Kutsatira Madh-hab mu chisilamu
Lero ndi: Friday, Shawwal 5, 1446 7:02 AM | Omwe awerengapo: 503
Assalam alaikm wa rahmatullah wabarakaatuh! Sheikh, ine ndinanva kuti ma salafi satsatira madh-hab. kodi izi ndi zoona? Ndimafuna ndidziwe nawo.
Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
Choyamba: tikamati ma Salaf, tikukamba za anthu amene adali olungama m’mbuyo mwathumu kuyambira pa Mtumiki (ﷺ), ma Swahābah ake, ma Tābi’īn, komanso ma Tabi’ut Tābi’īn. Munthu amene akutsatira mibadwo itatuyi amatchedwa Salafī pofuna kutanthauza amene watsamira pa ma Salaf mu kamvetsetsedwe kake ka zinthu mu chisilamumu.
Chachiwiri: liwu la Madh-hab pa chiyankhulo limatanthauza “njira”. Liwuli limachokera ku tsinde la chi Arab la “dhahaba” kutanthauza “adapita.” Mwachitsanzo, titha kuyankhula kuti, “dhahaba fulān ilā as-Sūq” (Uje adapita ku Msika). Tikabwera mu Chisilamu, liwu la Madh-hab limaimira “njira ya kamvetsetsedwe ka malamulo a mu Sharī’ah.” Ngati m’mene munthu angatengere njira ina yake kuti akafikire ku msika.
Pali Madhāhib (kuchulukitsa kwa madh-hab) okwanira anayi ku gulu la Ahlis Sunnah wal Jamā’ah (Salafiyyūn). M’menemu muli Madh-hab Hanafiyyah (omwe akutchedwa potengera Abū Hanīfah), Madh-hab Mālikiyyah (akutchedwa potengera Imam Malik Ibn Anas), Madh-hab Ash-Shāf’ī (akutchedwa potengera Imam Muhammad Ibn Idrīsā Ash-Shāf’ī), komanso Madh-hab Hanābilah (akutchedwa potengera Ahmad Ibn Hanbal). Ma a’immah (atsogoleri) anayi onsewa adali ma Salaf.
Mukawerenga ziphunzitso zawo, mupeza kuti iwowo adali oyesetsa kufuna kutenga zomwe mibadwo ya m’mbuyo mwawo idasiya (ma Tābi’īn ndi ma Swahābah). Ma Swahābah komanso ma Tābi’īn adamwalira asakutsatira ma Madhāhib anayiwa. Ndipo iwowo ndi anthu omwe atakalowe ku Jannah asanatsatirepo Abū Hanīfah, Malik, Ash-Shafi ngakhalenso Ahmad. Choncho, sitingawatenge ma Madhāhib kukhala njira yomwe munthu atakalowere nayo ku Jannah.
Pambuyo pozindikira zimenezi, Salafiyyūn sadayambe yanyozapo m’modzi wa eni Madhāhib kapena kumunenapo kuti ndi wosafunikira mu chipembedzomu. M’malo mwake timatsatira zomwe zili zogwirizana ndi Qur’ān komanso Sunnah kuchokera kwa iwowo komanso kusiya zomwe zasemphana ndi Qur’ān komanso Sunnah mopanda kunyoza.
Palibe vuto munthu kutsatira Madh-hab amene akukulongosolera zinthu bwino kusiyana ndi ena. Koma ma Salafiyyūn satsatira Madh-hab ena alionsewo ngati asemphana ndi hadīth ya mphamvu kuchokera kwa Mtumiki wa Allāh (ﷺ). Izizi ndi zimene eni Madh-hab adatilangizanso. Choncho, mudzapeza ena akukakamirabe Madh-hab ngakhale apatsidwa hadīth ya Swahīh kuchokera kwa Mtumiki wa Allāh (ﷺ).
Tamvani mawu okoma kuchokera kwa eni Madh-hab.
Abū Hanīfah An-Nu’mān Ibn Thābit amakonda kuyankhula kuti:[1]
لَا يَنْبَغِي لمن لم يعرف دليلي أَن يُفْتِي بكلامي. وَكَانَ رضي الله عنه إذا أفتى يَقُول: هَذَا رأى النُّعْمَان بن ثَابت، يَعْنِي نَفسه، وَهُوَ أحسن مَا قَدرنَا عَلَيْهِ؛ فَمن جَاءَ بِأَحْسَن مِنْهُ، فَهُوَ أولى بِالصَّوَابِ.
“Sizili zoyenera pa yemwe sakudziwa umboni wanga (kuti wachokera kuti) iyeyo apereke fatwā pogwiritsira ntchito mawu anga.” Ndipo adalinso akuyankhula pamene akupereka fatwā kuti: “Awa ndi maganizo a An-Nu’mān Ibn Thābit (kudzinena yekha mwini wake), ndipo ndi zomwe ife tayesetsa kumbali yathu. Choncho, amene angabwere ndi zabwino kwambiri kuposa zimenezi (kuchokera mu umboni wa mphamvu), ameneyo ndi amene yankho lake likuyenera kukhala pamwamba.”
Ndipo adayankhulanso motsindika kuti:[2]
حرام على من لم يعرف دليلي أن يُفتي بكلامي، فإِننا بشر نقول القول اليوم، ونرجع عنه غدًا.
Zili zoletsedwa pa uyo amene sadziwa komwe umboni wanga ukuchokera ndi kumapereka fatwā pogwiritsira ntchito mawu anga; Chifukwatu ndithudi, ife ndi anthu timayankhula lero mawu, kenako mawa ndi kuwabwenza kuti si olondola.
Nayenso Abū ‘Abdullāh Mālik Ibn Anas Ibn Mālik Ibn Abī ‘Āmir sadawalimbikitse anthu kuti amutsatire iyeyo mwa chimbulimbuli. Iye adawalimbikitsa anthu kutsatira Qur’ān ndi Sunnah ndipo adati:[3]
إِنَّمَا أَنَا بَشَرٌ أُخْطِئُ وَأُصِيبُ، فَانْظُرُوا فِي رَأْيِي، فَكُلُّ مَا وَافَقَ الْكِتَابَ وَالسُّنَّةَ فَخُذُوا بِهِ، وَمَا خَالَفَ فَاتْرُكُوهُ.
Ine ndine munthu amene nthawi zina ndimalondola ndipo nthawi zina ndimalakwitsa. Choncho aunikeni maganizo anga; (maganizo) onse amene mwawapeza kuti akugwirizana ndi Al-Kitāb (Qur’ān) komanso As-Sunnah, amenewo atengeni. Ndipo omwe akusemphana ndi ziwirizi asiyeni.
Mu kuyankhula kwina iye adati:[4]
كُلُّ أَحَدٍ يُؤْخَذُ مِنْ قَوْلِهِ، وَيُتْرَكُ، إِلاّ صَاحِبَ هَذَا القَبْرِ صلى الله عليه وسلم.
Aliyense zokamba zake zitha kutengedwa kapena kusiidwa, kupatulapo mwini manda awa (kunena Mtumiki wa Allāh (ﷺ)).
Tikabweranso mu mawu ena, iye adati:[5]
سَنَّ رَسُوْلُ اللهِ صلى الله عليه وسلم وَوُلَاةُ الأَمْرِ بَعْدَهُ سُنَناً، الأَخْذُ بِهَا اتِّبَاعٌ لِكِتَابِ اللهِ، وَاسْتِكمَالٌ بِطَاعَةِ اللهِ، وَقُوَّةٌ عَلَى دِيْنِ اللهِ، لَيْسَ لأَحَدٍ تَغِييرُهَا وَلَا تَبْدِيلُهَا، وَلَا النَّظَرُ فِي شَيْءٍ خَالَفَهَا، مَنِ اهْتَدَى بِهَا، فَهُوَ مُهتَدٍ، وَمَنِ اسْتَنصَرَ بِهَا، فَهُوَ مَنْصُوْرٌ، وَمَنْ تَرَكَهَا، اتَّبَعَ غَيْرَ سَبِيْلِ المُؤْمِنِيْنَ.
Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adakhazikitsa Sunnah (Njira yopangira zinthu mu Chipembedzomu), ndipo chilamulo chimene chimabwera pambuyo pake ndi Sunnah; kuitenga Sunnah imeneyi ndi gawo la kutsatira Buku la Allāh, ndipo ndi chisonyezo cha kukwaniritsa kumvera Allāh, komanso (Sunnah) ndi mphamvu pa chipembedzo cha Allāh. Sizili zoyenera pa wina aliyense kuti aisinthe, kapena ayang’ane mu zomwe zikutsutsana ndi iyo. Amene waongoka ndi Sunnah, ameneyo ndi woongoka, ndipo amene wasaka chipambano kudzera mu iyo, ameneyo wapambana. Ndipo amene waisiya, watsatira njira yosakhala ya okhulupirira.
Muhammad Ibn Idrīs Ash-Shāf’ī nayenso adatenga malangizo a mphunzitsi wake Mālik Ibn Anas poyankhula kuti:[6]
إِذَا صَحَّ الحَدِيْثُ فَهُوَ مَذْهَبِي، وَإِذَا صَحَّ الحَدِيْثُ، فَاضْرِبُوا بِقَولِي الحَائِطَ.
Ikakhala kuti hadīth ndi ya swahīh, amenewo ndiwo madh-hab anga; ndipo ikakhala kuti hadīth ndi ya swahīh, amenyetseni mawu anga ku khoma.
Ar-Rabī’ Ibn Sulaymān akufotokoza kuti Ash-Shāf’ī adati:[7]
إِذَا وَجَدْتُمْ فِي كِتَابِي خِلَافَ سُنَّةِ رَسُولِ اللَّهِ صلى الله عليه وسلم، فَقُولُوا بِسُنَّةِ رَسُولِ اللَّهِ صلى الله عليه وسلم وَدَعُوا مَا قُلْتُ.
Mukapeza mu buku langa zosemphana ndi Sunnah ya Mtumiki wa Allāh (ﷺ), inu yankhulani pogwiritsa ntchito Sunnah ya Mtumiki wa Allāh (ﷺ) ndipo siyani zimene ndinayankhula.
Mu mawu ena, Imām Ash-Shāf’ī adayankhula kuti:[8]
إذا وَجَدْتُمْ سُنَّة فَاتَّبِعُوهَا، وَلَا تَلْتَفِتُوا إلى قول أحد.
Ikakufikirani inu Sunnah (kuchokera mu hadīth ya mphamvu), itsatireni; ndipo musatembenukire ku mawu a munthu aliyense.
Ndipo mu kuyankhula kwina, iye (Ash-Shāf’ī) adati:[9]
كُلُّ مَا قُلْتُ؛ وَكَانَ عَنِ النَّبِيِّ صلى الله عليه وسلم خِلَافَ قَوْلِي مِمَّا يَصِحُّ، فَحَدِيثُ النَّبِيِّ صلى الله عليه وسلم أَوْلَى، وَلَا تُقَلِّدُونِي.
Pa zonse zomwe ndidanena, (mukapeza kuti) pali uthenga wolondola kuchokera kwa Mtumiki wa Allāh (ﷺ) womwe ukusiyana ndi mawu anga, basi hadīth ya Mtumiki wa Allāh (ﷺ) ikuyenera kukhala yoyambirira (kutsatiridwa), ndipo musanditsatire ine (mwa umbuli).
Bahr adati:[10]
قَالَ الشَّافِعِيُّ: لَقَدْ ضَلَّ مَنْ تَرَكَ حَدِيثَ رَسُولِ اللَّهِ صلى الله عليه وسلم لِقَوْلِ مَنْ بَعْدَهُ.
Adayankhula Ash-Shāf’ī kuti: Wasochera amene wasiya hadīth ya Mtumiki wa Allāh (ﷺ) potsatira mawu a amene anabwera pambuyo pake.
Ahmad Ibn Hanbal Ash-Shaybānī adali Imām wa anthu otsatira Sunnah mu nthawi yake. Iye sadawalangize anthu kuti amutsatire iyeyo m’malo mwa Mtumiki wa Allāh (ﷺ).
Mu kufotokoza kwake Abū Shāmah Al-Maqdisī adati:[11]
وَقد كَرِهَ الإِمَام أَحْمد أَن يَكْتبَ فَتَاوِيهِ وَكَانَ يَقُول: لَا تكْتبُوا عَنِّي شَيْئًا، وَلَا تُقَلِّدُونِي وَلَا تَقْلِدُوا فلَانا وَفُلَانًا وَخُذُوا مِنْ حَيْثُ أَخَذُوا.
Imām Ahmad ankaletsa kuti ma fatāwā ake adzilembedwa ndipo amayankhula kuti: “Musalembe chilichonse kuchokera kwa ine, ndipo musanditsatire mwa umbuli; komanso musatsatire uje mwa umbuli. Inu tengani kumene iwowo adatenga [komwe kuli kwa Mtumiki wa Allāh (ﷺ)].”
Adayankhula Ahmad Ibn Hanbal kuti:[12]
مَنْ رَدَّ حَدِيثَ النَّبِيِّ صلى الله عليه وسلم، فَهُوَ عَلَى شَفَا هَلَكَةٍ.
Aliyense amene wakana hadīth ya Mtumiki wa Allāh (ﷺ), ameneyo ali pa malire a chionongeko.
Tikaona mu zoyankhula za ma a’immah onsewa, sitikupezapo pamene iwo akuyankhula kuti mukanditsatira ine mukalowa ku Jannah. M’malo mwake onse akulimbikitsa kutsatira Mtumiki wa Allāh (ﷺ) komanso Qur’ān.
Pomaliza ‘Ā’ishah adayankhula kuti:[13]
إِنَّ أَبَا بَكْرٍ رضي الله عنه، قَالَ: «لَسْتُ تَارِكًا شَيْئًا كَانَ رَسُولُ اللَّهِ صلى الله عليه وسلم يَعْمَلُ بِهِ إِلَّا عَمِلْتُ بِهِ، وَإِنِّي لَأَخْشَى إِنْ تَرَكْتُ شَيْئًا مِنْ أَمْرِهِ أَنْ أَزِيغَ»
Ndithudi Abū Bakr (Allāh asangalale naye) adayankhula kuti: “Sindisiya ine chilichonse chimene Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adachichita kupatula kuti nanenso ndichichita; chifukwa ine ndikuopa kuti ndikasiya chilichonse mu chilamulo chake, ndidzasochera.”
Pochitira ndemanga hadīth imeneyi, Ibn Battwah adati:[14]
هَذَا يَا إِخْوَانِي الصِّدِّيقُ الْأَكْبَرُ يَتَخَوَّفُ عَلَى نَفْسِهِ الزَّيْغَ إِنْ هُوَ خَالَفَ شَيْئًا مِنْ أَمْرِ نَبِيِّهِ صلى الله عليه وسلم، فَمَاذَا عَسَى أَنْ يَكُونَ مِنْ زَمَانٍ أَضْحَى أَهْلُهُ يَسْتَهْزِئُونَ بِنَبِيِّهِمْ وَبِأَوَامِرِهِ، وَيَتَبَاهَوْنَ بِمُخَالَفَتِهِ، وَيَسْخَرُونَ بِسُنَّتِهِ. نَسْأَلُ اللَّهَ عِصْمَةً مِنَ الزَّلَلِ وَنَجَاةً مِنْ سُوءِ الْعَمَلِ.
Uyu, eh iwe mchimwene wanga, ndi As-Swiddīq Wamkulu yemwe amadziwopera kusochera pa iye mwini ngati angasiye china chake kuchokera mu chilamulo cha Mtumiki wa Allāh (ﷺ). Tsopano chingachitike ndi chiyani mu nthawi yomwe anthu akuseleula Mtumiki wawo (ﷺ) komanso kukana chilamulo chake, ndipo akupikisana mu kutsutsana naye komanso kuinyoza Sunnah yake? Tikumupempha Allāh kuti atiteteze mu kuphuluza komanso atipulumutse ku ntchito zoipa.
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.
[1] Al-Inswāf fi Bayan Asbābul Ikhtilāf, tsamba 104
[2] Majmū’ah Rasā’il, Vol. 1, tsamba 135
[3] Tārīkh Al-Islām, Vol. 11, tsamba 327
[4] Siyar A’lām An-Nubalā, Vol. 8, tsamba 93
[5] Siyar A’lām An-Nubalā, Vol. 8, tsamba 98
[6] Siyar A’lām An-Nubalā, Vol. 8, tsamba 248; Vol. 10, tsamba 35
[7] Ma’rifatus Sunan wal Āthār, Vol. 1, tsamba 217, hadīth #454; Al-Madkhal ilā as-Sunan al-Kubrā, tsamba 205, hadīth #249
[8] Tārīkh Dimishq li Ibn ‘Asākir, Vol. 51, tsamba 386
[9] Ādāb Ash-Shāf’ī, tsamba 15
[10] Al-Faqīh wal Mutafaqqih, Vol. 1, tsamba 386
[11] Mukhtaswar Al-Mu’ammal, tsamba 61
[12] Al-Ibānatil Kubrā, Vol. 1, tsamba 260, hadīth #97
[13] Al-Ibānatil Kubrā, Vol. 1, tsamba 245, hadīth #77 (yomwe ikupezeka mu Swahīh Al-Bukhārī, #3093)
[14] Buku lake ndi lomwelo latchulidwa pamwambapa komanso malo ake omwewo.