Hadith yokhudza kuchita Qunut pa Fajr iliyonse si yolondola
Download PDFLero ndi: Wednesday, Rabi' Al-Akher 29, 1447 7:57 AM | Omwe awerengapo: 294
Anthu amene amachita Qunut pa Fajr amapereka hadith ya Anas yomwe imanena kuti Mtumiki wa Allah (mtendere ndi madalitso zipite kwa iye) ankachita Qunut pa Fajr kufikira pamene adamwalira. Ndipo ina imati ngakhalenso Abu Bakr, Umar ndi Uthman ankachita nawonso Qunut pa Fajr. Kodi izizi ndi zoonadi?
Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
Ma ahādīth amenewo alipodi koma si olondola – ndi ofooka ndipo ena mwa ma ‘ulamā’ amati ndi opekedwa. Tiyeni tiwaone ma ahādīth amenewo mwa tsatanetsatane.
Hadīth yoyamba:
Abū Ja’far Ar-Rāzī akufotokoza kuti Ar-Rabī’ Ibn Anas adati Anas Ibn Malik adanena kuti:[1]
أَنَّ النَّبِىَّ صلى الله عليه وسلم قَنَتَ شَهْرًا يَدْعُو عَلَيْهِمْ ثُمَّ تَرَكَهُ، وَأَمَّا فِى الصُّبْحِ فَلَمْ يَزَلْ يَقْنُتُ حَتَّى فَارَقَ الدُّنْيَا.
Ndithudi, Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adachita Qunūt kwa mwezi, akumupempha Allāh kuti awapatse chilango iwowo (ma Banī Dhakwān, Ri’li, Banī Lihyān ndi Banī ‘Uswayyah) kenako adasiya (kuchita Qunūt). Koma pakakhala pa Subh (Fajr), iyeyo sadasiye kuchita Qunūt mpaka adasiyana ndi dzikoli.
Abū Ja’far Ar-Rāzī dzina lake lidali ‘Īsā Ibn Māhān Ar-Rāzī ndipo ma Muhaddithīn (‘ulamā’ odziwa bwino ma ahādīth) mu nthawi yake adati ndi wofooka (dhwa’īf).
Tikaona mu chitabu cha Tahdhīb At-Tahdhīb[2], tipeza mawu oti:
قال أحمد بن حنبل: ليس بقوي فى الحديث. وقال يحيى بن معين: يكتب حديثه ولكنه يخطىء. وقال عمرو بن علي: فيه ضعف، وهو من أهل الصدق، سيىء الحفظ. وقال أبو زرعة: شيخ يهم كثيرا. وقال النسائي: ليس بالقوي. وقال ابن حبان: كان ينفرد عن المشاهير بالمناكير، لا يعجبنى الاحتجاج بحديثه إلا فيما وافق الثقات. وقال العجلي: ليس بالقوي.
Ahmad Ibn Hanbal adati: “Iyeyu sadali qawiyy (wa mphamvu) mu ma ahādīth.” Ndipo Yahya Ibn Ma’īn adati: “Iyeyu amalemba ma ahādīth ake, koma amalakwitsa.” Ndipo ‘Amr Ibn ‘Alī adati: “Pali kufooka kwina kwake mwa iyeyu; ndipo iyeyu ndi m’modzi wa anthu achilungamo, koma adali woipa mu kasungidwe ka zinthu m’mutu mwake.” Abū Zur’ah adati: “Iye adali nkhalamba yomwe imazunguzika nthawi zambiri.” An-Nasā’ī adati: “Iyeyu sadali qawiyy.” Ibn Hibbān adati: “Iyeyu amasemphana ndi odziwika bwino pa ma ahādīth chifukwa choti amapereka ma ahādīth okanidwa; ndipo sindingakonde kupereka hadīth yake ngati umboni kupatula ngati hadīth yake yagwirizana ndi ya ena omwe ali odalilika.” Ndipo Al-‘Ajlī: “Iyeyu sali qawiyy.”
Hadīth yachiwiri:
Ismā’īl Al-Makkī ndi ‘Amr Ibn ‘Ubayd adafotokoza kuti Al-Hasan adapereka uthenga kuchokera kwa Anas Ibn Malik kuti iyeyu adati:[3]
قَنَتَ رَسُولُ اللَّهِ صلى الله عليه وسلم وَأَبُو بَكْرٍ، وَعُمَرُ، وَعُثْمَانُ، وَأَحْسَبُهُ وَرَابِعٌ حَتَّى فَارَقْتُهُمْ.
Adachita Qunūt Mtumiki wa Allāh (ﷺ), komanso Abū Bakr, ‘Umar ndi ‘Uthmān; ndipo ndikuganiza kuti adatinso: wachinayi (kunena ‘Alī) – adachita Qunūt mpaka ndidasiyana nawo.
Zokhudza Ismā’īl Ibn Muslim Al-Makkī tizipeza mu Tahdhīb At-Tahdhīb:[4]
قال أحمد بن حنبل: منكر الحديث. وقال ابن معين: ليس بشىء. وقال علي بن المديني: لا يكتب حديثه. وقال أبو حاتم: ضعيف الحديث مختلط، قلت له: هو أحب إليك أو عمرو بن عبيد؟ فقال: جميعا ضعيفان. وقال النسائي: متروك الحديث. وقال ابن حبان: ضعيف يروى المناكير عن المشاهير ويقلب الأسانيد.
Ahmad Ibn Hanbal adati: “Hadīth yake ndi munkar.” Ibn Ma’īn adati: “Iyeyu ndi wapanda pake.” Ndipo ‘Alī Ibn Madīnī adati: “Hadīth yake siikuyenera kulembedwa.” Abū Hātim adati: “Iyeyu ndi wofooka ndipo hadīth yake imakhala yosokonekera.” Ndidayankhula kwa iye (Abū Hātim) kuti: “Iyeyo (Ismā’īl Ibn Muslim) ndi wokondedwa kwa iwe kuposa ‘Amr Ibn ‘Ubayd?” Iye adati: “Onse awiriwa ndi ofooka.” An-Nasā’ī adati: “Hadīth yake ikuyenera kusiidwa.” Ibn Hibbān adati: “Iyeyu ndi wofooka ndipo amapereka ma ahādīth a munkar kuchokera kwa odziwika bwino pa ma ahādīth, ndipo amasakaniza ma isnād.”
Ndipo akakhala ‘Amr Ibn ‘Ubayd Al-Mu’tazilī, tipeza kuti:[5]
قال ابن معين: ليس بشيء. وقال عمرو بن علي: متروك الحديث، صاحب بدعة. وقال أبو حاتم: متروك الحديث. وقال النسائى: ليس بثقة، ولا يكتب حديثه. وقال أبو داود الطيالسي عن شعبة، عن يونس بن عبيد: كان عمرو بن عبيد يكذب فى الحديث. وقال حميد: لا تأخذ عن هذا شيئا فإنه يكذب على الحسن. وقال ابن عون: عمرو يكذب على الحسن.
Adayankhula Ibn Ma’īn kuti: “Iyeyu ndi wapanda ntchito.” Ndipo ‘Amr Ibn ‘Alī adati: “Iyeyu hadīth yake sikuyenera kutengedwa, adali munthu wa Bid’ah.” Ndipo Abū Hātim adati: “Hadīth yake ndi matrūk.” Ndipo An-Nasā’ī adati: “Iyeyu si wa mphamvu (qawiyy), musalembe hadīth yake.” Ndipo Abū Dāwūd At-Twayālisī, kuchokera kwa Shu’bah, yemwe adapereka uthengawu kuchokera kwa Yūnus Ibn ‘Amr, adati: “‘Amr Ibn ‘Ubayd adali wabodza mu (maphunziro a) hadīth.” Ndipo Humayd adati: “Musatenge chilichonse kuchokera kwa iye, chifukwa adali akumana pa Al-Hasan (kuti watenga ma ahādīth kwa iyeyo).”
Hadīth yomaliza:
Dīnār Ibn ‘Abdullāh, kapolo wa Anas Ibn Mālik, adafotokoza kuti Anas adati:
مَا زَالَ رَسُولُ اللَّهِ صلى الله عليه وسلم يَقْنُتُ فِي صَلَاةِ الصُّبْحِ حَتَّى مَاتَ.
Mtumiki wa Allāh (ﷺ) sadasiye kuchita Qunūt mu Swalāh ya Subh (Fajr) mpaka adamwalira.
Shaykh Al-Albānī adati mu A-Silsilah Adh-Dhwa’īfah:[6]
أخرجه الخطيب في "كتاب القنوت" له، وشنع عليه ابن الجوزي بسببه؛ لأن دينارا هذا قال ابن حبان فيه: " يروي عن أنس آثارا موضوعة لا يحل ذكرها في الكتب إلا على سبيل القدح فيه.
Hadīth imeneyi adaipereka ndi Al-Khatwīb mu buku lake la “Kitāb Al-Qunūt”, ndipo Ibn Al-Jawzī adamutsutsa iye kwambiri chifukwa cha hadīth imeneyi; chifukwa Ibn Hibban adati pa za Dinar: “Iyeyu amapereka ma ahādīth opeka potchula kuti wawatenga kwa Anas, omwe sali oyenera kuwatchula mu buku lake kupatula kungochita chionetsero kwa anthu zokhudza kufooka kwake.”
Choncho, ma ahādīth otchula za kuchita Qunūt pa swalāh iliyonse ya Fajr ndi ofooka kwambiri ndipo sakuyenera kugwiritsidwa ntchito ngati umboni.
Yomwe ili ya Swahīh (ya mphamvu) ndi imene Anas akufotokoza kuti:[7]
إِنَّمَا قَنَتَ رَسُولُ اللَّهِ صلى الله عليه وسلم بَعْدَ الرُّكُوعِ شَهْرًا ـ أُرَاهُ ـ كَانَ بَعَثَ قَوْمًا يُقَالُ لَهُمُ الْقُرَّاءُ زُهَاءَ سَبْعِينَ رَجُلاً إِلَى قَوْمٍ مِنَ الْمُشْرِكِينَ دُونَ أُولَئِكَ، وَكَانَ بَيْنَهُمْ وَبَيْنَ رَسُولِ اللَّهِ صلى الله عليه وسلم عَهْدٌ فَقَنَتَ رَسُولُ اللَّهِ صلى الله عليه وسلم شَهْرًا يَدْعُو عَلَيْهِمْ.
Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adachita Qunūt pambuyo poweramuka (Rukū’) kwa mwezi. Iyeyu adatumiza gulu (la ma Swahābah) lomwe limatchedwa Al-Qurrā’ (Owerenga Qur’ān) okwanira 70 kuti lipite kwa ma Mushrikūn omwe adali ocheperako mu kachulukidwe kawo poyerekeza iwo (ma Qurrā’). Ndipo pakati pawo ndi Mtumiki wa Allāh (ﷺ) padali mgwirizano wa mtendere (koma iwowo adawapha ma Qurrā’ aja). Choncho, Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adachita Qunūt kwa mwezi akuwapemphera (kwa Allāh) chilango pa iwowo.
Chomaliza, anthu akuyenera kuphunzitsidwa kuti azindikire za kulondola kapena kulakwika kwa hadīth. Ndi udindo wa omwe ali ndi uzindikiri kuwaunikira anthu ndi cholinga choti pakati pathu pasakhale kukokana.
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.
[1] ‘Abdur-Razzāq mu al-Muswannaf, Vol. 3, tsamba 110; Ad-Dāraqutni mu As-Sunan, Vol. 2, tsamba 39; Ibn Abī Shaybah mu al-Muswannaf, Vol. 2, tsamba 312; Al-Bazzār mu Kashf al-Astār, #556; Ahmad mu al-Musnad, Vol. 3, tsamba 162; At-Twahhāwi mu Sharh Ma’āni al-Athār, Vol. 1, tsamba 143; Al-Hākim mu al-Arba’īn; al-Bayhaqī mu As-Sunan, Vol. 2, tsamba 201.
[2] Tahdhīb At-Tahdhīb, Vol. 12, tsamba 57
[3] Sunan Ad-Dāraqutni, Vol. 2, tsamba 373, #1697; Sharh Ma’āni al-Athār, Vol. 1, tsamba 243; As-Sunan Al-Kubrā lil Bayhaqi, Vol. 2, 202.
[4] Tahdhīb At-Tahdhīb, Vol. 1, tsamba 332
[5] Tahdhīb At-Tahdhīb, Vol. 8, tsamba 62
[6] A-Silsilah Adh-Dhwa’īfah, Vol. 3, tsamba 386
[7] Swahīh Al-Bukhārī, #1002