī’ah. Ndipo iwowa ayesetse kuti mwamunayo akapezeka, abwere naye kwa mkaziyu ngati wavomereza kuti adzaonedwe ndi mkaziyo komanso pa ma mahram ake, komanso mwamunayo adzamuone mkaziyo pamaso pa ma mahram ake. Sizili zoyenera kuwalola awiriwa kuchita chibwenzi chifukwa izi ndi haraam.
 
Chachikulu, ana aakazi akwatitsidwe kwa mwamuna osati ndalama. Tikati mwamuna tikunena mwamuna ngati Usaamah Ibn Zayd yemwe Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adamusankhira Fatwimah Bint Qays.
 
Allāh ndiye mwini kudzindikira.