Kupirira ku Fitnah ya Chiwerewere
Download PDFLero ndi: Tuesday, Rabi' Al-Awwal 9, 1447 9:03 AM | Omwe awerengapo: 606
Funso langa ndi lakuti: masiku anowa mafitnah a zinā (chiwerewere) ali paliponse mbali zonse akazi ngakhalenso amuna, ndiye tingapilire bwanji ku mayesero amenewa?
Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
Fitnah ya chiwerewere inakhazikika pakati pathu chifukwa tinasiya zomwe Allāh adavumbulutsa. M’malo mwake tinatenga njira za anthu omwe adasochera pambuyo poti chiongoko chidawafikira. Allāh adachipanga chiwerewere kukhala nyasi komanso njira yoipa kwambiri. Ndipo adaipanga nikāh kukhala njira yokhayo imene mwamuna wachilendo ndi mkazi wachilendonso angapangire ubale. Choncho, ngati tingasiye kutsatira zimene zavumbulutsidwa kwa ife, zotsatira zake ndi chionongeko.
Allāh walamula akazi kuvala hijāb, kukhazikika mnyumba zawo, kutsitsa maso awo pamene akuyankhulana ndi amuna achilendo, kusamenyetsa mapazi awo pamene akuyenda mu msewu, komanso kusakongoletsa mawu awo pamene akuyankhulana ndi mwamuna wa chilendo. Ndipo amuna talamulidwa kutsitsa maso athu ndi kusunga maliseche athu posachita chiwerewere. Zonsezi zinaperekedwa kwa ife ndi cholinga choti pakati pathu pakhale kuongoka. Koma ambiri mwa anthu sazindikira ndipo amayesa ngati kumeneku ndi kuponderezedwa.
Adayankhula Usāmah Ibn Zayd komanso Sa’īd Ibn Zayd Ibn ‘Amr Ibn Nufayl kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adafotokozapo zokhudza akazi kuti:[1]
مَا تَرَكْتُ بَعْدِي فِي النَّاسِ فِتْنَةً أَضَرَّ عَلَى الرِّجَالِ مِنَ النِّسَاءِ.
Sindidasiye pambuyo panga (ndikamwalira) mwa anthu mayesero ovulaza kwambiri pa amuna kuposa akazi.
Kusonyeza kuti akazi ndi mayesero. Ndipo mayesero akatengedwa ngati si mayesero, zotsatira zake ndi kuvulala kwakukulu. Pali ma ahādīth ochuluka amene akufotokoza za fitnah ya chiwerewere mu masiku omaliza Qiyāmah isanafike.
Abū Hurayrah adafotokoza kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[2]
وَالَّذِي نَفْسُ مُحَمَّدٍ بِيَدِهِ لَا تَقُومُ السَّاعَةُ حَتَّى يَظْهَرَ الْفُحْشُ.
Ndikulumbirira mwa Yemwe mzimu wa Muhammad uli m’Dzanja Lake! Qiyāmah siidzafika mpaka Al-Fuhsh itaonekera (Al-Fuhsh apa akuimira chiwerewere).
Mu hadīth ina, Abū Hurayrah adapereka uthenga kuchokera kwa Mtumiki wa Allāh (ﷺ) kuti iye adati:[3]
وَالَّذِي نَفْسِي بِيَدِهِ لَا تَفْنَى هَذِهِ الْأُمَّةُ حَتَّى يَقُومَ الرَّجُلُ إِلَى الْمَرْأَةِ فَيَفْتَرِشَهَا فِي الطَّرِيقِ فَيَكُونَ خِيَارُهُمْ يَوْمَئِذٍ مَنْ يَقُولُ لَوْ وَارَيْتَهَا وَرَاءَ هَذَا الْحَائِطِ.
Ndikulumbirira mwa Yemwe mzimu wanga uli m’Dzanja Lake! Sudzaonongeka Ummah uno mpaka mwamuna adzatengana ndi mkazi ndi kukagonana mu msewu. Ndipo wabwino mwa iwowo mu nthawi imeneyo adzakhala yemwe adzayankhule kuti: Bola ukanamutengera mkaziyo pa ngodya apo.
Ma ahādīth oterewa alipo ochuluka. Chomwe wokhulupirira akuyenera kuchita ndi kukwatira komanso kudzitalikitsa ku nyasi zonse.
Adayankhula ‘Uthmān Ibn ‘Affān kuti:[4]
فَإِذَا أَحْسَنَ النَّاسُ فَأَحْسِنْ مَعَهُمْ، وَإِذَا أَسَاءُوا فَاجْتَنِبْ إِسَاءَتَهُمْ.
Choncho, pamene anthu akuchita ubwino, iwe chita ubwino limodzi ndi iwowo. Ndipo pamene akuchita zoipa, basi pewa zoipa zawozo (usachite nawo).
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.
[1] Sunan at-Tirmidhī, #2780
[2] Swahīh Ibn Hibbān, #6844 (Swahīh lighayrihi – Silsilah As-Swahīhah, #3211)
[3] Musnad Abī Ya’lā, #6183 (Qawī potengera Ad-Dārānī)
[4] Swahīh Al-Bukhārī, #695