Kupangitsa nikaah kudzera pa phone
Lero ndi: Saturday, Shawwal 27, 1446 11:54 AM | Omwe awerengapo: 298
Pali mwamuna wina amene ali ku South Africa ndipo adakwatira mkazi yemwe amakhala kuno ku Malawi. Mwamunayu adamufunsa mkaziyo za waliy wake ndipo adayankha kuti alipo. Waliy wa mkaziyu adavomereza ndipo ukwatiwo adapangira pa lamya, ndipo mahr idabweretsedwa ndi mchemwali wake wa mwamunayu tsiku lomwelo. Nkhawa yomwe mwamunayu ali nayo ndi yakuti, iyeyu atawafunsa anthuwa ngati padali....
Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
Kuti nikāh itheke, pakuyenera kukhala zinthu zinayi: walī, kugwirizana nako komwe mwamuna wachita, kuvomereza komwe mkazi wachita, ndi mboni ziwiri. Umboni wa izi tikuupeza mu hadīth ya Ibn ‘Abbās:[1]
فَالنِّكَاحُ يَثْبُتُ بِأَرْبَعَةِ أَشْيَاءَ الْوَلِيُّ وَرِضَا الْمَنْكُوحَةِ وَرِضَا النَّاكِحِ وَشَاهِدَيْ عَدْلٍ.
“Tsopano nikāh imatheka kudzera mu zinthu zinayi izi: walī, kukondwera kwa wokwatibwa, kukondwera kwa wokwatira, komanso mboni ziwiri zachilungamo.”
Tikaona mu hadīth ya ‘Ā`ishah, Ibn ‘Abbās ndi ‘Imrān Ibn Huswayn, Mtumiki (ﷺ) akufotokoza kuti:[2]
لَا نِكَاحَ إلَّا بِوَلِيٍّ وَشَاهِدَيْ عَدْلٍ وَمَا كَانَ مِنْ نِكَاحٍ عَلَى غَيْرِ ذَلِكَ فَهُوَ بَاطِلٌ.
“Palibe nikāh ngati palibe walī komanso mboni ziwiri zachilungamo. Ndipo nikāh yomwe siikupezeka chimodzi mwa ziwirizi, imeneyo siyovomerezeka.”
Imām Ash-Shāfi’ī adati:[3]
فَإِنَّ أَكْثَرَ أَهْلِ الْعِلْمِ يَقُولُ الْفَرْقُ بَيْنَ النِّكَاحِ وَالسِّفَاحِ الشُّهُودُ.
Ndithudi ochuluka mu gulu la ma Ulamā (ophunzira akuluakulu a chisilamu) adati: “Kusiyana kwa An-Nikāh ndi As-Sifāh (chibwenzi) ndiye ndi kupezeka kwa mboniku.”
Mu kufotokoza kwake Ibn Qudāmah akuti:[4]
أنَّه لا يَنْعَقِدُ إلَّا بشَهادةِ مُسْلِمَيْنِ، سواءٌ كان الزَّوْجانِ مُسْلِمَيْنِ، أو الزَّوْجُ وَحْدَه.
Ukwati ukuyenera kuchitika pokhapokha ngati pali mboni ziwiri za chisilamu, kaya okwatiranawo onse ndi asilamu kapane mwamuna yekha ndi msilamu.
As-Sarkhasī akuyankhula kuti:[5]
النِّكَاحَ عَقْدٌ عَظِيمٌ خَطَرُهُ كَبِيرٌ، وَمَقَاصِدُهُ شَرِيفَةٌ وَلِهَذَا أَظْهَرَ الشَّرْعُ خَطَرَهُ بِاشْتِرَاطِ الشَّاهِدَيْنِ فِيهِ مِنْ بَيْنَ سَائِرِ الْمُعَاوَضَاتِ.
Nikāh ndi chinthu chofunikira kwambiri (mchisilamu), ndipo zolinga zake ndi zolungama. Choncho, chisilamu chimaphunzitsa kuti payenera kukhala mboni ziwiri kuti ukwatiwu utheke, kusiyana ndi migwirizano ina yonse.
Tikabwera mu Al-Mawsū’ah Al-Fiqhiyyah, tipeza mukutambasulidwa kuti:[6]
ذَهَبَ الْحَنَفِيَّةُ وَالْمَالِكِيَّةُ وَالشَّافِعِيَّةُ وَالْحَنَابِلَةُ إِلَى أَنَّهُ يُشْتَرَطُ فِي شَاهِدَيِ النِّكَاحِ التَّكْلِيفُ، أَيْ أَنْ يَكُونَ كُلٌّ مِنْهُمَا عَاقِلاً بَالِغًا، فَلَا تُقْبَل شَهَادَةُ مَجْنُونٍ بِالإِجْمَاعِ، وَلَا شَهَادَةُ صَبِيٍّ وَلِأَنَّهُمَا لَيْسَا مِنْ أَهْل الشَّهَادَةِ.
Gulu lochuluka kuchokera mu ophunzira a Hanafiyyah, Mālikiyyah, Shāfi’iyyah komanso Hanābilah lidapereka nyengo pa nkhani ya mboni za nikāh kuti zikhale zokwanira: kutanthauza kuti onse awiri ochitira umboniwa akhale oti si amisala komanso akhale otha msinkhu. Anthu asalandire umboni kuchokera kwa munthu wodziwika ndi misala, kapena mwana chifukwa iwowa sali mu gulu la anthu ochitira umboni (pa chili chonse mchisilamu).
Gulu lambiri la ma fuqahā' lidatsindika kuti mboni zikhale zazimuna ziwiri osati akazi, choncho ngati panali akazi okhaokha, ukwatiwu ndi wosavomerezeka. Koma gulu la Hanafiyyah limati m’malo mwa amuna awiri, nzotheka kukhalapo akazi anayi, chifukwa choti pa Sharī’ah, akazi awiri amatengedwa ngati mboni imodzi.
Ndipo gulunso lochuluka la ma fuqahā' likutsindika kuti mbonizo zipezeke pa nthawi imene ukwatiwo ukumangidwa osati utamangidwa kale.
Koma gulu lotsatira Imām Mālik lidati izi zilibe ntchito ngati mboni sizinapezeke mu nthawi yomangitsa ukwati, koma zikuyenera kupezeka mwamuna ndi mkaziyo asanatsekule banja (asanakhale malo amodzi).
Zikufotokozedwa kuti:[7]
أَنَّ أَصْلَ الْإِشْهَادِ عَلَى النِّكَاحِ وَاجِبٌ، وَإِحْضَارُهُمَا عِنْدَ الْعَقْدِ مَنْدُوبٌ. فَإِنْ حَصَلَ عِنْدَ الْعَقْدِ فَقَدْ وُجِدَ الْأَمْرَانِ الْوُجُوبُ وَالنَّدْبُ. وَإِنْ فُقِدَ وَقْتَ الْعَقْدِ وَوُجِدَ عِنْدَ الدُّخُولِ فَقَدْ حَصَلَ الْوَاجِبُ وَفَاتَ الْمَنْدُوبُ. وَإِنْ لَمْ يُوجَدْ إشْهَادٌ عِنْدَ الدُّخُولِ وَالْعَقْدِ وَلَكِنْ وُجِدَتْ الشُّهُودُ عِنْدَ وَاحِدٍ مِنْهُمَا فَالصِّحَّةُ قَطْعًا. وَيَأْثَمُ أَوْلِيَاءُ النِّكَاحِ لِعَدَمِ طَلَبِ الشُّهُودِ، وَإِنْ لَمْ يُوجَدْ شُهُودٌ أَصْلًا فَالْفَسَادُ قَطْعًا كَذَا فِي الْحَاشِيَةِ بِتَصَرُّفٍ.
Tsinde pa nkhani yokhudza mboni pa nikāh ndi lokakamiza (wājib), ndipo zili zoyenera kuti mbonizo zikhalepo mu nthawi imene ukwati ukumangidwa. Ngati izi zitachitike mu nthawi yomwe ukwati ukumangidwa, ndiye kuti zonse zofunikira zimakhala zakwaniritsidwa – chomwe chili wājib komanso choyenera. Ngati mboni palibe mu nthawi yomangitsa ukwati, koma zapezeka pambuyo poti amangitsa kale ukwati koma sanayambe banja (sanagonane); pamenepa chomwe chili chokakamiza chatheka koma sizili zoyenera kuchita choncho. Ndipo ngati mboni sizinapezeke mu nthawi yomwe ukwati umamangidwa, kapena mu nthawi yomwe awiriwa sanatsegule banja (pogonana); ukwatiwobe ndi wovomerezeka, koma kuti walī pamodzi ndi woyendetsa ukwati (qādhw kapena Shaykh) apeza nsambi polephera kupeza mboni mwachangu. Ndipo ngati mboni sizinapezekeretu, pamenepo ukwati palibe.
Gulu lina la ophunzira lidati sizoyenera kuitana mboni ngati ukwatiwo walengezetsedwa chifukwa kubwera kwa khamu la anthu, zakwanira iwowo kukhala mboni.
Shaykh Al-Islām Ibn Taymiyyah adati:[8]
لَا رَيْبَ فِي أَنَّ النِّكَاحَ مَعَ الْإِعْلَانِ يَصِحُّ وَإِنْ لَمْ يَشْهَدْ شَاهِدَانِ مَعَ الْكِتْمَانِ وَالْإِشْهَادِ فَهَذَا بِمَا يُنْظَرُ فِيهِ وَإِذَا انْتَفَى الْإِشْهَادُ وَالْإِعْلَانُ فَهُوَ بَاطِلٌ عِنْدَ عَامَّةِ الْعُلَمَاءِ وَإِنْ قُدِّرَ فِيهِ خِلَافٌ فَهُوَ قَلِيلٌ.
Ndi zosakaikitsa kuti nikāh yomwe yalengezetsedwa ndi yovomerezeka ngakhale pasapezeke mboni ziwiri kuchitira umboni. Koma ngati siinalengezetsedwe koma yachitiridwa umboni, imeneyo ndi nkhani ina. ndipo ngati siinalengezetsedwe komanso siinachitiridwe umboni (ndi amuna awiri okhulupirira), imeneyo ndi yosavomerezeka malinga ndi ma Ulamā ambiri; angakhale kuti ena adatenga maganizo osiyana ndi awa, koma ndi ochepa kwambiri.
Chomwe tikuyenera kumvetsetsa apa ndi chakuti, nikāh isakhale ya chinsisi. Mboni ziwiri zikupezeka pa nikāh yomwe siinalengezetsedwe ku gulu la anthu. Tsopano ngati anthu akungotengana chifukwa choti walī wavomereza koma popanda mboni, umenewo si ukwati pa chisilamu (mpaka mboni zipezeke basi). Ndipo okwatiranawo akuyenera kuonetsetsa kuti mboni zilipo mu nthawi imene akutenganayi.
Kuchita ukwati pa phone sikoletsedwa ngati zonse zoyenera zilipo monga: mkwati ndi mkwatibi, waliy wa mkaziyu, mahr idziwike komanso mboni ziwiri zazimuna zachilungamo zipezeke.
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.
[1] Kitāb Al-Umm la Imām Ash-Shāfi’ī, Vol. 5, tsamba 180
[2] Muswannaf ‘Abdur-Razzāq, Vol. 6, tsamba 266, hadīth #11317; Ibn Hibbān, #4075; Ad-Dāraqutnī, #3521
[3] Kitāb Al-Umm la Imām Ash-Shāfi’ī, Vol. 5, tsamba 180
[4] Al-Mughniy, Vol. 7, tsamba 9
[5] Al-Mabsūtw, Vol. 5, tsamba 11
[6] Al-Mawsū’ah Al-Fiqhiyyah Al-Kawniyyah, Vol. 41, tsamba 296
[7] Hāshiyah As-Swāwiy 'alā Ash-Sharh As-Swaghīr, Vol. 2, tsamba 339
[8] Al-Fatāwā Al-Kubrā, Vol. 5, tsamba 455