Ndi zosakwanira kungokhulupirira basi koma osamagwira ntchito

Lero ndi: Friday, Shawwal 5, 1446 6:55 AM | Omwe awerengapo: 311

Funso:

13 January, 2025

Pali ena amene amanena kuti munthu chikhulupiriro ndi mu mtima basi zilibe ntchito zomwe iwe umachita ndi ziwalo zako chifukwa Allaah akayang'ana mitima yathu osati matupi athu zomwe amachitazo. Kodi izizi ndi zoona?

Yankho:

Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
 
Tikabwera mu chikhulupiriro cha Chisilamu, tipeza kuti zomwe zamanga chikhulupiriro ndi zinthu ziwiri: mawu (qawl) ndi ntchito (‘amal). Popanda chimodzi mwa ziwirizi, chimenecho sichingatchedwe chikhulupiriro mu chipembedzo cha Allāh.
 
Ili ndi gawo limene ambiri mwa asilamu adaliphonya. Iwo amaona ngati ndi zokwanira kungonena kuti akukhulupirira mwa Allāh, angelo Ake, mabuku Ake, atumiki Ake, Tsiku la Chiweruzo komanso Qadar; koma osagwira ntchito yolingana ndi ‘Aqīdah imeneyi.
Hassān Ibn ‘Atwiyyah adati:[1]
 
إِنَّ الْإِيمَانَ فِي كِتَابِ اللَّهِ صَارَ إِلَى الْعَمَلِ.
 
Chikhulupiriro mu Buku la Allāh chimafikira mpaka ku ntchito (sichithera pa mawu okha basi).
 
Akuyankhula Hudhayfah Ibnil Yamān kuti:[2]
 
إِنِّي لَأَعْرِفُ أَهْلَ دِيْنَيْنِ: أَهْلُ ذَيْنِكَ الدِّيْنَيْنِ فِي النَّارِ، قَوْمٌ يَقُولُونَ: الْإِيمَانُ قَوْلٌ وَإِنْ زَنَا، وَإِنْ سَرَقَ، وَقَوْمٌ يَقُولُونَ: فَمَا بَالُ الصَّلَوَاتِ الْخَمْسِ، إِنَّمَا هُمَا صَلَاتَانِ: صَلَاةُ الْغَدَاةِ، وَصَلَاةُ الْمَغْرِبِ، أَوِ الْعِشَاءِ .
 
Ine ndikuwadziwa anthu a zipembedzo ziwiri: anthu a zipembedzo ziwiri zimenezi onse ali ku Moto. (Oyamba) ndi anthu amene amayankhula kuti: Īmān ndi chikhulupiriro basi ngakhale udzichita chiwerewere komanso kuba. Ndipo (achiwiri mwa) anthuwa ndi omwe amayankhula kuti: Kodi nde ziti zomaswali kasanuzi. Ndithudi swalāh zilipo ziwiri basi: swalāh ya Fajr ndi Maghrib kapena ‘Ishā.
 
Ndipo Al-Hasan Al-Baswrī adati:[3]
 
لَوْ شَاءَ اللَّهُ عز وجل لَجَعَلَ الدِّينَ قَوْلًا لَا عَمَلَ فِيهِ، أَوْ عَمَلًا لَا قَوْلَ فِيهِ، وَلَكِنْ جَعَلَ دِينَهُ قَوْلًا وَعَمَلًا. فَمَنْ قَالَ قَوْلًا حَسَنًا، وَعَمِلَ سَيِّئًا رُدَّ قَوْلُهُ عَلَى عَمَلِهِ، وَمَنْ قَالَ قَوْلًا حَسَنًا وَعَمِلَ عَمَلًا صَالِحًا رَفَعَ قَوْلُهُ عَمَلَهُ.
 
Akadafuna Allāh Wapamwambamwamba, akadachipanga Chipembedzo kungokhala pa mawu chabe koma mkati mwake osakhalamo kugwira ntchito, kapena kugwira ntchito koma mkati mwake osakhalamo mawu. Koma kuti adachipanga chipembedzo Chake kukhalamo m’menemo mawu ndi ntchito. Tsopano uyo amene wayankhula mawu abwino ndi kumagwira ntchito zoipa; mawu akewo adzabwenzedwa ku ntchito yakeyo (zonse sizidzalandiridwa). Ndipo uyo amene wayankhula mawu abwino ndi kugwira ntchito yolungama, mawu ake adzakweza ntchito yake (ndipo zonsezi zidzafika kwa Allāh).
 
Ichi ndi chifukwa chake timanenetsa kuti Īmān si mu mtima mokha. Monga m’mene akuyankhulira Ibn Taymiyyah kuti:[4]
 
الْقَلْبُ هُوَ الْأَصْلُ .فَإِذَا كَانَ فِيهِ مَعْرِفَةٌ وَإِرَادَةٌ سَرَى ذَلِكَ إلَى الْبَدَنِ بِالضَّرُورَةِ.
 
Mtima ndiye phata (la chikhulupiriro). Ngati mu mtimamo muli kuzindikira komanso chikhumbokhumbo (chofuna kuchita chinthu chabwino), zimenezo zimafalikira ku thupi lonse motsindikizika.
 
Mu kuyankhula kwake Abī Hurayrah adati:[5]
 
الْقَلْبُ مَلِكٌ وَالْأَعْضَاءُ جُنُودُهُ فَإِذَا طَابَ الْمَلِكُ طَابَتْ جُنُودُهُ وَإِذَا خَبُثَ الْمَلِكُ خَبُثَتْ جُنُودُهُ.
 
Mtima ndi mfumu ndipo ziwalo ndi asilikali ake. Ngati mfumu ili yabwino, asilikalinso nawo amakhala abwino. Koma ngati mfumu yaipa, nawonso asilikali amaipa.
 
Mu kuyankhula kwina, Al-Hasan Al-Baswrī adati:[6]
 
لَيْسَ الْإِيمَانُ بِالتَّحَلِّي وَلَا بِالتَّمَنِّي، وَلَكِنْ مَا وَقَرَ فِي الْقَلْبِ وَصَدَّقَتْهُ الْأَعْمَالُ. مَنْ قَالَ حَسَنًا وَعَمِلَ غَيْرَ صَالِحٍ رَدَّهُ اللَّهُ عَلَى قَوْلِهِ، وَمَنْ قَالَ حَسَنًا وَعَمِلَ صَالِحًا رَفَعَهُ الْعَمَلُ، ذَلِكَ بِأَنَّ اللَّهَ عَزَّ وَجَلَّ يَقُولُ: {‌إِلَيْهِ ‌يَصْعَدُ الْكَلِمُ الطَّيِّبُ وَالْعَمَلُ الصَّالِحُ يَرْفَعُهُ}.
 
Chikhulupiriro sichinagone pa kungodzikongoletsa kunjaku kapena kungokhumba (kuti mumalakalaka kukalowa ku Jannah). Komatu (chikhulupiriro) ndi chimene chimakhazikika mu mtima ndipo chimatsindikizidwa ndi ntchito. Aliyense amene wayankhula zabwino koma osagwira ntchito yabwino, Allāh adzamubwenzere mawu akewo (sadzamulipira kalikonse); ndipo yemwe wayankhula zabwino ndi kutsogozanso ntchito yabwino, Allāh adzamukwezera ntchito yakeyo. Izi zili choncho chifukwa Allāh, Wapamwambamwamba, adayankhula kuti: (Kwa Iye ndi kumene kumakwera Liwu labwino, ndipo ntchito yabwino imakweza liwulo – Sūrah Fātwir 35:10).
 
Mukuyankhula kwake Shaykhul Islām Ibn Taymiyyah adati:[7]
 
فَإِذَا كَانَ الْقَلْبُ صَالِحًا بِمَا فِيهِ مِنَ الْإِيمَانِ عِلْمًا وَعَمَلًا قَلْبِيًّا لَزِمَ ضَرُورَةُ صَلَاحِ الْجَسَدِ بِالْقَوْلِ الظَّاهِرِ وَالْعَمَلِ بِالْإِيمَانِ الْمُطْلَقِ كَمَا قَالَ أَئِمَّةُ أَهْلِ الْحَدِيثِ: قَوْلٌ وَعَمَلٌ قَوْلٌ بَاطِنٌ وَظَاهِرٌ وَعَمَلٌ بَاطِنٌ وَظَاهِرٌ وَالظَّاهِرُ تَابِعٌ لِلْبَاطِنِ لَازِمٌ لَهُ مَتَى صَلَحَ الْبَاطِنُ صَلَحَ الظَّاهِرُ وَإِذَا فَسَدَ فَسَدَ؛ وَلِهَذَا قَالَ مَنْ قَالَ مِنْ الصَّحَابَةِ عَنْ الْمُصَلِّي الْعَابِثِ: لَوْ خَشَعَ قَلْبُ هَذَا لَخَشَعَتْ جَوَارِحُهُ.
 
Ngati mtima uli woongoka ku mbali ya chikhulupiriro, maphunziro (a chipembedzo) komanso zikhumbokhumbo; apa zotsatira zake ndi ntchito zooneka zomwe zilinso zolongosoka, monga mawu ndi ntchito za thupi. Monga momwe adayankhulira mtsogoleri wa ophunzira ma ahādīth kuti: Mawu ndi ntchito za thupi, za mkati ndi kunja komwe (zimalongosoka). Zomwe zili kunja zigwirizane ndi zomwe zili mkati, choncho ngati za mkati zili zolongosoka, ndiye kuti za kunjanso zikhala zolongosoka; ndipo ngati za mkati zisali zolongosoka, ndiye kuti za kunja nazonso zikhala zosalongosoka. Pa chifukwa ichi, m’modzi wa ma Swahābah adayankhulapo za yemwe amapemphera mosalongosoka kuti: “Ngati mtima wake wakhala wodzichepetsa komanso wa chidwi, thupi lake likadakhalanso lodzichepetsa komanso lodekha (poswalipo).”
Tizindikirenso kuti, chikhulupiriro chimene munthu amakhala nacho mu mtima sichikhazikika mu mtimamo malinga ndi ntchito zimene munthu akuchita. Ngati iye akugwira ntchito zabwino, chikhulupiriro chake chimakwera ndipo iye amakhala chifupi ndi Allāh. Pomwe akamagwira ntchito zoipa, iyeyu chikhulupiriro chake chimapunguka ndipo sakhala chifupi ndi Allāh.
 
Abū Hātim adayankhula kuti:[8]
 
‌أَنَّ ‌الإِيمَانَ ‌يَزِيدُ ‌بِالطَّاعَةِ، ‌وَيَنْقُصُ ‌بِالْمَعْصِيَةِ.
 
Ndithudi Chikhulupiriro chimaonjezekera kudzera mu kutsatira (malamulo a Allāh pamodzi ndi Mtumiki Wake ﷺ), ndipo chimapunguka kudzera mu kunyoza (malamulo a Allāh pamodzi ndi Mtumiki Wake ﷺ).
 
Mu kuyankhula kwake Khaythamah Ibn ‘Abdur-Rahmān adati:[9]
 
الْإِيمَانُ يَسْمَنُ فِي الْخِصْبِ وَيَهْزُلُ فِي الْجَدْبِ فَخِصْبُهُ الْعَمَلُ الصَّالِحُ وَجَدْبُهُ الذُّنُوبُ وَالْمَعَاصِي.
 
Chikhulupiriro chimakhala cha mphamvu mu nthaka ya chonde, ndipo chimakhala chofooka mu nthaka yoguga. Nthaka ya chonde ndi ntchito zabwino, ndipo nthaka yoguga ndi uchimo komanso kunyoza (malamulo a Allāh pamodzi ndi Mtumiki Wake ﷺ).
 
Ndipo Humayr Ibn Habīb Ibn Khumāshah adafotokoza kuti agogo ake (Khumāshah) adati:[10]
 
إِنَّ ‌الإِيمَانَ ‌يَزِيدُ ‌وَيَنْقُصُ. فَقِيلَ لَهُ: وَمَا زِيَادَتُهُ وَمَا نُقْصَانُهُ؟ قَالَ: إِذَا ذَكَرْنَا اللَّهَ وَخَشَيْنَاهُ فَذَلِكَ زِيَادَتُهُ. وَإِذَا غَفَلْنَا وَنَسَيْنَا وَضَيَّعْنَا فَذَلِكَ نُقْصَانُهُ.
 
“Ndithudi, Chikhulupiriro chimaonjezereka komanso chimapunguka.” Zidafunsidwa kwa iwo: “Ndi chani chomwe chimaonjezera chikhulupiriro komanso chimene chimapungula?” Iwo adati: “Pamene tikumukumbukira Allāh komanso kumamuopa, chikhulupiriro chimaonjezereka. Ndipo tikakhala kuti tatairira, tamuiwala Iye ndi kusochera, chikhulupiriro chimapunguka.”
Pa chifukwa ichi, msilamu weniweni ndi uyo amene wakhulupirira mu mtima ndiponso akuyankhula zabwino zokhazokha ndi pakamwa pake komanso akuchita ntchito zimene Allāh pamodzi ndi Mtumiki Wake (ﷺ) adalamula ndipo akusiya zimene adaletsa.
 
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.


[1] Al-Ibānatil Kubrā li Ibn Battwah, Vol. 2, tsamba 898, hadīth #1253


[2] Al-Ibānatil Kubrā li Ibn Battwah, Vol. 2, tsamba 892, hadīth #1246


[3] Al-Ibānatil Kubrā li Ibn Battwah, Vol. 2, tsamba 896, hadīth #1250


[4] Majmū’ Al-Fatāwā, Vol. 7, tsamba 187


[5] Shu’bal Īmān, Vol. 1, tsamba 132-133, hadīth #109; Majmū’ Al-Fatāwā, Vol. 10, tsamba 15


[6] Al-Ibānatil Kubrā li Ibn Battwah, Vol. 2, tsamba 805, hadīth #1093


[7] Majmū’ Al-Fatāwā, Vol. 7, tsamba 187


[8] Majmū’ Al-Fatāwā, Vol. 7, tsamba 187


[9] Al-Īmān li Ibn Taymiyyah, tsamba 178


[10] At-Twabaqāt Al- Kubrā, Vol. 4, tsamba 281