Kuwerengera Surah Al-Fatihah m'madzi ndi cholinga chofuna chitetezo

Lero ndi: Friday, Shawwal 5, 1446 6:54 AM | Omwe awerengapo: 254

Funso:

14 January, 2025

Kodi kuwerenga Surat Al-Fatihah ndi kuuzira m'madzi ndikumwa madziwo; kapena kumwaza madziwo mnyumba pofuna chitetezo ndizolakwika?

Yankho:

Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
 
Sitikupezapo umboni ulionse woti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adaphunzitsa ma Swahābah ake kuti akafuna kudziteteza kudzera mu chitetezo cha Allāh awerengere m’madzi Sūrah Al-Fatihah ndiye amwe madziwo. Kapena madziwo awamwaze mnyumbamo ndipo nyumbayo idzakhala yotetezeka ku ufiti ndi zonse zoipa.
 
Zomwe tikuzipeza kudzera mu hadīth ya Abū Sa’īd Al-Khudrī ndi zakuti ena mu gulu la ma Swahābah adawerenga Sūrah Al-Fātihah pa mwendo wa mfumu ya mudzi wina wake yomwe inalumidwa ndi nankhalizi kapena njoka. Ndipo nthawi iliyonse yomwe Sūrah imeneyi imawerengedwa, wowerengayo akaimaliza amauzira mpweya pa balalo. Ndipo adaiwerenga Sūrah imeneyi kokwanira kasanu ndi mphambu ziwiri (7). Ndipo uthenga umenewu utamupeza Mtumiki wa Allāh (ﷺ), iye adayankhula kuti: “Chidamudziwitsa ndi chiyani kuti adziwe zoti Sūrah Al-Fātihah ndi Ruqyah?” Werengani Sunan At-Tirmidhī, #2064; komanso Sunan Ibn Mājah, #2156.
 
Kuchokera mu hadīth imeneyi, ena mu gulu la ma ‘ulamā’ adafotokoza kuti munthu amene akudwala, palibe vuto kuwerenga Sūrah Al-Fātihah ndi kumauzira pamene akumva ululupo. Ndipo ena adatinso vuto palibe kuwerenga kokwanira ka 7, ndipo nthawi iliyonse ukamaliza kuiwerenga Sūrah imeneyi, uuzire m’madzi ndipo madziwo umwe pofuna kupeza machilitso amene Allāh adawaika mu Sūrah imeneyi.
 
Koma ku nkhani yofuna chitetezo, umboni ulionse palibe. Izizi tikuzipeza mu chikhulupiriro cha ma Sūfiyyah amene amachita zinthu za m’mutu mwawo mopanda kutsatira chiphunzitso cha Mtumiki wa Allāh (ﷺ) pamodzi ndi ma Salaf.
 
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.