Ndi chifukwa chiyani Shirk ili yoopsa kwambiri kuposa machimo ena onse

Lero ndi: Friday, Shawwal 5, 1446 7:03 AM | Omwe awerengapo: 242

Funso:

10 January, 2025

Kodi ndi chifukwa chiyani Shirk ili yoopsa kwambiri kuposa machimo ena onse? Chifukwa masiku ano tikuona olalikira komanso ophunzitsa ena akulimbikira kukamba nkhani ya Shirk pomwe ife sitidziwa kuswali, kupanga wudhu' komanso ndi zina monga za twahaarah.

Yankho:

Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
 
Choyamba, Shirk ndi chinthu chomwe asilamu ambiri akuchichita ndipo akuchipeputsa. Allāh adati:[1]
 
وَمَا يُؤْمِنُ ‌أَكْثَرُهُمْ ‌بِاللَّهِ ‌إِلَّا ‌وَهُمْ مُشْرِكُونَ.
 
Ndipo ambiri mwa iwo sakhulupirira mwa Allāh kupatula kuti amamuphatikizira ndi zinthu zina.
 
Chachiwiri, Allāh sakhululuka tchimoli munthu akalichita ndipo ndi tchimo lomwe limaononga ntchito zabwino zonse za munthu:[2]
 
وَلَقَدْ أُوحِيَ إِلَيْكَ وَإِلَى الَّذِينَ مِنْ قَبْلِكَ لَئِنْ أَشْرَكْتَ ‌لَيَحْبَطَنَّ ‌عَمَلُكَ وَلَتَكُونَنَّ مِنَ الْخاسِرِينَ.
 
Ndipo ndithu, zavumbulutsidwa kale kwa iwe (Muhammad) komanso kwa omwe anabwera m’mbuyo mwako kuti ngati ungachite Shirk, ndithu ntchito zako zidzakhala zopanda pake ndipo udzakhala mu gulu la osapambana.
 
Ndipo Allāh akuyankhulanso kuti:[3]
 
وَلَوْ أَشْرَكُوا لَحَبِطَ عَنْهُمْ مَا كَانُوا يَعْمَلُونَ.
 
Akanati achita Shirk, zikanaonongeka (zabwino) zomwe iwo akhala akuchita.
 
Chachitatu, Shirk ndi tchimo loyambirira mu machimo akuluakulu. Allāh akuyankhula kuti:[4]
 
قُلْ تَعالَوْا أَتْلُ مَا حَرَّمَ رَبُّكُمْ عَلَيْكُمْ أَلَّا تُشْرِكُوا بِهِ شَيْئاً.
 
Nena (iwe Muhammad): “Bwerani, ndikuwerengerani zomwe waletsa Mbuye wanu pa inu: (choyamba wakuletsani) kuti mumuphatikizire Iyeyo ndi china chake.”
 
Mu kufotokoza kwake ‘Abdullāh Ibn Mas’ūd adati:[5]
 
سَأَلْتُ رَسُولَ اللَّهِ صلى الله عليه وسلم أَىُّ الذَّنْبِ أَعْظَمُ عِنْدَ اللَّهِ؟ قَالَ:‏ أَنْ تَجْعَلَ لِلَّهِ نِدًّا وَهُوَ خَلَقَكَ‏.‏ قَالَ قُلْتُ لَهُ: إِنَّ ذَلِكَ لَعَظِيمٌ.‏
 
Ndidamufunsa Mtumiki wa Allāh (ﷺ) kuti: “Kodi ndi tchimo liti lomwe lili lalikulu pamaso pa Allāh?” Iye adati: “Kumupatsa Allāh niddan (opikisana Naye) pomwe Iyeyo ndi Yemwe adakulenga.” Ine ndidati: “Ndithudi limenelo ndi tchimo lalikulu.”
 
Tikaona mu hadīth ya Abū Bakrah, iye akufotokoza kuti:[6]
 
كُنَّا عِنْدَ رَسُولِ اللَّهِ صلى الله عليه وسلم فَقَالَ: ‏ أَلاَ أُنَبِّئُكُمْ بِأَكْبَرِ الْكَبَائِرِ - ثَلاَثًا - الإِشْرَاكُ بِاللَّهِ وَعُقُوقُ الْوَالِدَيْنِ وَشَهَادَةُ الزُّورِ أَوْ قَوْلُ الزُّورِ . وَكَانَ رَسُولُ اللَّهِ صلى الله عليه وسلم مُتَّكِئًا فَجَلَسَ فَمَازَالَ يُكَرِّرُهَا حَتَّى قُلْنَا لَيْتَهُ سَكَتَ.
 
Tidali limodzi ndi Mtumiki wa Allāh (ﷺ) ndipo iyeyo adati: “Kodi mukufuna ndikuuzeni za machimo akuluakulu?” Iye adayankhula izi katatu. (Kenako adati): “Kumuphatikizira Allāh ndi zinthu zina, kunyoza makolo, kuchitira umboni wa bodza kapena kuyankhula za bodza.” Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adali atatsamira (khoma) kenako adakhala pansi ndipo anali akubwerenza mawuwa kufikira poti ife tidakhumba atakhala chete.
 
Pomaliza, aliyense amene wamwalira akuchita Shirk, ameneyo akalowa ku Moto ndipo akakhala kumeneko mpaka muyaya. Allāh akuyankhula motere:[7]
 
إِنَّهُ مَنْ يُشْرِكْ بِاللَّهِ فَقَدْ حَرَّمَ اللَّهُ عَلَيْهِ الْجَنَّةَ وَمَأْوَاهُ النَّارُ.
 
Ndithudi, aliyense amene wamuphatikizira Allāh ndi chilichonse, basi Allāh wapupangira Jannah kukhala yoletsedwa pa iye; ndipo malo ake okakhazikika ndi ku Moto.
 
Ndipo Mtumiki wa Allāh (ﷺ) kudzera mwa Wakī’, kuti:[8]
 
مَنْ مَاتَ يُشْرِكُ بِاللَّهِ شَيْئًا دَخَلَ النَّارَ.
 
Aliyense amene wamwalira akumuphatikizira Allāh ndi chilichonse akalowa ku Moto.
 
Ibnil Qayyim adati:[9]
 
{إِنَّ اللَّهَ لَا يَغْفِرُ أَنْ يُشْرَكَ بِهِ وَيَغْفِرُ مَا دُونَ ذَلِكَ لِمَنْ يَشَاءُ} [سُورَةُ النِّسَاءِ: ٤٨]، فَأَخْبَرَ اللَّهُ سُبْحَانَهُ أَنَّهُ لَا يَغْفِرُ ‌الشِّرْكَ، وَأَخْبَرَ أَنَّهُ يَغْفِرُ مَا دُونَهُ.
 
{Ndithudi Allāh sakhululuka yemwe wamuchitira Iye Shirk, koma amakhululuka machimo ena onse kwa yemwe wamufuna – An-Nisā’ 4:48}: apa Allāh Wapamwambamwamba akutifotokozera kuti Iyeyo sakhululuka tchimo la Shirk (munthu akamwalira nalo), ndipo akutiuzanso kuti Iyeyo amakhululuka machimo ena (posakhala Shirk).
 
Tiyeni tilidziwe liwu la Shirk kuti limatanthauza chiyani mu Chisilamu. Koma choyamba, tikabwera pa chiyankhulo, liwuli limatanthauza kuti:[10]
 
‌اتِّخَاذُ ‌الشَّرِيكِ يعني أن يُجعل واحداً شريكاً لآخر. يقال: أَشْرَكَ بَيْنَهُمَا إِذَا جَعَلَهُمَا اثْنَيْنِ، أَوْ أَشْرَكَ فِي أَمْرِهِ غَيْرَهُ إِذَا جَعَلَ ذَلِكَ الْأَمر لِاثْنَيْنِ.
 
“Kutenga bwenzi” kutanthauza kuti kutenga wina ndi kumuika ngati bwenzi la wina. Zimanenedwa: “Wawalumika iwo awiri,” ngati wawapanga awiriwo kukhala a mphamvu zofanana. Kapena zimanenedwa: “Wabweretsa mu zochita zake wina,” ngati wawapanga anthu awiri kuti akhale okhudzidwa mu zochitikazo.
 
Tikaonanso mu chitsanzo china, tipeza kuti:[11]
 
وَالإِشْرَاكُ لُغَةً: مَصْدَرُ أَشْرَكَ، وَهُوَ ‌اتِّخَاذُ ‌الشَّرِيكِ، يُقَال: أَشْرَكَ بِاللَّهِ أَيْ: جَعَل لَهُ شَرِيكًا فِي مُلْكِهِ.
 
Ndipo Al-Ishrāk pa chiyankhulo: tsinde lake ndi “ashraka” komwe kuli kutenga bwenzi. Zimanenedwa kuti: “Wamupatsa bwenzi Allāh,” kutanthauza kuti; wamupatsa Iyeyo bwenzi mu ufumu Wake.
 
Tsopano tikabwera pa Sharī’ah, liwu la Shirk limaimira:
 
‌اتِّخَاذُ ‌الشَّرِيكِ أو الند مَعَ الله جَلَّ وَعَلَا فِي الرُّبُوبِيَّتِهِ؛ أَو فِي أُلُوهِيَّتِهِ أَوْ عِبَادَتِهِ؛ أَو فِي الأسماءِهِ والصفاته.
 
Kumuphatikiza Allāh ndi wina mu Umbuye Wake; kapena mu ntchito Zake za mapemphero; kapena mu Mayina Ake ndi Mbiri Zake.
 
Apa ndi pamene Allāh akutiuza kuti:[12]
 
وَاعْبُدُوا اللَّهَ وَلا تُشْرِكُوا بِهِ شَيْئً.
 
Mpembedzeni Allāh ndipo musamuchitire Shirk ndi chilichonse (kumupatsa abwenzi komanso opikisana Naye).
 
Abū Hurayrah akufotokoza kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[13]
 
قَالَ اللَّهُ تَبَارَكَ وَتَعَالَى: أَنَا أَغْنَى الشُّرَكَاءِ عَنِ الشِّرْكِ مَنْ عَمِلَ عَمَلاً أَشْرَكَ فِيهِ مَعِي غَيْرِي تَرَكْتُهُ وَشِرْكَهُ.
 
Allāh Wapamwambamwamba adayankhula kuti: “Ine ndi wosafuna kuti ndiphatikiziridwe ndi aliyense (kapena chilichonse); choncho, aliyense amene wachita ntchito mkati mwakemo akundiphatikira Ine ndi chinachake, ndimusiya iyeyo pamodzi ndi shirk yakeyo (sindimulipira chilichonse).”
 
Mu kuyankhula kwa Mu’āwiyah Ibn Haydah, Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[14]
 
لَا يَقْبَلُ اللهُ عَزَّ وَجَلَّ مِنْ مُشْرِكٍ بَعْدَ مَا أَسْلَمَ عَمَلًا أَوْ يُفَارِقَ الْمُشْرِكِينَ إِلَى الْمُسْلِمِينَ.
 
Allāh Wapamwambamwamba salandira ntchito kuchokera kwa munthu wa Shirk pambuyo poti wabwerera mu chisilamu mpaka atawasiya ochita Shirk ndi kupita kwa asilamu (kupanga ntchito za asilamu ndi kusiya ntchito za anthu a shirk).
 
Shirk imeneyi ili mu magulu odutsa 70 ndipo onsewo mukawasonkhanitsa pamodzi, amakwana magulu awiri akulu-akulu. Adayankhula ‘Abdullāh Ibn Mas’ūd kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[15]
 
‌الرِّبَا ‌بِضْعٌ ‌وَسَبْعُونَ ‌بَابًا، ‌وَالشِّرْكُ ‌مِثْلُ ‌ذَلِكَ.
 
Katapira ali mu magulu odutsa 70, ndipo Shirk ilinso ndi magulu ngati omwewo (odutsa 70).
 
Magulu akuluakulu amenewa ndi: Shirk yaikulu yomwe imamutulutsa munthu mu chisilamu akaichita; ndipo ina ndi yaing’ono yomwe imamuyandikitsa munthu ku shirk yaikulu koma siimutulutsa munthu mu chisilamu.
 
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.


[1] Sūrah Yūsuf 12:106


[2] Sūrah Az-Zumar 39:65


[3] Sūrah Al-An’ām 6:88


[4] Sūrah Al-An’ām 6:151


[5] Swahīh Muslim, #86


[6] Swahīh Muslim, #87


[7] Sūrah Al-Mā’idah 5:75


[8] Swahīh Muslim, #92


[9] Ad-Dā’ wa Ad-Dawā’ (Al-Jawabāl Kāfī), tsamba 24


[10] Mawqi’al Islām Su’āl wa Jawāb, Vol. 1, tsamba 881, Fatwā #34817


[11] Al-Mawsū’atil Fiqhiyyatil Kawniyyah, Vol. 42, tsamba 349


[12] Sūrah An-Nisā’i 4:36


[13] Swahīh Muslim, #2985


[14] Sunan al-Nasā’ī, #2568


[15] Al-Muswannaf li Ibn Abī Shaybah, #22012; Musnad Al-Bazzār, #1935 (swahīh malinga ndi Al-Albānī mu Swahīh At-Targhīb wa At-Tarhīb, #1852)