Âqīdah Yolondola Imatipangitsa Kukonda Maphunziro

Lero ndi: Thursday, Shawwal 4, 1446 11:34 AM | Omwe awerengapo: 194

Funso:

25 March, 2025

Kodi ndi zoona kuti munthu ukuyenera kuphunzira kaye usanayambe kuchita zinthu mu chisilamumu? Izi ndafunsa chifukwa pali zinthu zina zimene munthu unalamulidwa ndi Allah kuti uzichite ikakwana nthawi yake, ndiye ngati wazichita pamenepo upeza nsambi ngakhale wachita mopanda maphunziro?

Yankho:

Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
 
Chifukwa choyamba mu zifukwa zimene timayenera kuphunzirira Âqīdah ndi kusakasaka maphunziro olondola okhudza chipembedzo chathu. Palibe amene amachita molondola ntchito zonse zomwe tinalamulidwa ndi Allāh komanso Mtumiki Wake (ﷺ) kupatulapo amene waphunzira.
 
Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adafotokoza kudzera mu hadīth ya Abū Hurayrah kuti:[1]
 
مَنْ سَلَكَ طَرِيقًا يَلْتَمِسُ فِيهِ عِلْمًا، سَهَّلَ اللَّهُ لَهُ بِهِ طَرِيقًا إِلَى الْجَنَّةِ.
 
Yemwe wadzisankhira njira yoti m’menemo adzifuniramo maphunziro (a chipembedzo), Allāh amamufewetsera iyeyu njira yokalowera ku Jannah.
 
Mu hadīth ya Abū Ad-Dardā’, Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[2]
 
مَنْ سَلَكَ طَرِيقًا يَطْلُبُ فِيهِ عِلْمًا سَلَكَ اللَّهُ بِهِ طَرِيقًا مِنْ طُرُقِ الْجَنَّةِ؛ وَإِنَّ الْمَلاَئِكَةَ لَتَضَعُ أَجْنِحَتَهَا رِضًا لِطَالِبِ الْعِلْمِ، وَإِنَّ الْعَالِمَ لَيَسْتَغْفِرُ لَهُ مَنْ فِي السَّمَوَاتِ وَمَنْ فِي الأَرْضِ وَالْحِيتَانُ فِي جَوْفِ الْمَاءِ. وَإِنَّ فَضْلَ الْعَالِمِ عَلَى الْعَابِدِ كَفَضْلِ الْقَمَرِ لَيْلَةَ الْبَدْرِ عَلَى سَائِرِ الْكَوَاكِبِ. وَإِنَّ الْعُلَمَاءَ وَرَثَةُ الأَنْبِيَاءِ، وَإِنَّ الأَنْبِيَاءَ لَمْ يُوَرِّثُوا دِينَارًا وَلاَ دِرْهَمًا؛ وَرَّثُوا الْعِلْمَ فَمَنْ أَخَذَهُ أَخَذَ بِحَظٍّ وَافِرٍ.
 
Yemwe wadzisankhira njira yoti m’menemo adzisakiramo maphunziro (a chipembedzo), Allāh amamufewetsera iyeyu njira kuchokera mu njira za ku Jannah. Ndipo angelo amatsitsa mapiko awo (amadzichepetsa) pomusangalalira yemwe akuphunzira. Ndipo wophunzira amapempheredwa chikhululuko ndi onse amene ali kumwamba ndi omwe ali pa dziko komanso ndi nsomba yomwe ili m’madzi. Ndipo kupambana kwa wophunzira ndi wopembedza (yemwe amachita ma ‘ibādāt ochuluka), zili ngati m’mene umapambanira mwezi mu usiku womwe ukuwala kwambiri poyerekeza ndi nyenyezi zonse. Ndipo ophunzira ndi amene amatenga udindo wa atumiki. Ndipo atumiki sadasiye udindo (woyang’anira) dīnār ndi dirham; koma iwo adasiya maphunziro. Choncho, amene wawatenga maphunziro, iyeyu watenga gawo lalikulu kwambiri.
 
Alī Ibn Abī Twālib adayankhula kuti:[3]
الْعِلْمُ خَيْرٌ مِنَ الْمَالِ؛ الْعِلْمُ يَحْرُسُك وَأَنْتَ تَحْرُسُ الْمَالَ. وَالْمَالُ تُنْقِصُهُ النَّفَقَةُ، وَالْعِلْمُ يَزْكُو بِالْإِنْفَاقِ.
 
Maphunziro ndi opambana kuposa chuma; chifukwa maphunziro amakuteteza (kuti usagwere mu zinthu zolakwika) pomwe iwe umachiteteza chuma (kuti chisabedwe kapena kuonongedwa). Ndipo chuma chimapunguka ukamachigwiritsira ntchito, pomwe maphunziro amamuyeretsa munthu akamawagwiritsira ntchito.
 
Imām Ash-Shāfi’ī adati:[4]
 
‌مَنْ ‌لَا ‌يُحِبُّ ‌الْعِلْمَ لَا خَيْرَ فِيهِ، فَلَا يَكُنْ بَيْنَكَ وَبَيْنَهُ مَعْرِفَةٌ وَلَا صَدَاقَةٌ. فَإِنَّهُ حَيَاةُ الْقُلُوبِ وَمِصْبَاحُ الْبَصَائِرِ.
 
Yemwe sakonda maphunziro, mwa iyeyo mulibe ubwino. Choncho, pasakhale pakati pako ndi iyeyo kudziwana kapena ubwenzi ulionse. Chifukwa maphunziro ndi moyo wa mitima komanso dangalira la kuona.
 
Koma awa si maphunziro ongoloweza chabe. Awa ndi maphunziro amene munthu umawagwiritsira ntchito pamene wawapeza.
 
Imāmul Muhaddithīn Muhammad Ibn Ismā’īl Al-Bukhārī adati:[5]
 
بَاب: ‌الْعِلْمُ ‌قَبْلَ ‌الْقَوْلِ ‌وَالْعَمَلِ.
 
Khomo (gawo la): Maphunziro (kukhala) patsogolo pa mawu ndi ntchito.
 
Izi zikutiunikira kuti yemwe akufuna kuti agwire ntchito inayake kapena kuyankhula mawu ena-ake; iyeyu ayambe kaye wasaka maphunziro ndi cholinga choti alondole mu ntchitoyo kapena mu zoyankhulazo.
 
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.


[1] Swahīh Muslim, #2699a; Sunan at-Tirmidhī, #2646


[2] Sunan Abī Dāwūd, #3641


[3] Hilyatul Awliyā, Vol. 1, tsamba 80; Adab Ad-Dunyā wa Ad-Dīn, tsamba 42


[4] Mughnī Al-Muhtāj, Vol. 1, tsamba 99


[5] Swahīh Al-Bukhārī, Vol. 1, tsamba 37