Kodi kulela ndi kololedwa?

Download PDF

Lero ndi: Friday, Safar 6, 1447 1:19 AM | Omwe awerengapo: 70

Funso:

07 July, 2025

Ine ndi mkazi amene ndikufuna kudziwa zokhudza nkhani ya kulera mu Chisilamu.

Yankho:

Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
 
Chisilamu chimalimbikitsa mwamuna ndi mkazi kuti abereke ana ambiri ndipo asaope umphawi. Ngakhale zili choncho, palibe pamene panalembedwa kuti mkazi adzikhala ndi pathupi nthawi yomwe wabereka kumene pambuyo pomaliza nifās. Ndipo palibe pamene panalembedwa kuti ngati banja silibereka ana 20 lidzalandira chilango kuchokera kwa Allāh. Chomwe chili chodziwika ndi chakuti kukhala ndi ana ambiri kumabweretsa madalitso kwa makolo komanso ndi chinthu chimene chili mu zimene Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adalimbikitsa.
 
Kukhala ndi Ana Ambiri ndi Sunnah
 
Ibn Juyaj adafotokoza kuti:[1]
 
أن رجلاً أتى النبي صلى الله عليه وسلم فقال: يا رسول الله! إن لي ابنة عم هي همي من النساء وهي عاقرٌ. فقال رسول الله صلى الله عليه وسلم: لا تنكحها! ثم قال له: لأن تنكح سوداء ولوداً خيرٌ من أن تنكح حسناء لا تلد.
 
Mwamuna wina anafika kwa Mtumiki wa Allāh (ﷺ) ndipo adati: “Eh iwe Mtumiki wa Allāh (ﷺ)! Ine ndili ndi msuweni wanga (cousin) yemwe ndi wakhalidwe labwino koma ndi ‘Āqir (wosabereka).” Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati: “Usamukwatire.” Kenako adapitiriza nati: “Kukwatira mkazi wakuda thupi koma wobereka ndi zabwino kwambiri kusiyana ndi kukwatira mkazi woyera thupi koma wosabereka.”
 
Ndipo Ma'qil Ibn Yasār akufotokoza kuti:[2]
 
جَاءَ رَجُلٌ إِلَى النَّبِيِّ صلى الله عليه وسلم، فَقَالَ: إِنِّي أَصَبْتُ امْرَأَةً ذَاتَ حَسَبٍ وَجَمَالٍ وَإِنَّهَا لاَ تَلِدُ أَفَأَتَزَوَّجُهَا؟ قَالَ :لاَ‏.‏ ثُمَّ أَتَاهُ الثَّانِيَةَ فَنَهَاهُ، ثُمَّ أَتَاهُ الثَّالِثَةَ فَقَالَ: تَزَوَّجُوا الْوَدُودَ الْوَلُودَ فَإِنِّي مُكَاثِرٌ بِكُمُ الأُمَمَ.
 
Mwamuna wina adafika kwa Mtumiki wa Allāh (ﷺ) ndipo adati: “Ine ndapeza mkazi wochokera ku banja labwino ndipo iye ndi wokongola kwambiri koma ndi wosabereka: kodi ndimukwatire?” Mtumiki (ﷺ) adati: “Ayi (Usamukwatire).” Kenako mwamuna uja adabweranso kachiwiri ndipo adaletsedwanso. Kenako anabweranso kachitatu ndipo Mtumiki (ﷺ) adati: “Kwatira mkazi wachikondi komanso wobereka chifukwa ndidzawaposa anthu a mitundu ina ndi kuchuluka kwanu.”
 
Anas Ibn Mālik akutifotokozera kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[3]
 
تزوجوا الودود الولود من النساء فإني مكاثرٌ بكم النبيين يوم القيامة! وإياكم والعاقر فإن مثلها كمثل رجلٍ قاعدٍ على رأس بئرٍ [يسقي] أرضاً سبخةً فلا أرضه تنبت ولا عينه تنضب.
 
Kwatirani achikondi komanso obereka mu gulu la akazi; chifukwa ine ndidzanyadira pa atumiki ndi kuchuluka kwanu tsiku la Chiweruzo. Ndipo pewani kukwatira akazi omwe ali Āqir (osabereka), chifukwa (kukwatira) m’modzi wa iwo zili ngati mwamuna amene wakhazikika pamwamba pa chitsime, ndipo iyeyu namathirira munda wake tsiku lililonse, koma nthaka yakeyo yosalola kutulutsa zomera, ndipo madzi odutsa m’mundamo osalowa pansi.
 
'Abdullāh Ibn ‘Umar adati:[4]
 
حَصِيرٌ فِي بَيْتٍ، ‌خَيْرٌ ‌مِنَ ‌امْرَأَةٍ ‌لا ‌تَلِدُ.
 
Mphasa mnyumba (yomwe imagwiritsidwa ntchito pokhalira komanso kugonera) ndi yabwino kusiyana ndi mkazi yemwe sabereka.
 
Nayenso mkazi walimbikitsidwa kuti akwatiwe ndi mwamuna amene ali wobereka. Sizili zokondedwa kuti iye adzikwatitse kwa mwamuna amene ali gojo, kapena mwamuna amene salabadira zokhala ndi ana ochuluka chifukwa choopa umphawi. Muhammad Ibn Sīrīn akufotokoza kuti:[5]
 
أَنَّ عُمَرَ بْنَ الْخَطَّابِ، بَعَثَ رَجُلًا عَلَى بَعْضِ السِّعَايَةِ فَتَزَوَّجَ امْرَأَةً، وَكَانَ عَقِيمًا، فَلَمَّا قَدِمَ عَلَى عُمَرَ ذَكَرَ لَهُ ذَلِكَ، فَقَالَ: «هَلْ أَعْلَمْتَهَا أَنَّكَ عَقِيمٌ؟» قَالَ: لَا، قَالَ: «فَانْطَلِقْ فَأَعْلِمْهَا ثُمَّ خَيِّرْهَا».
 
‘Umar Ibnil Khattwāb adatumiza mwamuna wina kuti akatolere Zakāh, ndipo mu ulendowu, mwamunayu, adakwatira mkazi. Koma mwamunayu adali ‘aqīm (wosabereka). Pamene anabwerera mu ulendowu, iye anabweretsedwa kwa ‘Umar ndipo izi (zoti mwamunayu ndi wosabereka koma wakwatira) zidatchulidwa kwa iye. ‘Umar adati: “Kodi unamuuza mkaziyu kuti ndiwe wosabereka?” Iye adati: “Ayi.” ‘Umar adati: “Thetsa banja kenako umuuze (zoti ndiwe wosabereka), ndipo umupatse iyeyo chisankho (choti umukwatirenso kapena ayi)”
 
Ma ahādīth onsewa akulimbikitsa mwamuna kukwatira mkazi komanso mkazi kukwatiwana ndi mwamuna amene adziberekerana naye ana ochuluka. Choncho, sizoyenera kutenga maganizo a anthu amene amati kuchuluka kwa anthu kumabweretsa chiopsezo pa zinthu za padziko zomwe zili zosakwanira, chikhalirecho Allāh Mwini kuzindikira adapereka zokwanira pano pa dziko lapansi kwa akapolo Ake ndipo sizingapunguke chifukwa cha kuchulukana kwathu kumene adalimbikitsa Mtumiki (ﷺ).
 
Enanso amati kukhala ndi ana ochuluka ndi chipsinjo kwa mwamuna chifukwa sangakwanitse kudyetsa ana ambiri. Tizindikire kuti yemwe amadyetsa ana si mwamunayo. Allāh ndi Amene amadyetsa mwamunayo pamodzi ndi anawo.
 
Ma Swahābah Ankalera
 
Nkhani ya kulera ili ndi umboni mu Sharī’ah umene ukusonyeza kuti ndi yololedwa ngati zifukwa zopangirazo zili zovomerezeka.
 
Tikabwera mu nthawi ya Mtumiki wa Allāh (ﷺ), tipeza kuti ma Swahābah amalera ndipo panalibe chiletso chilichonse kuchokera kwa Allāh komanso Mtumiki Wake (ﷺ). Abū Sa’īd Al-Khudrī akunena kuti:[6]
 
سُئِلَ رَسُولُ اللهِ صَلَّى اللهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ عَنِ الْعَزْلِ؟ فَقَالَ: مَا مِنْ كُلِّ الْمَاءِ يَكُونُ الْوَلَدُ، وَإِذَا أَرَادَ اللهُ خَلْقَ شَيْءٍ لَمْ يَمْنَعْهُ شَيْءٌ.
 
Zidafunsidwa kwa Mtumiki wa Allāh (ﷺ) zokhudza ‘Azl ndipo iye adati: “Sikuti umuna onse umabweretsa mwana, koma kuti Allāh akafuna kulenga chinthu (mwana kudzera mwa mkazi), palibe amene angachipangitse kuti chisalengedwe.”
 
Liwu lakuti ‘Azl malinga ndi kufotokoza kwa Imām An-Nawawī adati:[7]
 
‌الْعَزْلُ ‌هُوَ ‌أَنْ ‌يُجَامِعَ ‌فَإِذَا ‌قَارَبَ ‌الْإِنْزَالَ ‌نَزَعَ وَأَنْزَلَ خَارِجَ الْفَرْجِ وَهُوَ مَكْرُوهٌ عِنْدَنَا فِي كُلِّ حَالٍ وَكُلِّ امْرَأَةٍ سَوَاءٌ رَضِيَتْ أَمْ لَا لِأَنَّهُ طَرِيقٌ إِلَى قَطْعِ النَّسْلِ وَلِهَذَا جَاءَ فِي الْحَدِيثِ الْآخَرِ تَسْمِيَتُهُ الْوَأْدَ الْخَفِيَّ لِأَنَّهُ قَطْعُ طَرِيقِ الْوِلَادَةِ كَمَا يُقْتَلُ الْمَوْلُودُ بِالْوَأْدِ وَأَمَّا التَّحْرِيمُ فَقَالَ أَصْحَابُنَا لَا يَحْرُمُ.
 
‘Azl ikutanthauza kuti, pamene mwamuna wayandikira kuthira, iye amatulutsa maliseche ake kwa mkazi ndi kuthirira panja pa maliseche a mkaziyo. Malingana ndi kuona kwathu, mchitidwe uwu ndi makrūh (wosakondedwa) mu nyengo zonse komanso kwa akazi onse, kaya mkaziyo wapereka chilolezo kapena ayi; chifukwa choti imeneyi ndi njira yopewa kukhala ndi ana. Ichi ndi chifukwa chake mu hadīth ina ikutchedwa, “mchitidwe wokwirira ana mwa chinsinsi,” chifukwa imatsekereza khomo lokhalira ndi ana, ngati momwe kulili kupha khanda ndi kulikwirira. Koma tikakamba za kuletsedwa kwa mchitidwewu, ma Swahābah athu adati si harām.
 
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.


[1] Adab An-Nisā’i li ‘Abdul-Mālik Ibn Habib, tsamba 152, #31


[2] Sunan Abī Dāwūd, #2050


[3] Adab An-Nisā’i li ‘Abdul-Mālik Ibn Habib, tsamba 152, #30


[4] Tārīkh Baghdād, Vol. 14, tsamba 353, #6782


[5] Sunan Sa’īd Ibn Mansūr, Vol. 2, tsamba 81, #2021


[6] Swahīh Muslim, #1438


[7] Al-Minhaj Sharh Swahīh Muslim, Vol. 10, tsamba 9

Funsoli lakuthandizani?