Kukwatira mkazi wa chipembedzo china
Lero ndi: Friday, Shawwal 5, 1446 7:06 AM | Omwe awerengapo: 531
Kodi ndizovomerezeka mu chisilamu kukwatira mkazi wa chipembedzo china monga chikhristu? Ndinamva sheikh ena akunena kuti ma swahaabah amakwatira akazi azipembedzo zina ndi kumakhala nawo. Ndiye mundithandize pamenepo in shaa Allah.
Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
Choyamba: tizindikire za mkazi wa chipembedzo china kuti ndi ndani. Mkazi wa chipembedzo china:
1. Akhonza kukhala wa chikhristu
2. Akhonza kukhala wa chiyuda
3. Akhonza kukhala wopembedza ma jinn
4. Akhonza kukhala wopembedza mizimu
5. Akhonza kukhala wopembedza zosema kapena zoumba
6. Akhonza kukhala wopembedza zolengedwa zina za moyo
7. Akhonza kukhala wopembedza zolengedwa zina zopanda moyo
8. Akhonza kukhala yemwe alibe chipembedzo china kupatulapo kupembedza maganizo ake
Mu chilolezo chake Allāh, Iye adaloleza mwamuna wa chisilamu kukwatira akazi awiri oyambirirawo: wa chikhristu kapena chiyuda. Umboni wa izi tikuupeza mu āyah iyi:[1]
وَالْمُحْصَنَاتُ مِنَ الْمُؤْمِنَاتِ وَالْمُحْصَنَاتُ مِنَ الَّذِينَ أُوتُوا الْكِتَابَ مِن قَبْلِكُمْ إِذَا ءَاتَيْتُمُوهُنَّ أُجُورَهُنَّ مُحْصِنِينَ غَيْرَ مُسَافِحِينَ وَلَا مُتَّخِذِىٓ أَخْدَانٍ.
Ndi (aloledwanso kwa inu) akazi odzisunga kuchokera mwa akazi okhulupirira komanso odzisunga kuchokera mwa omwe adapatsidwa Buku m’mbuyo mwanu (Ayuda ndi Akhristu), pamene mwawapatsa mahr yawo, uku mukukhumba kukhala odzisunga osati achiwerewere kapena kuwatenga ngati zibwenzi zanu.
Mu mawu amenewa: Allāh waika zinthu zingapo zimene mwamuna wokhulupirira akuyenera kuzindikira asanamukwatire mkazi yemwe ali wa chikhristu kapena chiyuda:
a) Mkaziyo asakhale wa chimasomaso (yemwe amavala moonetsa ziwalo za thupi lake, amene alibe manyazi ndi amuna achilendo, komanso ndi womasuka ndi amuna achilendo, amenenso alibe anzake achimuna).
b) Asakhalenso kuti amapanga naye ubwenzi wa harām.
Pochitira ndemanga āyah imeneyi, Ibn Kathīr adati:
وَهُوَ قَوْلُ الْجُمْهُورِ ههنا، وَهُوَ الْأَشْبَهُ لِئَلَّا يَجْتَمِعَ فِيهَا أَنْ تَكُونَ ذِمِّيَّةً وَهِيَ مَعَ ذَلِكَ غَيْرُ عَفِيفَةٍ، فَيُفْسِدُ حَالَهَا بِالْكُلِّيَّةِ وَيَتَحَصَّلُ زَوْجُهَا عَلَى مَا قِيلَ فِي الْمَثَلِ: «حَشَفًا وَسُوءَ كَيْلَةٍ» وَالظَّاهِرُ مِنَ الآية أن المراد من المحصنات: العفيفات عن الزنا.
Awa ndiwo mawu a ophunzira ochuluka, omwe alinso olondola – ndi cholinga choti apewe kuphatikizana kuwiri komwe kuli: mkaziyo kukhala woti si msilamu komanso nkukhala wa chigololo. Zomwe zingatanthauze kuti iyeyo ndi mkazi amene ali woonongekeratu, ndipo mwamuna wake apeza zomwe aluya anayankhula chitsanzo ichi: “Katundu woipa ndipo wanamiza kudzera pa muyezo (sikero).” Tanthauzo la pamwamba chabe ka āyah imeneyi ndi lakuti akazi amene akunenedwa kuti odzisunga: ndi akazi amene ali odziteteza ku chiwerewere.
Chachiwiri: ndi zoonadi kuti ena mu gulu la ma Swahābah adakwatirapo akazi achikhristu. Izi tikuzipeza mu kuyankhula kwake Ibn Abī Hātim yemwe akuti:[2]
عن ابن عباس: نَزَلَتْ هَذِهِ الْآيَةُ {وَلَا تَنْكِحُواْ الْمُشْرِكَاتِ حَتَّى يُؤْمِنَّ} قَالَ: فَحَجَزَ النَّاسُ عَنْهُنَّ حَتَّى نَزَلَتِ الآية الَّتِي بَعْدَهَا: {وَالْمُحْصَنَاتُ مِنَ الَّذِينَ أُوتُواْ الْكِتَابَ مِنْ قَبْلِكُمْ} فنكح الناس نِسَاءِ أَهْلِ الْكِتَابِ، وَقَدْ تَزَوَّجَ جَمَاعَةٌ مِنَ الصَّحَابَةِ مِنْ نِسَاءِ النَّصَارَى وَلَمْ يَرَوْا بِذَلِكَ بأساً أخذاً بهذا الْآيَةِ الْكَرِيمَةِ.
Ibn ‘Abbās adafotokoza kuti: itatsika āyah iyi: {Musakwatire akazi opembedza mafano mpaka atakhulupirira} iye adati: Amuna adawasiya akazi amenewa (osawakwatira) kufikira pamene idavumbulutsidwa āyah ina pambuyo pake yoti: {Ndi akazi odzisunga kuchomwe mwa omwe adapatsidwa Buku m’mbuyo mwanu}. Choncho, amuna adakwatira akazi kuchokera mwa eni Buku (Ayuda ndi Akhristu), ndipo ndithudi ambiri mu gulu la ma Swahābah adakwatira kuchokera mu akazi achikhristu ndipo palibe yemwe adaona vuto pa zimenezi – iwo adagwiritsira ntchito āyah imeneyi.
Ngakhale ma Swahābah amakwatira akazi amenewa, iwowo adawapanga kukhala a makrūh (osakondedwa) poyerekeza ndi akazi okhulupirira (amene akuyenera kukhala oyambirira kukwatibwa.
1. Iwo amaopa kukwatira akazi achikhristu ndi chiyuda chifukwa ambiri mwa iwowo ndi osadzisunga (chibwenzi kwa iwowo amachitenga ngati ndi chinthu chabwinobwino).
Shaqīq Ibn Salamah adafotokoza kuti:[3]
تزوج حذيفة يهودية فكتب إليه عمر: خلِّ سبيلها، فكتب إليه: أتزعم أنها حرام فأخلي سبيلها؟ فقال: لا أزعم أنها حرام، ولكني أخاف أن تعاطوا المومسات منهن .
Hudhayfah adakwatira mkazi wa chiyuda ndipo ‘Umar adamulembekera kalata pomuuza kuti: “Musiye mkazi ameneyo.” Hudhayfah adalemba kwa ‘Umar kuti: “Ukufuna kundiuza kuti mkaziyu ndi woletsedwa choncho ndimusiye?” ‘Umar adamulembera kuti: “Sindikunena kuti mkaziyo ndi woletsedwa; koma ndikuopa kuti ukhonza kukwatira omwe ali achimasomaso mwa iwowo.”
2. Amaopanso kuti amuna akayamba kukwatira akazi amenewa, akazi okhulupirira adzayamba kukwatiwana ndi amuna osakhulupirira kapena kukhala opanda amuna (ngati akaziwa adzakhale akukana kukwatiwana ndi amuna okanira podziwa kuti zimenezo ndi harām.
‘Āmir Ibn ‘Abdullāh Ibn Nastwās adafotokoza kuti:[4]
أن طلحة بن عبيد الله نكح بنت عظيم اليهود، قال : فعزم عليه عمر إلا ما طلقها
Twalhah Ibn ‘Ubaydullah adakwatira mwana wa mkazi wa mtsogoleri wa chiyuda. ‘Umar adakakamira kuti Twalhah amusiye banja mkaziyo.
Ibn Jarīr At-Twabarī pochitira ndemanga zomwe ‘Umar adanena kwa Hudhayfah komanso Twalhah adati:[5]
وإنما كره عمر لطلحة وحذيفة رحمة الله عليهم نكاحَ اليهودية والنصرانية: حذرًًا مِن أن يقتدي بهما الناس في ذلك، فيزهدوا في المسلِمات، أو لغير ذلك من المعاني، فأمرهما بتخليتهما.
‘Umar sadasangalatsidwe ndi Twalhah komanso Hudhayfah, Allāh awachitire onse chisoni, za kukwatira kwawo mkazi wa chiyuda ndi wa chikhristu; kuopera kuti anthu angayambe kuwatsatira mu zimenezi ngati zitsanzo zawo kenako ndi kuyamba kusasangalatsidwa ndi akazi achisilamu. Kapena pa zifukwa zina zofananirako. Choncho, adawalamula iwowo kuti awasiye banja akaziwa.
3. China ndi chakuti ma Swahābah akuluakuluwa amadziwa za zotsatira zosakhala bwino pambuyo pokwatira mkazi ngati ameneyu.
Tsopano tiyeni tione zotsatira zenizeni pa nkhani yokwatira mkazi wa chikhristu kapena chiyuda:
1. Mwamuna akuyenera kusamaliritsa pa mkaziyu pa chipembedzo chake. Sakuyenera iye kukhala wofooka mu Âqīdah yake ngakhale ndi dontho lomwe. Makamakanso mkaziyo akakhala kuti ndi wotsata chipembedzo chakecho. Izi zikutanthauza kuti mkaziyo apachika mitanda mnyumbamo, adzimverera nyimbo zotamanda Yesu mnyumbamo, ndipo ana sakhala otetezeka ku chikhulupiriro chopotokachi chifukwa mayi ndi yemwe amalera ana.
2. Iyeyu sadzitha kumukana mwamunayu kukhala naye malo amodzi mu nthawi yomwe ali pa masiku ake. mwachidule, mkaziyu amupangitsa mwamunayu kuchita nyasi zimene samayenera kuchita ndipo akhala m’modzi mwa amuna a uve omwe adzisemphana ndi Sharī’ah.
3. Mkaziyu potuluka mnyumba sadzivala hijāb. Ndipo nsambi za kusavala kwake kwa hijab zizigwera pa mwamunayo pokhapokha ngati mwamunayo akumulamula mkaziyo ndipo mkaziyo akumachotsa hijab kunja kwa nyumba kapena akutuluka asanavale hijab mwamunayo ngati kulibeko. Ndipo izi ndi zomwe mkaziyu angamachite. Pa chifukwa ichi, mwamunayu akhala woyaluka.
4. Mkaziyo mudzamupeza akumasukirana ndi amuna achilendo nthawi yomwe watuluka mnyumbamo.
5. Banja likatha, dziko limapereka mphamvu kwa mayi kuti ndi amene atakhale ndi ana – kapena mwamunayo akamwalira. Izi zidzapangitsa kuti anawo asatsatire chipembedzo cha Allāh koma atsatire chipembedzo cha mayi awowo.
Zimafotokozedwa kuti kukwatira mkazi wa chikhristu ndi kololedwa koma sikolimbikitsidwa chifukwa ana amakhala ali pa chiopsezo chachikulu kuti atha kukhala akhristu. Izizi zaonekera mwa amuna achisilamu ambiri pa chisankho chawo chomwe adapanga pokwatira mkazi wa chikhristu.
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.
[1] Sūrah Al-Mā’idah 5:5
[2] Tafsīr Ibn Kathīr, Vol. 3, tsamba 331
[3] Tafsīr At-Twabarī, Vol. 4, tsamba 366; Tafsīr Ibn Kathīr, Vol. 1, tsamba 583
[4] Al-Muswannaf Ibn ‘Abdur-Razzāq, Vol. 6, tsamba 79
[5] Tafsīr At-Twabarī, Vol. 4, tsamba 366