Kupisilira madzi pomwe ukuchita wudhu
Lero ndi: Friday, Shawwal 5, 1446 7:03 AM | Omwe awerengapo: 334
Kodi munthu yemwe akupanga wudhu ndizoleledwanso pa iye kupisirila madzi mu nthawi yomwe akupanga wudhu? Nanga akatelo, ngati zili zololedwa, sizimaononga madziwo?
Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
Palibe hadīth imene imaletsa munthu kutunga madzi mu chiwiya chomwe ukupangira wudhu pogwiritsira ntchito dzanja. Ndipo hadīth imene tikuipeza ndi yomwe m’modzi wa ma Swahābah, yemwe ndi Uthman Ibn ‘Affan, amapisa dzanja lake mu chiwiya chomwe munali madzi opangira wudhu ndi kumatunga ndi dzanjali.
Akufotokoza Humrān yemwe adali kapolo woomboledwa ndi ‘Uthmān kuti:[1]
أَنَّهُ رَأَى عُثْمَانَ بْنَ عَفَّانَ دَعَا بِإِنَاءٍ، فَأَفْرَغَ عَلَى كَفَّيْهِ ثَلاَثَ مِرَارٍ فَغَسَلَهُمَا، ثُمَّ أَدْخَلَ يَمِينَهُ فِي الإِنَاءِ فَمَضْمَضَ، وَاسْتَنْشَقَ...
“Ndidamuona ‘Uthmān Ibn ‘Affān akuitanitsa madzi mu chiwiya. Kenako (madziwo atabweretsedwa), anawathira pa manja ake ndi kuwasambitsa kokwanira katatu. Kenako anapisa dzanja lake la manja mu chiwiya chija ndi (kutunga kenako ndi) kuwathira mkamwa komanso ndi kukwezera m’mphuno pambuyo pake ndi kuwamina madziwo….”
Kuchokera mu hadīth imeneyi, tiona kuti ‘Uthman adapisa dzanja lake m’madzi pomwe amapanga wudhu.
Koma choyamba munthu asambitse kaye manjawo kokwana katatu ndiye adzipisa bwino ndi dzanja lakelo.
Allāh ndiye Mwini kudzindikira.
[1] Swahīh Al-Bukhārī, #159