Tandifotokozereni zifukwa zomveka bwino pa nkhani ya mitala

Lero ndi: Saturday, Shawwal 27, 1446 11:07 AM | Omwe awerengapo: 215

Funso:

06 April, 2025

Ndimafuna kudziwa zifukwa zimene Sharii'ah idalolezera mwamuna kukwatira akazi mpaka anayi. Komanso chifukwa chimene ife akazi sitiloledwa kukwatiwa kwa amuna awiri nthawi imodzi.

Yankho:

Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
 
Sharī’ah inabwera ndi cholinga chofuna kusamala zofuna za unyinji wa okhulupirira onse osati za wokhulupirira m’modzi yekha, komanso kuteteza okhulupirira ku vuto lalikulu osati laling’ono.
 
Chitsanzo chabwino ndi nkhani imene Sharī’ah idavomereza kuti mwamuna atha kukwatira akazi angapo. Chisilamu chinabwera kuti chipereke malire pa kachulukidwe ka akazi amene mwamuna akuyenera kuwakwatira nthawi imodzi pachifukwa choti m’mbuyomo panalibe malire. Choncho, chisilamu chinaika malire a akazi anayi ndipo chidafotokoza zomwe mwamuna akuyenera kuchita pa ukwati woterewu.
 
Ngakhale kuti kugawana mwamuna chili chinthu chopweteka kwa akazi ambiri, kufunikira kwa ukwati woterewu (mitala) mu madera onse padziko pano kumaonekera pa zotsatira zimene zilipo chifukwa cha chiletso cha mitala chomwe maiko ochuluka anaika, kapena zikhalidwe zina zomwe zilipo pakati pa mitundu ya anthu ena kumbali yonyasidwa ndi mitala.
 
Pali zifukwa zambiri zimene Sharī’ah idalolezera mitala ndipo zina mwa izo ndi izi:
 
1. Mitala imaonjezera chiwerengero cha Ummah.
 
Zili zodziwika kuti Ummaah umaonjezekera kudzera mu ma anja achisilamu amene akubereka ana ochuluka. Ndipo ana ambiri akuyenera kupezedwa kudzera mwa mwamuna amene wakwatira akazi angapo kusiyana ndi amene wakwatira mkazi mmodzi.
 
Anthu ozindikira amadziwa kuti kuchuluka kwa ana achisilamu kumalimbitsa chisilamu ndipo chimakhala ndi anthu omwe adzachiteteze komanso kuchitukula. Siyani kutenga maganizo a anthu amene amati kuchuluka kwa anthu kumabweretsa chiopsezo pa zinthu zapadziko zomwe zili zosakwanira, popeza Allāh Mwini kuzindikira adapereka zokwanira pano pa dziko lapansi kwa akapolo ake ndipo sizingapunguke chifukwa cha mitala yomwe Iyeyo Allāh waichitanso kukhala yololedwa.
 
2. Chiwerengero chikuonetsa kuti akazi alipo ochuluka kuposa amuna ndipo chidzakhala chikukwerabe kufikira pamene hadīth ya Mtumiki wa Allāh (ﷺ) idzakwanire.
 
Anas Ibn Mālik akufotokoza kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[1]
 
مِنْ أَشْرَاطِ السَّاعَةِ أَنْ يَقِلَّ الْعِلْمُ، وَيَظْهَرَ الْجَهْلُ، وَيَظْهَرَ الزِّنَا، وَتَكْثُرَ النِّسَاءُ وَيَقِلَّ الرِّجَالُ، حَتَّى يَكُونَ لِخَمْسِينَ امْرَأَةً الْقَيِّمُ الْوَاحِدُ.
 
“Zina mwa zizindikiro za kuyandikira kwa Tsiku la Chiweruzo ndi monga: maphunziro achipembedzo adzachepa (kudzera mu kumwalira kwa ma ‘Ulamā); umbuli mu chipembedzo udzachuluka; chiwerewere chidzachitidwa poyera (anthu sadzaona vuto kuchita chigololo ndipo adzachivomereza); akazi adzachuluka kuposa amuna, mpaka padzafika poti mwamuna m’modzi adzasamalira akazi makumi asanu (50).”
 
Mu kuyankhula kwa Abū Mūsā, Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[2]
 
وَيُرَى الرَّجُلُ الْوَاحِدُ يَتْبَعُهُ أَرْبَعُونَ امْرَأَةً، يَلُذْنَ بِهِ مِنْ قِلَّةِ الرِّجَالِ وَكَثْرَةِ النِّسَاءِ. ‏
 
Ndipo udzaona mwamuna m’modzi akumutsatira akazi makumi anayi (40) kuti awayang’anire, chifukwa cha kuchepa kwa amuna komanso kuchuluka kwa akazi.
 
Mukaona ma ahādīth awiriwa, ayenda mu mndandanda wabwino: pachifukwa choti anthu ophunzira chipembedzo amene amachita zinthu chifukwa choopa Allāh amwalira, mbuli ndi zimene zimadzadza ndipo zimaikidwa patsogolo kuti ziziongolera anthu. Zotsatira zake ndi zakuti zina zomwe Allāh waloleza monga mitalayi anthu amati ilibe ntchito. Ndipo chiwerewere chimayamba kufalikira chifukwa choti akaziwo achuluka ndipo amuna akukanika kudziwa za ubwino wokwatira akazi angapo.
 
Choopsa ndi chakuti; chifukwa cha kuchuluka kwa akazi, komanso kufooka kwa amuna pofuna kutenga akazi angapo, komanso nsanje mwa akazi amene akwatiwa kale; mkazi uyu wopanda mwamunayu sadzakwatiwa, ndipo sadzakhala ndi mwamuna woti amuteteze ku zilakolako zake mu njira ya halāl. M’malo mwake adzakhala chida chomwe amuna ena adzidzathetserapo zilakolako zawo mwa harām. Ngati adzakhale ndi ana, anawa adzakula akusowekera chikondi cha bambo ndipo adzakula akuona ngati amuna ndi anthu oipa omwe amathawa udindo wawo.
 
Mukaonanso ana amene amabadwa mu njira ya chiwerewere nthawi zambiri amakhala osokonekera ngati sanaleredwe bwino. Akakula ndi kuzindikira kuti iwowo alibe bambo, amayamba kuonetsa khalidwe loipa ndipo amasochera. Amayambanso kuwada anthu amene sadawathandize iwowa kukulira mu banja loyenera. Amasanduka njira yomwe dziko limapitira pansi, atsogoleri a magulu azigawenga, ngati m’mene zilili maiko ena omwe satsata Sharī’ah.
 
3. Amuna amakhala pa chiopsezo chotaya miyoyo yawo kwambiri malinga ndi malo amene iwowo amagwira ntchito. Monga kukwera malo apamwamba, kulowa m’migodi, kuyenda nthawi yaitali pa nsewu, kukhala asilikali komanso apolisi amene amagona usiku kumateteza malo ofunikira ndi ntchito zina zimene sitingathe kuzitchula pazokhapazokha. Iyi ndi njira imozi imene ikuchepetsa chiwerengero cha amuna. Ndipo amuna amenewa amasiya akazi omwe akufunanso nawo chitetezo ku zilakolako zawo komanso chikondi ndi chisamaliro.
 
4. Pali amuna amene Allāh anawadalitsa ndi mphamvu zambiri moti iwowa sakwanira ndi mkazi m’modzi. Ngati khomo latsekedwa pa iwowa loti akhale ndi akazi opyola mmodzi, iwowa mphamvu zawo amakathetsera malo a haraam.
 
Kuphatikiza pamenepo, mkazi amakhala pa masiku ake mwezi ulionse (kapena pakutha pa miyezi iwiri ngakhale itatu malinga ndi m’mene alili akazi ena). Ndipo akabereka, amakhala masiku ochulukirapo asanakumane ndi mwamuna wake ku chipinda. Nthawi imeneyi mwamuna amakhala asakukhala naye malo amodzi mkazi wakeyu ndipo amuna ochepa ndi amene amapirira makamaka mkazi akabereka kumene.
 
5. Nthawi zina mkazi amakhala chumba (wosabereka), kapenanso sangathe kukwanitsa zina mwa zimene mwamuna akufuna, kapena atha mwamunayo osagonana naye mkaziyu chifukwa akudwala, kapena ngati mwamuna akufuna ana ambiri, mkaziyu atha osakwanitsa malingana ndi njira yomwe waberekera. Zili zachilungamo kuti mwamunayu akwatire mkazi wina ndipo mkazi woyambayu sakuyenera kutsutsa izi pokhapokha ngati ali wamufunira mwamunayo zoipa.
 
Izi ndi zina mwa zifukwa zimene Allāh walolezera amuna kukwatira akazi anayi.
 
Mtsutso wa akazi ena:
 
Chabwino amuna alolezedwa kukwatira akazi anayi ndipo zaletsedwa kwa akazi kukwatiwa kwa amuna odutsa mmodzi. Kodi uku si kuwapondereza akaziwo?
 
Yankho pa mtsutso umenewu:
 
Malinga ndi kufotokoza komwe tikukupeza mu Al-Mufasswal fī Ahkāmil Mar’ah, tipeza kuti:[3]
 
المرأة لا يفيدها أن تُعطى حق تعدد الأزواج ، بل يحطّ من قدرها وكرامتها، ويُضيع عليها نسب ولدها؛ لأنها مستودع تكوين النسل، وتكوينه لا يجوز أن يكون من مياه عدد من الرجال وإلا ضاع نسب الولد، وضاعت مسؤولية تربيته، وتفككت الأسرة، وانحلت روابط الأبوة مع الأولاد، وليس هذا بجائز في الإسلام، كما أنه ليس في مصلحة المرأة، ولا الولد ولا المجتمع .
 
Palibe chifukwa choti mkazi akwatiwe kwa amuna awiri, atatu kapena anayi. Izi zili choncho poteteza mkaziyo ku umunthu wake komanso mkaziyo sangathe kudziwa bwinobwino bambo weniweni wa mwana amene wabadwa pa chifukwa choti wagona ndi amuna awiri kapena atatu mu masiku oyandikana. Zoterezi sizololedwa pa Sharī’ah kuti ana asadziwe bambo awo enieni popeza aliyense mwa abambowo akukana kuti mwanayo sakufanana ndi iwowo kapena onsewo akukanganirana kuti mwanayo ndi wake. Izi zitha kuphwasula ma anjawa kudula ubale pakati pa bambo ndi ana ake, zomwe zili haraam pa Sharii’ah komanso zochititsa manyazi kwa mkaziyo ndi anawo pa mudzi.
 
Allāh ndiye Mwini kudzindikira.


[1] Swahīh Al-Bukhārī, #81


[2] Swahīh Al-Bukhārī, #1414


[3] Al-Mufasswal fī Ahkāmil Mar’ah, Vol. 6, tsamba 290