Ndikukanika kukwatira chifukwa ndilibe chuma
Lero ndi: Thursday, Shawwal 4, 1446 11:37 AM | Omwe awerengapo: 346
Ndine mnyamata wa zaka 25 ndipo ndamaliza kumene maphunziro anga a sukulu ya ukachenjede. Ndilibe zondikwaniritsa kuti nditha kusamala banja makamaka ana amene ndingadzakhale nawo mtsogolomu. Kodi ndi malangizo anji amene mungandipatse chifukwa ine ndi m’modzi mwa anyamata amene....
Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
Choyambirira:
Ukwati sichinakhalepo chinthu chotsekereza munthu kuti akwaniritse zokhumba zake, koma kuti ndi chinthu chomwe chimamuthandizanso iyeyo kuti zokhumba zake zija azikwaniritse. Shaytwān ndi amene amawanong’oneza anthu kuti asachite kaye nikāh asanakwaniritse zomwe iwowo akuziona kuti ndi zabwino ndipo m’malo mwake, iyeyu (Shaytwān) amawaitanira ku njira yoipa imene imawagwetsera ambiri mu uchimo. Mutha kuona kuti izi ndi zomwe zachuluka masiku ano pamene mwamuna akuchedwetsa ukwati, kapena makolo kuwaletsa ana awo kuti asakwatire kapena kukwatiwa asanamalize sukulu, kapena asanapeze ntchito; ndipo izi zabweretsa masautso pa achinyamata amene ngakhale achedwetsedwa choncho, zokhumba zawozo sizimakwaniritsidwabe.
Tikaona mu m’badwo woyamba wa chisilamu (ma Swahābah), tipeza kuti iwo adali patsogolo kuchita zinthu zabwino zowatalikitsa ku uchimo ndipo sankachedwetsa ukwati. Amautenganso ukwati kukhala njira imodzi yopezera ma rizq (zosowa zawo) kuchokera kwa Allāh.
Iwo adali kuwalimbikitsa amene anabwerera ku chisilamu pambuyo pa kumwalira kwa Mtumiki (ﷺ) kuti akwatire.
‘Abdullāh Ibn Mas’ūd adati:[1]
الْتَمِسُوا الْغِنَى فِي النِّكَاحِ.
“Funanifunani kulemera kudzera mu ukwati.”
Umar Ibnil Khattwāb adati:[1]
عَجَبِي مِمَّنْ لَا يَطْلُبُ الْغِنَى فِي النِّكَاحِ، وَقَدْ قَالَ اللَّهُ تَعَالَى: إِنْ يَكُونُوا فُقَراءَ يُغْنِهِمُ اللَّهُ مِنْ فَضْلِهِ.
Amandidabwitsa yemwe safunafuna kulemera kudzera mu ukwati, chikhalirecho Allāh adati: “Ngati ali osauka, Allāh adzawalemeretsa kudzera mu chuma Chake.”
Mu kuyankhula kwina, ‘Abdullāh Ibn Mas’ūd adati:[2]
لَوْ لَمْ يَبْقَ مِنْ أَجْلِي إِلاّ عَشَرَةُ أَيَّامٍ وَأَعْلَمُ أَنِّي أَمُوتُ فِي آخِرِهَا يَوْمًا وَلِي طَوْل النِّكَاحِ فِيهِنَّ لَتَزَوَّجْتُ مَخَافَةَ الْفِتْنَةِ.
“Nditati ndatsala ndi masiku khumi mu umoyo wanga, ndipo ndikudziwa kuti pamapeto pa masikuwa ndimwalira, ndipo ndinali ndi kuthekera kuti nditha kukwatira, ndikanakwatira poopa mayesero.”
Choncho, tikuwalangiza anyamata kuti akwatire ndipo asankhe akazi olungama amene sali osakadza ndipo sali ofuna zambiri kuchokera mwa mwamuna kumbali ya mahr ndi zina zotero.
Ndipo tikuwalangiza awo amene sangakwanitse kusunga mkazi kaamba kosowekera kuti amuope Allāh ndipo asachite za harām, kapena kutsatira zomwe zikuchitika mu gulu la zinthu za harām, kapena kukhudza zomwe zili zoletsedwa kwa iwowo (kukhudza mkazi yemwe sali mahram wawo). Adzithandize okha, kudzera mu chifuniro cha Allāh, mu njira imeneyi potsatira chiphunzitso cha Mtumiki wa Allāh (ﷺ) monga kusala, kuswali, kuchita ma du'ā pafupipafupi komanso kukhala limodzi ndi gulu la anthu olungama amene amalimbikitsana za kuopa Allāh. Adzitangwanitsenso ndi zinthu za phindu monga kusakasaka maphunziro a chisilamu, kuphunzira ndi kuloweza Qur'ān ndi ma ahādīth, komanso kuchita ntchito zotukula chisilamu. Ngati munthu adzitangwanitse ndi zinthu zokhudza kutsatira Allāh, iyeyu adzakhala osaganizira zinthu za harām.
Chachiwiri:
Malangizo athu kwa makolo komanso atsogoleri a m’madera onse mdziko muno ndi akuti, kumaliza maphunziro chisakhale chinthu chomuyenereza munthu kuti akwatire. Ndi liti limene ukwati unasanduka njira yomutsekerezera munthu ku maphunziro? Pomwe chilungamo chake ndi chakuti: ngati munthu wamvetsetsa bwino chipembedzo chake, iye amadziwa kuti ukwati ndi njira imodzi yomutetezera munthu amene akusakasaka maphunziro ku chimasomaso. Chifukwa ukwati umampangitsa munthu kukhala wosaganizira zambiri monga kukakumana ndi chibwenzi kapena kukaimbirana lamya ndi chibwenzi kapena kulephera kugona chifukwa choti akuganizira chibwenzi. Komanso pamwamba pa zonsezi, kukwatira ndi lamulo limene Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adalipereka pa anyamata kuti alikwaniritse ngati ali ndi kuthekera.
Taonani momwe Allāh akufotokozerera mu Qur’ān:[3]
وَأَنكِحُوا۟ الْأَيَامَىٰ مِنكُمْ وَالصَّالِحِينَ مِنْ عِبَادِكُمْ وَإِمَآئِكُمْۚ إِن يَكُونُوا۟ فُقَرَآءَ يُغْنِهِمُ اللَّهُ مِن فَضْلِهِۦۗ وَاللَّهُ وَاسِعٌ عَلِيمٌ.
Ndipo kwatitsani amene ali mbeta mwa inu (mwamuna wopanda mkazi kapena mkazi wopanda mwamuna), ndipo (kwatitsaninso) omwe ali olungama mwa akapolo ndi azakazi anu. Ngati ali osauka, Allāh adzawalemeretsa kuchokera mu Chuma Chake. Allāh ndi Wokwanira ku zofuna za zolengedwa Zake, Wodziwa (nyengo imene akapolo Ake ali).
Choncho, tisanyengeke ndi umoyo wa amene sali asilamu. Tisaope umphawi koma timuope Allāh amene ali Mwini chuma. Nzotheka mnyamata kukwatira mtsikana kenako onse ndi kumapita ku sukulu ndipo ndi kukhala ndi ana pambuyo pomaliza sukuluyo.
Ophunzira akuluakulu adavomereza kuti ngati munthu wamwamuna akukumana ndi mayesero kuchokera kwa mkazi ndipo akulephera kupirira, iyeyu akuyenera kumukwatira.
Ibn Qudāmah adati:[4]
والناسُ فى النِّكاحِ على ثلاثةِ أضْرُبٍ؛ منهم مَنْ يخافُ على نفْسِه الوُقوعَ فى مَحْظُورٍ إن تَرَكَ النكاحَ، فهذا يجبُ عليه النِّكاحُ فى قولِ عامَّةِ الفُقهاءِ؛ لأنَّه يَلْزَمُه إعْفافُ نفسِه، وصَوْنُها عن الحَرامِ، وطَرِيقُه النكاحُ.
Anthu pa nkhani ya nikāh ali mu zigawo zitatu: ena mwa iwo ndi uyo amene amadziopera kuti atha kugwera mu zinthu za harām ngati sangakwatire. Munthu uyu zili zokakamizidwa pa iye kuti akwatire potengera mfundo ya ma fuqahā’ ochuluka. Izi zili choncho chifukwa choti akuyenera kukhala wodzisungabe komanso wodziletsa ku zinthu za harām, ndipo njira ya zonsezi ndi kukwatira basi.
Ndi zotheka kuchititsa nikāh potengera Sharī'ah, ndipo walīmah nkudzachita mtsogolomo; chifukwa mu njira imeneyi, zikhala zololedwa kwa mnyamatayu ndi mkaziyu kukhala pa awiriwiri nkumacheza, kugonana kumene pogwiritsa ntchito kulera kosakhalitsa kapena kuseweretsana ngati sakufuna kukhala malo amodzi mu nthawi imene akusakasaka maphunziro awowo.
Ndipo ngati makolo a anawa akuwakaniza kuti akwatirane pa zifukwa za chikhalidwe kapena kuopera anthu, kenako anawa nkuchita chigololo pachifukwa choti alephera kudziletsa ndipo agwera mu msampha wa Shaytwān, makolowa nawonso amapeza nawo machimo pamaso pa Allāh chifukwa athandizira anawa kuchita za harām.
Mu kuyankhula kwawo ma Swahābah awiri Abū Sa’īd komanso Ibn ‘Abbās adati: Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adanena kuti:[5]
مَنْ وُلِدَ لَهُ وَلَدٌ فَلْيُحْسِنِ اسْمَهُ وَأَدَبَهُ فَإِذَا بَلَغَ فَلْيُزَوِّجْهُ فَإِنْ بَلَغَ وَلَمْ يُزَوِّجْهُ فَأَصَابَ إِثْمًا فَإِنَّمَا إِثْمُهُ عَلَى أَبِيهِ.
“Yemwe wabereka mwana, iyeyu amupatse dzina labwino komanso amukonze khalidwe lake (pomuphunzitsa chipembedzo). Ndipo mwanayu akatha msinkhu, amukwatitse. Koma ngati mwanayu watha msinkhu mpaka osamukwatitsa ndipo iyeyo wachita tchimo (chiwerewere), tchimo lakelo limagwera pa bambo ake.”
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.
[1] Tafsīr Al-Qurtwubiy, Vol. 12, tsamba 241; komanso Tafsīr Ibn Kathīr, Vol. 6, tsamba 51
[2] Al-Mawsū’al Fiqhiyyah Al-Kawniyyah, Vol. 41, tsamba 214
[3] Suurah An-Nuur 24:32
[4] Al-Mughnī, Vol. 9 tsamba 341
[5] Shu’bal Īmān, #8299; Mishkāt Al-Maswābīh, Vol 2, tsamba 939, hadīth 3138