Zoona zenizeni za dziko la Iran
Download PDFLero ndi: Tuesday, Rabi' Al-Awwal 9, 1447 9:06 AM | Omwe awerengapo: 319
Kodi nkoyenela kuti tidziyankhula zinthu zolakwika kwa anthu okhala mu dziko la Iran pomwe akuwathibula ma Israel pamene mayiko ena achisilamu angokhala chete?
Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
Choyambirira dziwani kuti dziko la Iran limatsatira Chikhulupiriro cha chi Shī’ah makamaka nthambi ya Ithna ‘Ashariyyah. Pafupifupi 90-95% ya anthu okhala mdzikoli ali pa chikhulupiriro chimenechi. Pali zambiri zimene tingafotokoze ku mbali ya zikhulupiriro za ma Shī’ah. Zina mwa izo ndi izi:
1. Iwowo amatemberera ma Swahābah m’mizikiti ndi m’misonkhano yawo
2. Adaika mu shahadah yawo mawu oti: “Ndikuchitira umboni kuti Abū Bakr, ‘Umar, ‘Uthmān, 'Ā’ishah ndi Hafswah onse ali ku Moto.” Ndipo munthu sangakhale Shī’ah pokhapokha mawu amenewa awayankhule.
3. Amanena kuti Qur’ān yomwe tili nayo leroyi si yomwe idavumbulutsidwa kwa Mtumiki (ﷺ). Amanena kuti idasinthidwa ndipo ma āyāt ena adachotsedwamo ndi kuonjezeredwa ndi zokamba za anthu (ma Swahābah).
4. Amatsindika kuti Mut’ah ikadapitirirabe mpaka lero (Mut’ah ndi ukwati wosakhalitsa umene ma Swahābah ankachita Mtumiki wa Allāh (ﷺ) asadamwalire).
5. Ali ndi ma ahādīth omwe amafotokoza kuti ma Swahābah onse kupatulapo atatu adachita kufr pambuyo pa kumwalira kwa Mtumiki wa Allāh (ﷺ).
6. Amakhulupirira kuti mkazi amene wakwatiwa kwa munthu yemwe si Shī’ah kwa iwowo ndi wololedwa kumukwatira chifukwa amati sali pa banja koma pa chibwenzi.
7. Amati ‘Umar Ibnil Khattwāb anali munthu wa Bid’ah.
8. Samavomereza utsogoleri wa Abū Bakr, ‘Umar ndi ‘Uthmān.
9. Amakhulupirira kuti ma Imām awo omwe amawatsatira ndi olemekezeka kuposa atumiki kupatulapo Mtumiki wa Allāh (ﷺ).
10. Zodabwitsanso kwambiri ndi zakuti, ma Imām amenewa amawapempha zosowekera zawo (kumachita du’ā kwa iwowo) ndipo mu chikhulupiriro chawo amati ma Imām ali ndi mphamvu za umulungu.
11. Kubisa chikhulupiriro (Tuqyah) ndi nsichi imodzi kuchokera mu nsichi za chikhulupiriro chawo.
12. Kunama, phuzo, miseche komanso kunyoza ndi mbali imodzi yopezera malipiro awo.
13. Dothi lopezeka pa manda a Husayn kapena Imām wawo aliyense muli machilitso.
14. Iwo amati anthu onse adalengedwa kuchokera ku dothi wamba kupatulako ma Shī’ah omwe adalengedwa kuchokera ku dothi lopambana la ku Jannah.
15. Ma Shī’ah akamamamuona munthu wotsatira Sunnah, iwowa amatsindika kuti mwazi wake uli wololedwa kuukhetsa. Kusonyeza kuti ife pamaso pawo ndi anthu amene taloledwa kuphedwa mopandanso kukaikira kulikonse. Iwowo akhala akupha anthu otsatira Sunnah omwe amakhala mdziko lawolo m’mbuyomu ndipo panopa zimenezi amachita ngakhale ambiri sazindikira.
Ndiye pochepetsa zokamba, palibe zinthu zolakwika zimene zimayankhulidwa zokhudza ma Shī’ah. Iwowo ndi anthu amene adasemphana ndi chikhulupiriro cholondola ngakhale atati adzimenya nkhondo ndi Israel, Russia kaya America. Ifeyo sitingawadandaule chifukwa cha kuvulaza kwawo kumene amachita pa chipembedzo cha Allāh.
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.