Kuchita Qunut pa Fajr iliyonse

Download PDF

Lero ndi: Wednesday, Rabi' Al-Akher 29, 1447 7:57 AM | Omwe awerengapo: 656

Funso:

07 October, 2025

As-Salām a'lykum wa rahmatullahi wa barakatuh. Dera lomwe ndikukhala kuli mizikit ingapo, koma omwe ndimapita maka pa fajr ndi wina omwe uli chapafupi. Vuto ndilakuti imam komanso gulu lochuluka la jamaat pamenepa ndiya Qadiriyyah nde moti qunūt ndi tsiku lililonse. Ine nthawi yokweza manja sindikweza nawo chifukwa sindinamvepo kut Mtumiki chinali chizolowezi chake kuchita qunūt pa fajr swalah. Vuto lina ndilakuti, imam amatha kuwuza ma sheikh ena kut aswalitse chonsecho enawo mbiri zawo ndiza matalasimu. Akaswalitsa amatalisimuwo, ine swalah yanga ndimaibwerenza. Pano ndafika pokaikira swalah ya imam wapa mzikitipa kut mwina swalah siilandilidwa mwina nayenso ndiwa matalasimu. Moti tsiku lililonse swalah yanga ndimaibwerenza. Mtima oswali pa jamah ndilinawo, alhamdulillah. Kodi ndikulakwa kukaikira kusalandiridwa kwa swalah yanga? Allah akupatseni zabwino pano pa Dunia komanso ku Akhirah chifukwa ndapindula komanso ndikupindulabe ndi nkhan ya Aqeedah kudzera kuma lesson anu. Ameen.

Yankho:

Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
 
Choyamba, chomwe chili chofunikira pa munthu ndi kutsatira umboni kuchokera mu Qur’ān komanso Sunnah, ngakhale umboniwo ukutsutsana ndi madh-hab a munthuyo. Ndipo ndi zofunikira kumvetsetsa Qur’ān ndi Sunnah kudzera mu kamvetsetsedwe ka ma Salaf, osati mu kamvetsetsedwe kathu kokha. Tikamati ma Salaf tikukamba za ma Swahābah ndi ma Tābi’īn.
 
Zomwe zili zolondolola kuchokera mu Sunnah ndi zakuti: zili mu Sunnah kuchita Qunūt mu nthawi ya mavuto (pamene vuto lalikulu lawagwera asilamu kapena ena mwa asilamu). Pamenepa zidzakhala mustahabb (zokondedwa) kuchita Qunūt ndi kumamupempha Allāh kuti achotse vutoli. Koma ngati vuto palibepo pakati pathu, mfundo yolondola ndi yakuti Qunūt siimafunikira (werengani funso 43 kuti mudziwe zokhudza hadīth imene imakamba za Qunūt).
 
Chachiwiri, mu funso lanuli muli zinthu ziwiri, gawo loyamba ndi nkhani ya Qunūt ndipo gawo lachiwiri ndi nkhani ya matalasimu.
 
Ikakhala nkhani ya Qunūt, Shaykhul Islām Ibn Taymiyyah adati:[1]
 
وقد تبين بما ذكرناه أن القنوت يكون عند النوازل... ومن قال إنه من أبعاض (أجزاء) الصلاة التي يجبر بسجود السهو، فإنه بنى ذلك على أنه سنة يسن المداومة عليه، بمنزلة التشهد الأول ونحوه، وقد تبين أن الأمر ليس كذلك، فليس بسنة راتبة، ولا يسجد له، لكن من اعتقد ذلك متأولاً في ذلك، له تأويله، كسائر موارد الاجتهاد، ولهذا ينبغي للمأموم أن يتبع إمامه فيما يسوغ فيه الاجتهاد، فإذا قنت قنت معه، وإن ترك القنوت لم يقنت، فإن النبي صلى الله عليه وسلم قال: (إنما جعل الإمام ليؤتم به). وقال: (لا تختلفوا على أئمتكم)، وثبت عنه في الصحيح أنه قال: (يصلون لكم، فإن أصابوا فلكم ولهم، وإن أخطأوا فلكم وعليهم.
 
Tidabweretsa poyera kale mu zomwe tidatchula kuti Qunūt ikuyenera kuchitidwa mu nthawi ya An-Nawāzil (pamene kwagwa mavuto)… aliyense amene anganene kuti Qunūt ndi gawo la Swalāh lomwe likuyenera kupangiridwa Sajdah As-Sahw (ngati mu swalayo siinachitidwa) ameneyo akutsamira ku mbali yoti iyoyo ndi Sunnah yomwe ikuyenera kuchitidwa nthawi zonse, ngati mmene zilili pa nkhani ya Tashahhud woyamba ndi zina zotero. Koma ndi zodziwika kuti izi si momwe zilili; iyo (Qunūt) si Sunnah yoti idzichitidwa nthawi iliyonse, ndipo sipakuyenera kuti pachitidwe Sajdah As-Sahw ngati iyo (Qunūt) yasiidwa. Ndipo ngati wina angakhulupirire kuti iyo ndi Sunnah ya nthawi zonse potengera Ijtihād yake, izi ndi zabwinobwino, ngati momwe zililinso zina zonse mu zigawo za Ijtihād.
 
Choncho, munthu amene akuswali kumbuyo kwa Imām akuyenera kutsatira zimene akuchita Imām mu zinthu zimene Ijtihād ikugwerapo. Ndiye ngati iye (Imām) achita Qunūt, iyeyo nayenso achite nawo. Ngati Imām sachita Qunūt, nayenso asachite nawo. Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati: “Imām amasankhidwa kuti atsatiridwe.” Ndipo adatinso: “Musasemphane ndi Imām wanu.” Ndipo zili zotsindikizika kuchokera mu As-Swahīh kuti iye [Mtumiki wa Allāh (ﷺ)] adati: “Iwowo amakutsogolerani mu Swalāh; ngati angamailondoloze, (malipiro) ali pa inu komanso pa iwowo. Koma ngati angailakwitse, (malipiro) ali pa inu ndipo tchimo lili pa iwowo.”
 
Ndipo nawonso Shaykh Ibn Al-‘Uthaymīn adayankhulapo motere:[2]
 
وسئل الشيخ ابن عثيمين رحمه الله: عندنا إمام يقنت في صلاة الفجر بصفة دائمة فهل نتابعه؟ وهل نؤمن على دعائه؟ فأجاب :من صلى خلف إمام يقنت في صلاة الفجر فليتابع الإمام في القنوت في صلاة الفجر، ويؤمن على دعائه بالخير، وقد نص على ذلك الإمام أحمد رحمه الله تعالى.
 
Adafunsidwa Shaykh Ibnil ‘Uthaymīn (Allāh awachitire chisoni): Ife tili ndi Imām amene amachita Qunūt pa Swalāh iliyonse ya Fajr, kodi tikuyenera kumutsatira? Nanga tikuyenera kumanena Āmīn pa du’ā yake? Shaykh adayankha kuti: “Yemwe akuswali kumbuyo kwa Imām amene amachita Qunūt mu Swalāh ya Fajr, iyeyu amutsatire imamuyo mu Qunūt ya pa Fajr ndipo adzichita Āmīn pa du’ā yakeyo. Izi zidafotokozedwa ndi Imām Ahmad (Allāh amuchitire chisoni).”
 
Tsopano likakhala gawo lokhudza kuswali kumbuyo kwa Imām amene akudziwika ndi mchitidwe wolemba matalasimu; Swalāh ya munthuyu siilandilidwa. Zindikirani kuti matalasimu ndi ufiti ndipo mu Chisilamumu ndi zoletsedwa munthu kulemba kapena kukatenga matalasimu. Choncho, aliyense amene wadziwika kuti amalemba matalasimu, ngati iyeyu amatsogolera anthu pa Swalāh, anthu auzidwe kuti asiye kuima kumbuyo kwake. Ngati anthu pa mzikitipo saona kulakwika kwa matalasimu pambuyo poti aunikiridwa, sizili zomuyenera msilamu yemwe amamuopa Allāh ndi Tsiku la Chiweruzo kuswali mu mzikiti woterewu.
 
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.


[1] Majmū’ Al-Fatāwā, Vol. 23, tsamba 115


[2] Majmū` Fatāwā Ibn Al-‘Uthaymīn, Vol. 14, tsamba 177

Funsoli lakuthandizani?