Shirk ya chikondi
Lero ndi: Friday, Shawwal 5, 1446 7:03 AM | Omwe awerengapo: 237
Ndinawamva omwe amachita Khutbah akunenapo za Shirk ya chikondi koma sanatambasule kwambiri. Iwo adangofotokoza kuti kukondetsetsa chinthu kwambiri kumamugwetsera munthu mu Shirk ya chikondi. Kodi Shirk imeneyi ndi iti?
Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
Tikamati Shirk ya Chikondi, uku ndiye kumuphatikizira Allāh ndi zolengedwa Zake mu chikondi. Kutanthauza kuti; munthu kumachikonda chinthu china chake kapena wina wake kwambiri kuposa momwe umamukondera Allāh.
Allāh akuyankhula kuti:[1]
وَمِنَ النَّاسِ مَن يَتَّخِذُ مِن دُونِ اللَّهِ أَندَادًا يُحِبُّونَهُمْ كَحُبِّ اللَّهِۖ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓا أَشَدُّ حُبًّا لِّلَّهِ.
Mwa anthu muli ena amene adatenga pambali pa Allāh An-dādā (opikisana naye Allāh); iwo amawakonda ma an-dādāwo ndi chikondi choyenera kumukondera nacho Allāh. Pomwe okhulupirira chikondi chawo chambiri chili pa Allāh.
Ibn Kathīr akuchitira ndemanga kuti:
وَقَوْلُهُ: {وَالَّذِينَ آمَنُوا أَشَدُّ حُبًّا لِلَّهِ} وَلِحُبِّهِمْ لِلَّهِ وَتَمَامِ مَعْرِفَتِهِمْ بِهِ، وَتَوْقِيرِهِمْ وَتَوْحِيدِهِمْ لَهُ، لَا يُشْرِكُونَ بِهِ شَيْئًا، بَلْ يعبدونه وحده ويتوكلون عليه، ويلجؤون فِي جَمِيعِ أُمُورِهِمْ إِلَيْهِ.
Mawu ake Allāh oti: {Pomwe okhulupirira chikondi chawo chambiri chili pa Allāh}; chifukwa choti iwowa okhulupirirawa amamukonda kwambiri Allāh, amadziwa Ukulu Wake, amamulemekeza Iye kwambiri, amakhulupirira mu Umodzi Wake; choncho samamuphatikizira Iyeyo ndi chili chonse. Koma kuti amamupembedza Iye Yekha, amadalira mwa Iye, ndipo amafuna chithandizo kudzera mwa Iye mu zonse zokhudza umoyo wawo.
Pa nkhani imeneyi ya chikondi, Imām Ibn Qayyim al-Jawziyyah adati:[2]
وَهَاهُنَا أَرْبَعَةُ أَنْوَاعٍ مِنَ الْمَحَبَّةِ؛ أَحَدُهَا: مَحَبَّةُ اللَّهِ، وَلَا تَكْفِي وَحْدَهَا فِي النَّجَاةِ مِنْ عَذَابِ اللَّهِ وَالْفَوْزِ بِثَوَابِهِ، فَإِنَّ الْمُشْرِكِينَ وَعُبَّادَ الصَّلِيبِ وَالْيَهُودَ وَغَيْرَهُمْ يُحِبُّونَ اللَّهَ. الثَّانِي: مَحَبَّةُ مَا يُحِبُّ اللَّهُ، وَهَذِهِ هِيَ الَّتِي تُدْخِلُهُ فِي الْإِسْلَامِ، وَتُخْرِجُهُ مِنَ الْكُفْرِ، وَأَحَبُّ النَّاسِ إِلَى اللَّهِ أَقْوَمُهُمْ بِهَذِهِ الْمَحَبَّةِ وَأَشَدُّهُمْ فِيهَا. الثَّالِثُ: الْحُبُّ لِلَّهِ وَفِيهِ، وَهِيَ مِنْ لَوَازِمِ مَحَبَّةِ مَا يُحِبُّ، وَلَا تَسْتَقِيمُ مَحَبَّةُ مَا يُحِبُّ إِلَّا فِيهِ وَلَهُ. الرَّابِعُ: الْمَحَبَّةُ مَعَ اللَّهِ، وَهِيَ الْمَحَبَّةُ الشِّرِكِيَّةُ، وَكُلُّ مَنْ أَحَبَّ شَيْئًا مَعَ اللَّهِ لَا لِلَّهِ، وَلَا مِنْ أَجْلِهِ، وَلَا فِيهِ، فَقَدِ اتَّخَذَهُ نِدًّا مِنْ دُونِ اللَّهِ، وَهَذِهِ مَحَبَّةُ الْمُشْرِكِينَ. وَبَقِيَ قِسْمٌ خَامِسٌ لَيْسَ مِمَّا نَحْنُ فِيهِ: وَهِيَ الْمَحَبَّةُ الطَّبِيعِيَّةُ، وَهِيَ مَيْلُ الْإِنْسَانِ إِلَى مَا يُلَائِمُ طَبْعَهُ، كَمَحَبَّةِ الْعَطْشَانِ لِلْمَاءِ، وَالْجَائِعِ لِلطَّعَامِ، وَمَحَبَّةِ النَّوْمِ وَالزَّوْجَةِ وَالْوَلَدِ، فَتِلْكَ لَا تُذَمُّ إِلَّا إِذَا أَلْهَتْ عَنْ ذِكْرِ اللَّهِ، وَشَغَلَتْ عَنْ مَحَبَّتِهِ .
Pali mitundu inayi ku mbali ya chikondi; 1) mtundu woyamba ndi chikondi pa Allāh. Koma chikondichi sichikusonyeza kuti chakwanira kumupulumutsa munthu ku chilango cha Allāh komanso kumupezetsa malipiro a Allāh. Opembedza mafano, opembedza mtanda, Ayuda ndi ena otero amamukonda Allāh. 2) mtundu wachiwiri ndi chikondi pa zomwe Allāh amazikonda. Ichi ndi chikondi chimene chimamubweretsa munthu mu chisilamu komanso kumutulutsa munthu mu kufr (kukanira). Yemwe ali wokondedwa kwambiri mwa anthu pamaso pa Allāh ndi uyo amene ali wolondora ndi wodzipereka mu gawo la chikondi limeneli. 3) mtundu wachitatu ndi kukonda chinthu kapena munthu chifukwa cha Allāh, komwe kuli gawo limodzi mu zigawo zokonda chimene Allāh amakonda. Chikondi cha munthu pa zomwe Allāh amakonda sichingakhale chokwanira mpaka iyeyo atakonda chinthu kapena munthu chifukwa cha Allāh. 4) mtundu wachinayi ndi kukonda china chake ndi chikondi chomwe umamukondera nacho Allāh, ndipo chikondi ichi ndi chimene chikukhudzana ndi Shirk. Aliyense amene amakonda chinthu ndi chikondi cha Allāh, komanso osati chifukwa cha Allāh; iyeyu wachitenga chinthucho kukhala niddan (chopikisana ndi Allāh). Ichi ndiye ndi chikondi cha ma Mushrikūn (opembedza mafano). Ndiye kwatsala mtundu wina wa chisanu wa chikondi womwe si mbali ya mutu wathu; ichi ndi chikondi cha chilengedwe chomwe chimaikidwa mwa munthu aliyense pokonda chinthu chomwe chimamusangalatsa. Monga chikondi cha munthu wa ludzu pa madzi, kapena wanjala pa chakudya, kapena chikondi pa tulo, kapena kukonda mkazi ndi ana. Chikondichi sicholakwika pokhapokha ngati chingamutsekereze munthu kuti adzimukumbukira Allāh kapena kumutalikitsa munthu ku kumukonda Allāh.
Potambasula bwino mawu a Ibn Al-Qayyim, titha kufotokoza motere:
1) Chikondi pa Allāh: uku ndiko kumumvera Allāh pa zomwe walamula komanso waletsa. Pamene kapolo wamukonda Mbuye wake, iye akuyenera kuchita zomusangalatsa Mbuyeyo komanso kusiya zomunyasa Iye.
2) Kukonda zomwe Allāh amakonda: uku ndiye kukonda chilichonse chomwe Allāh amachikonda. Monga Allāh amakonda omwe amakhala odziyeretsa (Al-Mutatwahhirīn) komanso omwe amabwerera kwa Iye polapa (At-Tawwābīn);[3] omwe amagwira ntchito zabwino (Al-Muhsinīn)[4]; omwe amatsata Mtumiki Wake (ﷺ)[5]; omwe amakhala ndi Taqwā[6]; omwe amapirira (As-Swābirīn)[7]; omwe amadalira mwa Iye (Al-Mutawakkilīn)[8]; omwe amachita chilungamo (Al-Muqsitwīn)[9] ndi ena omwe Iye wawatchula mu Qur’ān komanso kudzera pa lilime la Mtumiki Wake (ﷺ). Apanso pali gawo lowakonda ma Swahābah a Mtumiki (ﷺ). Ndipo munthu sangawakonde awawa kupatula yekhayo amene ali ndi chikondi pa Allāh.
3) Kukonda chifukwa cha Allāh: uku ndiye kuchikonda chinthu kapena munthu chifukwa chofuna chisangalalo cha Allāh. Ngati munthu akukonda mnzake chifukwa cha Allāh, iye amamutsogolera ku zinthu zabwino ndipo amamutalikitsa ku zinthu zoipa.
Akuyankhula Al-Barā’ Ibn ‘Āzib kuti:[10]
كُنَّا جُلُوسًا عِنْدَ النَّبِيِّ صَلَّى اللهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ، فَقَالَ: إِنَّ أَوْثَقَ عُرَى الْإِيمَانِ، أَنْ تُحِبَّ فِي اللهِ، وَتُبْغِضَ فِي اللهِ.
Tidali titakhala limodzi ndi Mtumiki wa Allāh (ﷺ) ndipo iye adati: “Ndithudi gawo lolemera (lopambana) kwambiri la chikhulupiriro ndiye ndi kukonda chifukwa cha Allāh komanso kunyasidwa chifukwa cha Allāh.”
Anas Ibn Mālik akufotokoza kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[11]
ثَلَاثٌ مَنْ كُنَّ فِيهِ وَجَدَ حَلَاوَةَ الْإِيمَانِ: أَنْ يَكُونَ اللهُ وَرَسُولُهُ أَحَبَّ إِلَيْهِ مِمَّا سِوَاهُمَا، وَأَنْ يُحِبَّ الْمَرْءَ لَا يُحِبُّهُ إِلَّا لِلهِ، وَأَنْ يَكْرَهَ أَنْ يَعُودَ فِي الْكُفْرِ كَمَا يَكْرَهُ أَنْ يُقْذَفَ فِي النَّارِ.
Aliyense amene angakhale ndi zinthu zitatu izi, ameneyo wapeza kukoma kwenikweni kwa chikhulupiriro: 1) yemwe Allāh pamodzi ndi Mtumiki Wake (ﷺ) ali okondedwa kwambiri kuposa chilichonse; 2) yemwe wakonda wina ndipo sakumukonda kupatulapo chifukwa cha Allāh; 3) yemwe amadana ndi kubwerera ku Kufr ngati momwe amanyasidwira kuti aponyedwe mu Moto.
Ngati wazindikira za chimodzi mu zinthu zimene zingamuyandikitse kwa Allāh, iye amachikonda chimenecho ndi kumachichita. Ndipo zotsatira za kuchita chinthu chomwe chimamusangalatsa Allāh, kapena kukonda yemwe wakondedwa ndi Allāh; chabwino china chimakhala chikumuitananso munthuyu kuti achichite. Ndipo amakhala nthawi zambiri akutangwanika ndi kuchita zabwino zokhazokha.
4) Kukonda chinthu ndi chikondi cha Allāh: uku ndiye kuchikonda chinthu ndi chikondi chomwe umamukondera nacho Allāh. Ndithudi, chisangalalo chenicheni cha umoyo uno ndiye ndi kumudziwa komanso kumukonda Allāh kwambiri.
Alipo anthu amene amamukonda munthu mnzawo kufikira poti amachita zomwe Allāh waletsa, kapena kusiya zomwe Allāh waloleza. Kapenanso kukhala mu nkhawa ndi kuchotsa umoyo wawo chifukwa choti chomwe iwowo amachikondacho chatha, sichinapambane, chaonongeka kapena kuwasiya kumene (ngati ali munthu mnzawo).
Kodi inu simudamvepo munthu kuti wadzipha chifukwa choti timu yake ya masewera a mpira siinapambane? Simudamvepo inu kuti munthu wadzichotsa moyo wake chifukwa choti alibe ndalama? Simudamvepo inu kuti munthu wadzimanga pakhosi chifukwa cha wokondedwa wake yemwe wakwatiwa kapena wakwatira munthu wina? Ichi ndi chikondi chimene chimaikidwa mu gulu la Shirk. Ndipo ndi chikondi chimene chachulukira pakati pa asilamu ambiri mu nthawi yathu ino.
Tizindikire kuti popanda chikondi, ‘ibādah siingakhalepo. Ngati munthu wamukonda Allāh, iye amachita zimene Allāh walamula mosangalala komanso kuchokera pansi pa mtima. Chimodzimodzinso ngati munthu amakonda munthu mnzake kwambiri kuposa Allāh, mudzamupeza akuchita zomwe wokondedwa wakeyo walamula mosakakamizidwa ndipo amazichita mwa mtima wonse. Shirk ija imabwera mu njira imeneyi.
5) Chikondi cha Chilengedwe: ichi ndi chikondi chomwe aliyense amakhala nacho. Iye amakonda zinthu zomwe zamusangalatsa monga chakudya china kusiyana ndi china; kapena mtundu wina wa chovala kusiyana ndi wina; kapena malo ena kusiyana ndi malo ena. Kapenanso kuwakonda ana ndi mkazi wake. Chikondi ichi ndi chabwinobwino. Mu nthawi yomwe munthu wafika poti wachikondetsetsa chinthu kwambiri mopyola nacho malire; mwachitsanzo, kuwakonda ana ndi mkazi wako kufikira poti akukuiwalitsa kupemphera ndi kuchita zomwe Allāh walamula; pamenepo zigwera mu gawo lachinayi lija.
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.
[1] Sūrah Al-Baqarah 2:165
[2] Ad-Dā’u wa Ad-Dawā’ (Al-Jawāb Al-Kāfī), tsamba 189-190
[3] Sūrah Al-Baqarah 2:222
[4] Sūrah Al-Baqarah 2:195
[5] Sūrah Āli ‘Imrān 3:31
[6] Sūrah Āli ‘Imrān 3:76
[7] Sūrah Āli ‘Imrān 3:146
[8] Sūrah Āli ‘Imrān 3:159
[9] Sūrah Al-Mā’idah 5:42
[10] Musnad Ahmad, #18524
[11] Swahīh Al-Bukhārī, #16, #21