Kuseweretsedwa maliseche ndi mkazi wako

Download PDF

Lero ndi: Tuesday, Rabi' Al-Awwal 9, 1447 9:06 AM | Omwe awerengapo: 1154

Funso:

12 August, 2025

Kodi kuseweretsedwa maliseche ndi mkazi wako ndi koletsedwa pa Sharī’ah?

Yankho:

Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
 
Pamene mwamuna ndi mkazi akwatirana, iwo ali ololedwa kugwirana paliponse, kusisitana, kupsopsonana, kunyambitana komanso kuyankhulana mawu achikoka mu nthawi yomwe ali awiri. Chilakolako chenicheni chimabwera pamene munthu akuyang’ana, kusisita, kupsopsona komanso kuyankhula mawu okoma.
 
Gawo lina la kuseweretsana ndiye kuti mwamuna agundanitse thupi lake lonse ndi la mkazi wake. Mu gawo ilinso muli kukumbatirana, kusisitana, kugudubuzana, kunyamula thupi la mkazi ndi manja, kukhukhuza khungu pa thupi la mnzakeyo, kutsamirana kapena kugonerana. Izi ndi zololedwa onse atavala zovala kapena ali maliseche.
 
Ibn Qudāmah adati:[1]
 
ولا بأسَ ‌بالتَّلذُّذِ ‌بها ‌بينَ ‌الألْيَتَيْنِ ‌مِن ‌غيرِ ‌إيلَاجٍ؛ لأنَّ السُّنّةَ إنما وردتْ بتَحْريمِ الدُّبُرِ، فهو مَخْصوصٌ بذلك، ولأنَّه حُرِّمَ لأجلِ الأذَى، وذلك مخصوصٌ بالدُّبُرِ، فاخْتَصَّ التَّحريمُ بِه.
 
Ndipo palibe vuto mwamuna kuseweretsa gawo la pakati pa matako (a mkazi wake) popanda kulowetsa maliseche ake (kumalo otulukira chimbudzi), chifukwa zomwe zaletsedwa ndi malo otulukira chimbudziwo (kulowetsako maliseche kapena chala); ndipo malowa atchulidwa paokha, ndipo ndi oletsedwa chifukwa choti ndi onyasa, komanso (nyasizo) zili kumalo amenewo; choncho, kwaletsedwa mopatulidwa.
 
Mu kuyankhula kwake Zakariyyā Al-Answārī adati:[2]
 
‌وَالتَّلَذُّذُ ‌بِالدُّبُرِ ‌بِلَا ‌إيلَاجٍ ‌جَائِزٌ.
 
Kuseweretsa kumbuyo kwa mkazi (kunja kwa malo amene pamatulukira chimbudzi) popanda kulowetsa (maliseche) ndi zololedwa.
 
Apa mwamuna atha kumakhukhuza maliseche ake pakati pa matako a mkazi wake; atha kumasisita ndi dzanja lake pa mpata womwe uli pakati pa maliseche a mkaziyo ndi njira yotulukira chimbudzi; kapenanso atha kumakhukhuza ndi chida chake pamwamba pa njirayi koma asalowetse.
 
Al-Kasānī adati:[3]
 
‌مِنْ ‌أَحْكَامِ ‌النِّكَاحِ ‌الصَّحِيحِ ‌حِل ‌النَّظَرِ ‌وَالْمَسِّ ‌مِنْ ‌رَأْسِهَا إِلَى قَدَمَيْهَا حَالَةَ الْحَيَاةِ؛ لِأَنَّ الْوَطْءَ فَوْقَ النَّظَرِ وَالْمَسِّ، فَكَانَ إِحْلَالُهُ إِحْلَالاً لِلْمَسِّ وَالنَّظَرِ مِنْ طَرِيقِ الأُوْلَى.
 
Ena mwa malamulo olondola a nikāh ndi akuti zili zololedwa kuyang’ana komanso kusisita gawo lililonse la thupi (la mkazi) kuchokera ku mutu kwake mpaka kufikira kumapazi ngati iye ali moyo (sali wakufa). Chifukwa kugonana kumadutsa pa kuona ndi kugwira, choncho zili zolondola kuti kugwira ndi kuona ndi kololedwa.
 
Ibn ‘Ābidīn adati:[4]
 
سَأَل أَبُو يُوسُفَ أَبَا حَنِيفَةَ عَنِ الرَّجُل يَمَسُّ فَرْجَ امْرَأَتِهِ وَهِيَ تَمَسُّ فَرْجَهُ لِيَتَحَرَّكَ عَلَيْهَا هَل تَرَى بِذَلِكَ بَأْسًا؟ قَال: لَا، وَأَرْجُو أَنْ يَعْظُمَ الأُجْرُ.
 
Abū Yūsuf adamufunsa Abū Hanīfah zokhudza mwamuna amene amagwira maliseche a mkazi wake komanso mkaziyo amagwira maliseche a mwamuna wake ndi cholinga choti akweze chilakolako chake, kuti: “Kodi pamenepa pali vuto lililonse?” Iye adati: “Ayi, ndipo ndikukhulupirira kuti malipiro ake akhala ochuluka (Allāh awalipira awiriwa malipiro ambiri).” 
 
Mwamuna atha kusangalala ndi mkazi wake momwe akufunira; chomwe chaletsedwa pa iye ndi mathanyula (kugonana ndi mkazi wake kudzera malo otulukira chimbudzi) komanso kugonana naye mkaziyo ali pa masiku ake kapena pa nifās (akabereka kumene). Kupatula izi, iye atha kusangalala naye mkaziyo mu njira iliyonse yomwe akufuna, monga kumupsopsona, kumusisita, kumuyang’ana ndi zina zotero. Mpaka athanso kumuyamwa nsonga za mawere ake, chifukwa izi zimagwera pa nkhani ya kugonana komwe kuli kololedwa.
 
Kuyamwa nsonga za mawere ndi china mwa zinthu zimene ambiri mwa amuna samachilabadira. Ichi ndi chinthu chimene mkazi chimamukwezetsa chilakolako chake chifukwa ndi chimene chimakhala chokondedwa kwa iyeyu. Zimatha kutheka mwamuna kungoyamwa pang’ono nsonga za mawere a mkazi wake, kenako iye nayamba kugonana naye; izi ndi zosakondedwa popeza mwamunayu amakhala akuphonya limodzi mu magawo okwaniritsa zilakolako za mkazi wake.
 
Funso litha kubwera pa nkhani yoti mwamuna akukhukhuza maliseche ake pa ntchafu za mkazi wake, kapena mimba ya mkaziyo, kapena pa mawere ake mkaziyo, kapena pakati pa mawere a mkaziyo kapena zigawo zina za thupi la mkaziyo; komanso mkazi kukhukhuza maliseche ake pa gawo lina la thupi la mwamuna wake – kuti kodi izi ndi zololedwa?
 
Yankho la funso limeneli ndi lakuti ndizololedwa kutero. Mu kuyankhula kwake Ibn ‘Ābidīn adati:[5]
 
الْإِنْزَالِ بِالْكَفِّ أَوْ ‌بِتَفْخِيذٍ أَوْ تَبْطِينٍ امْرَأَتَهُ أَوْ أَمَتَهُ لَا شَيْءَ عَلَيْهِ.
 
Mwamuna kuthira kudzera mu kuseweretsedwa ndi dzanja, kapena kukhukhuza maliseche ake pa ntchafu kapena mimba ya mkazi wake angakhalenso mzakazi wake, palibe vuto lililonse pa iye.
 
Choncho, ngati mwamuna angathire chifukwa chokhukhuza maliseche ake pa thupi la mkazi, pamenepo palibe vuto lililonse. Izi zimathandizanso ngati mkaziyo ali pa masiku ake, kapena wabereka kumene ndipo mwamuna ali ndi chilakolako chokwera kwambiri. Koma ngati izi zingachitidwe popanda kufunikira kwenikweni, zikhalabe zololedwa koma zosakondedwa pang’ono.
 
Izi zikutipatsa chithunzithunzi choti mwamuna ndi mkazi ali ndi ufulu pa thupi la wina ndi mnzake. Pa chifukwa ichi, zaloledwa pa onse awiri kugundanitsa maliseche awo pa thupi la mnzakeyo mpaka kufikira pokwaniritsidwa chilakolako.
 
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.


[1] Al-Mughnī, Vol. 10, tsamba 228


[2] Asnā’ Al-Matwālib, Vol. 3, tsamba 113


[3] Badāi’ as-Swanāi’, Vol. 2, tsamba 331


[4] Hāshiyah Ibn ‘Ābidīn, Vol. 5, tsamba 234


[5] Radd Al-Muhtār, Vol. 2, tsamba 399 komanso Vol. 4, tsamba 27

Funsoli lakuthandizani?