Ndakhala pa chibwenzi kwa nthawi yaitali
Lero ndi: Thursday, Shawwal 4, 1446 11:35 AM | Omwe awerengapo: 522
Ndine mkazi wa zaka 27. Ndinagwa m’chikondi ndi mwamuna wina wodziwa bwino chisilamu. Koma sitinayambe takumanapo ndipo iyeyu adandifunsira pa lamya. Adandilonjeza kuti adzandikwatira ndipo adandipempha kuti ndimudikirire popeza pakadali pano ali mu nyengo yovutirapo kuti sangathe kunditenga kaye.....
Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
Choyambirira timupemphe Allāh kuti akuongoleleni ndi kukupatsani chisangalalo. Ndipo timupemphe Allāh kuti aonjezere atsikana ngati inu amene mwaima nji podzisunga pa chifukwa choopa Allāh osati anthu, ndipo simukudumpha malire amene Allāh adaika. Anthu ambiri lero lino akupyola malire potengera zikhalidwe kapena zipembedzo zomwe zilibe gawo pa chilamulo cha Allāh. Zikhalidwe zomati mwamuna ndi mkazi ayenera kukhala kaye pa chibwenzi ndi cholinga choti adziwane asanalowe m'banja. Ndipo anthu nkumaona kuti palibe vuto pa zoterezi. Choncho, amalumpha malire amene Allāh wawaika, ndipo Allāh amawayesa ndi mavuto omwe lero lino tikuwamva kapena kuwerenga angakhalenso kuwaona, omwe mkati mwake muli phunziro kwa msilamu aliyense komanso kwa munthu aliyense wanzeru.
Mukuyenera kudziwa kuti kukumana kulikonse kwa pakati pa anthu osiyana maliseche (mwamuna ndi mkazi) omwe pakati pawo ukwati uli wotheka ndi njira imodzi imene imadzetsa Fitnah (mayesero). Sharī'ah yadzadza ndi umboni omwe umasonyeza kuti ndi zofunikira kupewa kugwera mu misampha ya Shaytwān mu gawo limeneli. Pali hadīth imene 'Alī Ibn Abī Twālib akufotokoza kuti:[1]
وَلَوَى عُنُقَ الْفَضْلِ؛ فَقَالَ الْعَبَّاسُ: يَا رَسُولَ اللَّهِ! لِمَ لَوَيْتَ عُنُقَ ابْنِ عَمِّكَ؟ قَالَ: رَأَيْتُ شَابًّا وَشَابَّةً فَلَمْ آمَنِ الشَّيْطَانَ عَلَيْهِمَا.
''Ndipo iye (Mtumiki wa Allāh (ﷺ)) adatembenuza khosi la Al-Fadhwl Ibn 'Abbās. Choncho 'Abbās adati: ''Eh iwe Mtumiki wa Allāh (ﷺ)! Bwanji watembenuza khosi la mwana wa amalume ako?'' Iye adati: ''Ndidaona kuti mnyamata ndi msungwana sadali otetezedwa kwa Shaytwān.''
Kusonyeza kuti kuyang'ana kumene Al-Fadhwl amamuyang'ana mtsikana wachilendoku, komanso mtsikanayo kumuyang'ana Al-Fadhwl, panali kuthekera kwakukulu kumene kukadachititsa awiriwa kugwera mu msampha wa satana.
Choncho, munachita bwino kudula kulumikizana kwanu ndi mnyamatayu, ndipo tikukulangizani kuti musiye kutumizirananso ma text pa WhatsApp, chifukwa kucheza komwe mukuchitakonso ndi msampha wina umene ungakudzetsereni awirinu zoipa.
Koma izi sizikutanthauza kuti pali kulakwika kuti mwamuna kapena mkazi akonde chomwe mtima wake wasangalatsidwa malinga ndi m’menenso Allāh ndi Mtumiki Wake (ﷺ) walangizira. Ibnul Qayyim Al-Jawziyyah adati:[2]
ولهذا إذا حصلَ العِشْقُ بسببٍ غير محظورٍ؛ لم يُلَمْ عليه صاحبُه، كمن كان يعشقُ امرأتَه، أو جاريته.
“Pa chifukwa ichi, ngati chikondi chikudzadza mu mtima mwa munthu chomwe si cha harām, munthuyo sakuyenera kunenedwa kuti akulakwitsa, ngati m’mene mwamuna amakondera azikazi ake kapenanso kapolo wake wa mkazi…”
Shaykh Ibn Uthaymīn adati:[3]
قد يسمع إنسان عن امرأة بأنها ذات خلق فاضل وذات علم فيرغب أن يتزوجها، وكذلك هي تسمع عن هذا الرجل بأنه ذو خلق فاضل وعلم ودين فترغبه، لكن التواصل بين المتحابين على غير وجه شرعي هذا هو البلاء، وهو قطع الأعناق والظهور، فلا يحل في هذه الحال أن يتصل الرجل بالمرأة، والمرأة بالرجل، ويقول إنه يرغب في زواجها، بل ينبغي أن يخبر وليها أنه يريد زواجها، أو تخير هي وليها أنها تريد الزواج منه، كما فعل عمر رضي الله عنه حينما عرض ابنته حفصة على أبي بكر وعثمان رضي الله عنهما، وأما أن تقوم المرأة مباشرة بالاتصال بالرجل: فهذا محل فتنة.
Mwamuna atha kumva za khalidwe labwino la mkazi wina wake komanso maphunziro ake a mkaziyo atha kufuna kuti amukwatire. Kapena mkazi kumva za khalidwe la mwamuna wina wake komanso maphunziro ake ndi kulimbikira kwake pa chipembedzo, ndipo mkaziyo atha kufuna kuti akwatiwe ndi mwamunayi. Koma kukumana kwa awiriwa komwe kusali kololedwa pa chisilamu ndi kumene kuli ndi vuto, komwe kuli ndi zotsatira zolakwika. Mu njira yotereyi, sizoyenera kuti mwamuna ngati wasangalatsidwa ndi mbiri ya mkaziyu ndiye akumane naye kapena mkazi amene wasangalatsidwa ndi mbiri ya mwamunayu ndiye akumane naye, ndi cholinga choti amuuze kuti ndikukwatire. Koma kuti amuuze waliy (womuyang’anira) wake kuti akufuna kukwatira mkaziyo kapena mkaziyo akufuna kukwatiwa kwa mwamunayo… Chifukwa ngati angakumane awiriwa popanda ma mahram awo, izi ndi zomwe zimawagwetsera mu fitnah.
Chomwe mukuyenera kuchita ndi kumuuza mwamunayo kuti abwere adzakumane ndi waliy wanu kuti afunsire banja. Iyeyu asabwenzeretsedwe m’mbuyo ndi kusapeza bwino kwake kapena kutangwanika kwake (ngati pali pa sukulu ya ukachenjede) chifukwa akufunsira banja, ndipo kukhala malo amodzi pakati pa awirinu kutachedwetsedwe, pamenepo palibe vuto chifukwa nikāh yo ikhala kuti yachitika.
Vuto lomwe lilipo masiku ano ndi lakuti amuna akufuna atadzadzitsa nyumba yawo ndi katundu ndiye adzikatenga bwino mkazi. Mu nthawi yomwe iyeyu akudikira kuti nyumba idzadze ndi katundu amakhala akuchita chibwenzi ndi mtsikana ndipo awiriwa amakhala akuchimwa ngati akukumana ndi kumakhala mnyumbamo awiriwiri.
Kuchedwa kukwatira kumakhala koopsa pa inu ngati muli ndi chikondi pa mwamuna, kapena mwamuna kukhala ndi chikondi pa mkazi ndiye iyeyu osakwatira poopa umphawi. Zili bwino kuopa Allāh amene adzakupatseni malipiro pa kukwatirana kwanu ndipo iye Allāh ndi mwini kupereka zosowa zathu. Inuyo awirinu mukukula ndipo nyengo ya mwamunayu siikusintha. Awa ndi mayesero amene Allāh wakupatsani ndi cholinga chofuna kuona chikhulupiriro chanu pa Iye. Komanso mudziwe kuti ena mwa amuna amene akufunsirani banja kudzera mwa waliy wanu atha kukhala abwino kwa inu kuposa mwamuna amene mukumudikirayo. Ndipo Allāh atha kuikanso chikondi chambiri pakati pa inu kuposa chikondi chomwe chilipo pakati pa inu ndi mwamuna mukudikirirayo.
Allāh ndiye Mwini kudzindikira.
[1] Musnad Ahmad, Vol. 2, tsamba 6, hadīth #562; Sunan At-Tirmidhī, #885 (Shaykh Al-Albānī adaitcha kuti ndi ya hasan mu Swahīh At-Tirmidhī)
[2] Rawdhwatul Muhibbīn, tsamba 147
[3] Liqā’āt Bābul Maftūh, Vol. 26, Fatwa #13