Kupempha Chilolezo Kwa Mkazi Woyamba

Lero ndi: Thursday, Shawwal 4, 1446 11:35 AM | Omwe awerengapo: 345

Funso:

17 March, 2025

Kodi ndi zoyenera kuti mwamuna apemphe chilolezo kwa mkazi wake pamene akufuna kukwatira mkazi wachiwiri?

Yankho:

Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
 
Pamene mwamuna wafuna kukwatira mkazi wina, sizili mu Sharī’ah kuti iyeyu apemphe chilolezo kwa mkazi woyamba chifukwa kukwatira mkazi wina ndi ufulu wake mwamunayu. Ngakhale kuti zili choncho, nthawi zina zimakhala bwino kuti mwamuna amufotokozere mkazi wake kuti akukwatira mkazi wina ndipo achite izi mwa chikondi ndi cholinga choti achepetse ululu wa chilengedwe umene mkazi amamva ikakhala nkhani yotereyi.
 
Sizili zololedwa kuti mwamunayu ayambe kaye wachita chibwenzi ndi mkazi wachiwiriyo kenako amukwatire. Mwamuna atha kutomera mkaziyo ndi kukhala ka nyengo kamene iyeyo angakapereke kwa mkaziyo kuti adikirire asanamukwatire. Kapena atha kuyendetsa ndondomeko yonse ya nikāh mosachedwetsa.
 
Akazi ambiri achisilamu amaganiza kuti mwamuna wawo sangatenge mkazi wina pokhapokha iwowo apereke chilolezo. Ndipo amayankhula kuti ngati iwowo alibe vuto lililonse, sizili zololedwa pa mwamuna wawo kukwatira mkazi wina. Ili ndi gawo la kusazindikira kumene ali nako pa nkhani ya mitala. Nthawi zambiri amamuikira zikhomo mwamunayu kuti asakwatire mkazi wina ponena kuti: “Kodi ndi chiyani chimene ine ndilibe chomwe mkazi winayo ali nacho?”
 
Tikafufuza mu Sharī’ah, tipeza kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) amakwatira akazi popanda kupempha chilolezo kwa akazi ake enawa. Tikaona mu hadīth ya ‘Abdul-‘Azīz Ibn Swuhayb, iye akufotokoza kuti Anas Ibn Mālik adati:[1]
 
فَأَصَبْنَاهَا عَنْوَةً، فَجُمِعَ السَّبْىُ، فَجَاءَ دِحْيَةُ فَقَالَ يَا نَبِيَّ اللَّهِ، أَعْطِنِي جَارِيَةً مِنَ السَّبْىِ‏.‏ قَالَ: ‏"‏اذْهَبْ فَخُذْ جَارِيَةً."‏‏‏ فَأَخَذَ صَفِيَّةَ بِنْتَ حُيَىٍّ، فَجَاءَ رَجُلٌ إِلَى النَّبِيِّ ﷺ فَقَالَ: يَا نَبِيَّ اللَّهِ، أَعْطَيْتَ دِحْيَةَ صَفِيَّةَ بِنْتَ حُيَىٍّ سَيِّدَةَ قُرَيْظَةَ وَالنَّضِيرِ، لاَ تَصْلُحُ إِلاَّ لَكَ‏.‏ قَالَ: ‏"‏ادْعُوهُ بِهَا‏"‏‏.‏ فَجَاءَ بِهَا، فَلَمَّا نَظَرَ إِلَيْهَا النَّبِيُّ ﷺ قَالَ: ‏"‏خُذْ جَارِيَةً مِنَ السَّبْىِ غَيْرَهَا‏"‏‏.‏ قَالَ: فَأَعْتَقَهَا النَّبِيُّ ﷺ وَتَزَوَّجَهَا‏.
 
Tidagonjetsa (dera la Khaybar), ndipo katundu wopeza pa nkhondoyi anatoleredwa. Dihya anabwera ndipo adati: “Eh iwe Mtumiki wa Allāh (ﷺ)! Ndipatse mzakazi kuchokera mu gulu la akapolo agwidwawa.” Mtumiki (ﷺ) adati: “Pita kasankhe yemwe ukumufuna.” Choncho Dihya adasankha Swafiyyah bint Huyay. Kenako munthu wina anabwera kwa Mtumiki (ﷺ) ndi kunena kuti: “Eh iwe Mtumiki wa Allāh (ﷺ)! Wapereka Swafiyyah bint Huyay kwa Dihya pomwe iyeyu (Swafiyyah) ndi mfumukazi ya mitundu iwiri: Quraydhwah komanso An-Nadhwiir? Palibetu mwamuna amene angapindule naye mkaziyu kuposa iwe.” Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati: “Tamuuzeni Dihya abwere naye mkaziyo.” Choncho, Dihya anabwera naye mkazi uja ndipo Mtumiki (ﷺ) atamuona mkaziyo adati kwa Dihya: “Tenga kuchokera mwa azakaziwa amene ukumufuna kupatulako uyu (kuloza Swafiyyah).” Anas adaonjezera nati: “Kenako Mtumiki (ﷺ) adamuombola (kumupatsa ufulu) Swafiyyah ndipo adamukwatira (ali ku ulendo womwewu wa ku Khaybar).”
 
Mu hadīth imeneyi tiona kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) sadakafike mpaka ku Madīnah ndi cholinga choti akawafotokozere akazi ake kuti akufuna kukwatira Swafiyyah. Iye adamukwatira ali kutali ndi akazi ake ena. Pamene amafika ku Madiinah, adafika ndi mkazi wina ndipo adangowadzitsa akazi ake enawo zoti pabwera mkazi mnzawo. Komanso akazi a Mtumiki (ﷺ) samadabwa Mtumikiyo (ﷺ) akachita zimenezi chifukwa amadziwa kuti umenewo ndi ufulu wa mwamuna. Ndipo iwo amamufunsa Mtumikiyo (ﷺ) kuti mkazi amene wakwatira kumeneyo ali bwanji.
 
Mu kulongosola kwake Anas Ibn Mālik adati:[2]
 
بُنِيَ عَلَى النَّبِيِّ ﷺ بِزَيْنَبَ ابْنَةِ جَحْشٍ بِخُبْزٍ وَلَحْمٍ فَأُرْسِلْتُ عَلَى الطَّعَامِ دَاعِيًا فَيَجِيءُ قَوْمٌ فَيَأْكُلُونَ وَيَخْرُجُونَ، ثُمَّ يَجِيءُ قَوْمٌ فَيَأْكُلُونَ وَيَخْرُجُونَ، فَدَعَوْتُ حَتَّى مَا أَجِدُ أَحَدًا أَدْعُو فَقُلْتُ: يَا نَبِيَّ اللَّهِ! مَا أَجِدُ أَحَدًا أَدْعُوهُ؟ قَالَ: ارْفَعُوا طَعَامَكُمْ، وَبَقِيَ ثَلاَثَةُ رَهْطٍ يَتَحَدَّثُونَ فِي الْبَيْتِ. فَخَرَجَ النَّبِيُّ ﷺ فَانْطَلَقَ إِلَى حُجْرَةِ عَائِشَةَ، فَقَالَ: ‏"السَّلاَمُ عَلَيْكُمْ أَهْلَ الْبَيْتِ وَرَحْمَةُ اللَّهِ."‏‏ فَقَالَتْ: وَعَلَيْكَ السَّلاَمُ وَرَحْمَةُ اللَّهِ، كَيْفَ وَجَدْتَ أَهْلَكَ؟ بَارَكَ اللَّهُ لَكَ. فَتَقَرَّى حُجَرَ نِسَائِهِ كُلِّهِنَّ، يَقُولُ لَهُنَّ كَمَا يَقُولُ لِعَائِشَةَ، وَيَقُلْنَ لَهُ كَمَا قَالَتْ عَائِشَةُ‏.‏
 
Pa walīmah ya ukwati wa Mtumiki (ﷺ) ndi Zaynab bint Jahsh, panakonzedwa mkate ndi nyama. Ine ndidatumizidwa kuti ndidzikaitana anthu kuti abwere ku phwandoli, choncho anthu anayamba kubwera (m’magulu); iwo amadya kenako nkutuluka (mnyumbamo). Gulu lina limabweranso, nkudya kenako nkutuluka. Ndidakhalabe ndikuwaitanira anthu ku phwandoli kufikira poti sadapezekenso ena oti aitanidwe. Kenako ndidati, “Eh iwe Mtumiki wa Allāh (ﷺ)! Sindidapeze munthu woti ndimuitane.” Iye adati, “Tenga chakudya chotsalachi.” Mnyumbamo mudatsarira ka gulu ka anthu atatu omwe amacheza. Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adatuluka ndikupita ku nyumba ya ‘Ā`ishah ndipo kumeneko adati: “As-Salām ‘alaykum ahlal Bayt wa rahmatullāh!” ‘Ā`ishah adayankha nati: “Wa ‘alaykas salām wa rahmatullāh. Kodi mwamupeza bwanji mkazi wanu (ali motani mkazi wanu watsopanoyu)? Allāh akudalitse.” Adanyamukanso kupita ku nyumba za akazi ake enawo ndipo adawalonjera ngati momwe adachitira kwa ‘Ā`ishah, ndipo iwo adamulonjeranso ngati m’mene adayankhira ‘Ā`ishah.
 
Zikadati ndi ufulu wa mkazi kupereka chilolezo kwa mwamuna kuti akwatire mkazi wina, Mtumiki wa Allāh (ﷺ) sakadakwatira akaziwa mu njira imeneyi. Iye akadakhala woyambirira kupempha chilolezo kwa akazi ake enawo. Koma izi sizili mu Sharī’ah ndipo akazi asawavutitse amuna awo powauza kuti chifukwa chani mwakwatira mkazi wina osandiuza kaye ine.
 
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.


[1] Swahīh Al-Bukhārī, #371


[2] Swahīh Al-Bukhārī, #4793