Kutsirika munda kuti akuba asakubere zomwe walima.
Lero ndi: Friday, Shawwal 5, 1446 7:04 AM | Omwe awerengapo: 283
Ndinamva kuti kutsirika munda ndi koletsedwa. Koma nanga ndi njira iti imene msilamu angaitsatire kuti asaberedwe m'munda mwake makamaka nthawi ino ya njalayi?
Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
Choyambirira: ufiti, maula komanso matsenga pa chisilamu ndi kufr (kukanira). Aliyense amene wapita kwa asing’anga kukaombedza, kukachitako maula, kufuna mankhwala a banja, a mwayi, a malonda, otsirikira munda ndi zina zotero ameneyo wakanira mu zomwe Allāh adavumbulutsa kwa Mtumiki Wake ﷺ.
Abū Hurayrah adafotokoza kuti Mtumiki wa Allāh ﷺ adati:[1]
مَنْ أَتَى كَاهِنًا، أَوْ عَرَّافًا، فَصَدَّقَهُ بِمَا يَقُولُ، فَقَدْ كَفَرَ بِمَا أُنْزِلَ عَلَى مُحَمَّدٍ.
“Aliyense amene wapita kwa sing’anga kapena bimbi; ndipo wakhulupirira mu zimene wauzidwa (kapena kupatsidwa) kumeneko, ameneyo wakanira mu zomwe zidavumbulutsidwa kwa Muhammad (ﷺ).”
Choncho, sizili zoyenera kupita kwa asing’anga kukatengako mankhwala kapena thandizo lililonse.
Chachiwiri: inu ngati msilamu yedzamirani mwa Allāh, mukhale ndi taqwā mwa Iyeyo komanso mudzipempha chikhululuko pa machimo amene mumachita. Allāh walonjeza aliyense wa taqwā kuti adzamufewetsera ma Rizq poyankhula kuti:[2]
وَمَن يَتَّقِ ٱللَّهَ يَجْعَل لَّهُۥ مَخْرَجًا - وَيَرْزُقْهُ مِنْ حَيْثُ لَا يَحْتَسِبُۚ وَمَن يَتَوَكَّلْ عَلَى ٱللَّهِ فَهُوَ حَسْبُهُۥٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ بَٰلِغُ أَمْرِهِۦۚ قَدْ جَعَلَ ٱللَّهُ لِكُلِّ شَىْءٍ قَدْرًا.
Ndipo aliyense amene angakhale ndi taqwā mwa Allāh – Iye adzamupatsa njira yotulukira (masautso amene akudutsawo) – Ndipo adzamupatsa ma Rizq kuchokera ku m’mbali zimene samaziyembekezera. Ndipo amene wayedzamira mwa Allāh – basi ameneyo ali womukwanira (ku chilichonse). Ndithudi, Allāh adzakwaniritsa cholinga Chake. Ndithudi, Allāh adakhazikitsa pa chilichonse muyezo.
Tilibe chikhulupiriro china chopambana kuposa kudalira mwa Allāh kuti atiteteze ku zonse zomwe zili zoipa. Popeza Iyeyo ndi Wakutha kutichotsera mavuto onse ngati m’mene akuyankhulira:[3]
وَإِن يَمْسَسْكَ ٱللَّهُ بِضُرٍّ فَلَا كَاشِفَ لَهُۥٓ إِلَّا هُوَۖ وَإِن يَمْسَسْكَ بِخَيْرٍ فَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَىْءٍ قَدِيرٌ
Ndipo ngati Allāh wakupatsa mavuto, palibe amene angakuchotsere kupatulapo Iyeyo. Ndipo ngati Iye wakupatsa ubwino – basi Iye pa zonse (zomuyenera Iyeyo) ali Wakutha.
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.
[1] Musnad Ahmad, #9536
[2] Sūrah At-Twalāq 65:2-3
[3] Sūrah Al-An’ām 6:17