Zoyenera Kudziwa Musanasankhe Njira ya Kulera

Download PDF

Lero ndi: Thursday, Safar 5, 1447 7:18 AM | Omwe awerengapo: 60

Funso:

07 July, 2025

Kodi ndi zinthu ziti zimene zimapangitsa kuti kulera kukhale kovomerezeka kapena koletsedwa mu Chisilamumu?

Yankho:

Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
 
Pambuyo poti tafotokoza nkhani ya ‘Azl mu funso 26, njira zonse zimene munthu angasankhe pofuna kuti asapereke pathupi kwa mkazi wake ndi zololedwa, ndipo zilinso chimodzimodzi kwa mkaziyo kutenga njira zoti asakhalire ndi pathupi. Izi zili choncho chifukwa choti chilamulo (hukm) chololeza mwamuna kuchita ‘Azl ndi cholinga chopewa pathupi, chilinso mwa mkaziyo chifukwa wotenga pathupi ndi iyeyo.
 
Shaykh Ibn Bāz adagwiritsira ntchito hadīth ya Jābir ngati umboni wovomereza mwamuna ndi mkazi kusankha njira ya kulera ndi cholinga choti apereke mpata pakati pa ana awo (asabereke mowirikiza); ndipo iwo adati:[1]
 
إذا كانت المرأة لديها أولاد كثيرون، ويشق عليها أن تربيهم التربية الإسلامية لكثرتهم، فلا مانع من تعاطي ما ينظم الحمل لهذه المصلحة العظيمة، حتى يكون الحمل على وجه لا يضرها، ولا يضر أولادها، كما أباح الله العزل لهذه المصلحة وأشباهها.
 
Ngati mkazi ali ndi ana ochuluka, ndipo zili zovuta pa iyeyu kuwasamalira molingana ndi chisilamu chifukwa cha kuchuluka kwawo; palibe vuto kuti iyeyu apereke mpata pa kutenga pathupi msanga ndi cholinga choti akwaniritse ntchito yofunikirayi (kulera anako); izi zipangitsa kuti pathupipo pasapereke vuto kwa iyeyo kapena ana akewo, ndipo Allāh adaloleza ‘Azl pa chifukwa chimenechi ndi zifukwa zina zofananirako.
 
Shaykh Ibn ‘Uthaymīn adati:[2]
 
محاولة منع الحمل في الأصل جائزة؛ لأن الصحابة رضي الله عنهم كانوا يعزلون في عهد الرسول صلى الله عليه وسلم، ولم يُنْهَوْا عن ذلك، ولكن هي خلاف الأولى؛ لأن تكثير الأولاد أمرٌ مشروعٌ ومطلوب.
 
Tsinde ndi lakuti kutenga njira ya kulera ndi kololedwa, chifukwa ma Swahābah amachita ‘Azl mu nthawi ya Mtumiki wa Allāh (ﷺ); ndipo iyeyo sadawaletse kutero. Komabe (kulera) ndi kotsutsana ndi zomwe zili zokondedwa (kukhala ndi ana ambiri), chifukwa choti kukhala ndi ana ochuluka ndi chinthu chimene chakhazikitsidwa komanso ndi chokondedwa.
 
Khonsolo yoona za Fiqh (Majma’al Fiqh) idafotokoza kuti:[3]
 
يجوز التحكم المؤقت في الإنجاب بقصد المباعدة بين فترات الحمل، أو إيقافه لمدة معينة من الزمان، إذا دعت إليه حاجة معتبرة شرعا، بحسب تقدير الزوجين عن تشاور بينهما وتراض، بشرط أن لا يترتب على ذلك ضرر، وأن تكون الوسيلة مشروعة، وأن لا يكون فيها عدوان على حمل قائم.
 
Ndi zololedwa kugwiritsa ntchito njira zosakhalitsa (temporary) za kulera ndi cholinga chotalikitsa mipata yomwe mkazi angamatengere pathupi, kapena kuimikira kaye kutenga pathupi kwa kanthawi kochepa; komanso achite izi ngati pali chifukwa chomveka bwino pa Sharī’ah, ndipo pakhale kuwerengera (kuti mkazi ayembekezere miyezi ingati kuti adzayambenso kutenga pathupi) ndi mgwirizano wa awiriwa. Koma izi zichitidwe ngati sizibweretsa vuto lililonse ndipo njirayo ikhale yovomerezeka ndi Sharī’ah ndikutinso njirayo siiononga pathupi pamene palipo kale (ngati mkaziyo ali woyembekezera).
 
Pali zinthu zisanu izi zimene mwamuna ndi mkazi akuyenera kuyang’ana pa nkhani ya kulera:
 
1- Ngati chisankho chochedwetsera kukhala ndi ana chili chizolowezi chabe pakati pa anthu, ndipo mwamuna ndi mkazi akuchita izi pofuna kutsatira chikhamu cha anthuchi; ndiye kuti izi zikhala zinthu zosokoneza komanso zosemphana ndi Sharī’ah. Izi zili choncho chifukwa zaikidwa kukhala chinthu chimene chakhazikitsidwa ngati lamulo la tsopano pakati pa anthu; ndipo izi zibweretsa zotsatira zosakhala bwino (akazi kumafuna kusakhala ndi ana ambiri dala).
 
2- Ngati kuchedwetsa kukhala ndi anako kuli kuopa kuwadyetsa ndi kuwasamalira, apa zikhala zoopsa kwambiri chifukwa uku ndi kumukaikira Allāh kuti sangakwanitse kusamala akapolo Ake. Ndipo zoterezi zimasonyeza mantha a munthu pa zinthu zimene iyeyu alibe nazo uyang’aniri (zinthu zimene zili m’manja mwa Allāh Yekha basi). Apa, zikhala harām mwamuna ndi mkazi kutenga njira ya kulera.
 
3- Ngatinso chifukwa chochedwetsera kukhala ndi ana ambiri chikubwera kaamba ka mikangano pakati pa mwamuna ndi mkaziyo; mwachitsanzo mwamuna sakumupatsa mkazi chomwe akufuna ndipo mkaziyo wanyanyala ndi kuyamba kutenga njira ya kulera, izi zikhala zoletsedwa. Kapena mwamuna sakufuna ana ambiri chifukwa choti sakusangalatsidwa ndi mkaziyo, ndipo wamuuza mkaziyo kuti akatenge njira ya kulera; apanso zikhala zosaloledwa. Mwamuna kapena mkazi alibe ufulu womuletsa mnzake kusakhala ndi ana ochuluka.
 
4- Ngati chisankho cha awiriwa ndi chakuti akutenga kulera chifukwa chotsatira zikhalidwe za ma kuffār monga m’modzi wa iwowo ali pa ntchito yomwe sikumulora kukhala ndi ana ambiri; izinso zikhala zoletsedwa. Mkazi kugwira ntchito chisakhale chifukwa chomutsekerezera mwamuna ufulu wake wokhala ndi ana. Kapena mwamuna kumanamizira ntchito nkumamumana mkazi ufulu wokhala ndi pathupi kuti abereke. Alipo ena mwa akazi masiku ano omwe amamuuza mwamuna kuti ndi ntchito yangayi pakadali pano sindikufuna kutenganso pathupi. Izi mwamuna asavomereze chifukwa ntchito ya mkazi si chinthu chimene chikuyenera kukhala khomo lomutsekerezera iyeyo udindo umene Allāh adamupatsa (womwe uli kubereka, kulera ana ndi kusamala nyumba).
 
5- Ngati njira ya kulerayo ili kutseketsa; izi zikhala zinthu zomwe zili zosemphana ndi chilengedwe pokhapokha ngati pali vuto lomwe lapezeka pa mkaziyo (monga kukhala ndi ana ambiri ndipo pali chiopsezo choti akaberekanso atha kumwalira; kapena kuvulala fupa la mchiuono limene lingaonongeke chifukwa cha kutenga pathupi; kapena mkaziyo amachirira njira ya mpeni ndipo wabereka kokwanira kanayi). Ngati palibe zifukwa izi, zikhala harām mwamuna kapena mkazi kukatseketsa.
 
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.


[1] Fatāwā Nūr ‘ala Ad-Darb li Ibn Bāz, Vol. 21, tsamba 394


[2] Fatāwā Nūr ‘ala ad-Darb li Ibn ‘Uthaymīn, Vol. 22, tsamba 2


[3] Majallat al-Majma’, Vol. 1, tsamba 73

Funsoli lakuthandizani?