Zina mwa Zotsatira za Njira za Kulera

Download PDF

Lero ndi: Thursday, Safar 5, 1447 7:37 AM | Omwe awerengapo: 66

Funso:

08 July, 2025

Munafotokoza mu funso 26 ndi 27 zokhudza kulera ndipo zamveka bwino kwambiri komanso taphunzirapo. Koma ndimamva kuchokera kwa anthu osiyanasiyana kuti njira za kulera zili ndi zotsatira zina zoipa kwambiri ku thupi la munthu. Mungatambasuleko zina mwa zoipazi? Allaah akupatseni zabwino pa ntchito yomwe mukugwirayi potiunikira zokhudza Chisilamu.

Yankho:

Kutamandidwa konse ndi kwa Allaah!
 
Ndi zoonadi ndithu kuti pali zotsatira zambiri zimene zabwera m’matupi a anthu chifukwa cha njira za kulera. Zina mwa zomwe tauzidwa ndi akatswiri a za umoyo ndi izi:
 
1- Kuchepekera mphamvu kwa mwamuna: pamene mkazi akutenga njira za kulera, mwamuna akumakhala wofooka mu nthawi yogonana. Tidziwenso kuti si onse mwa amuna amene zingawachitikire izi. Ichi ndi chifukwa chake ena akumamwa mankhwala oti adzikhalitsa akamagonana ndi mkazi wawo.
 
2- Mkazi sakumakhala ndi chilakolako (decreased sexual drive): pamene mkazi wayamba kutenga njira za kulera – makamaka mapilisi kapena jakisoni – iye sakumakhala ndi chikhumbokhumbo choti agonane ndi mwamuna wake. Nthawi zinazo naye akumamwa mankhwala ena oti adzipatse chilakolako ndi cholinga choti agonane ndi mwamuna wake.
 
3- Kusatulutsa chikazi chambiri (vaginal dryness): ena mwa akazi amene amatulutsa chikazi chambiri asanayambe kumwa mapilisi kapena kutenga jakisoni wa kulera, iwo amayamba kutulutsa chikazi chochepa.
 
4- Mkazi kuonjezekera thupi: ena mwa akazi amayamba kunenepa chifukwa cha mapilisi kapena jakisoni.
 
5- Kutaya magazi kwambiri: izi zili zowanda pakati pa akazi amene amagwiritsa ntchito njira ya mapilisi komanso jakisoni nthawi yaitali.
 
6- Kuthamanga magazi kwambiri mwa akazi ena (elevated high blood pressure).
 
7- Zimatha kutenga mpaka chaka kuti mkazi abwerere mu chimake pambuyo poti wasiya kugwiritsa ntchito jakisoni wa kulera.
 
8- Kusinthasintha kwa machitidwe (mood swings): akazi ena amapezeka kuti akukhala a ukali mosadziwika bwino, ena kukhala odandaula nthawi zambiri, pomwe ena amakhala bwinobwino popanda kusintha kulikonse.
 
9- Kupweteka kwa mutu kwambiri (migraines): njira zina za kulera zimatha kuchepetsa kupweteka kwa mutu pomwe zina zimaonjezera. Kupweteka kwa mutuku kumatha kuchoka pakatha kanthawi, kapena kukhazikika ngati mkaziyo akugwiritsirabe njira ya kulera yomwe adasankhayo.
 
10- Kusintha kwa mawere: ena mwa akazi amakula mawere awo ndipo ena amamva kuwawa mu mawere awo.
 
11- Kupweteka mwa dzidzidzi ku msana.
 
Izi ndi zina mwa zotsatira za kutenga njira za kulera (kupatulapo ‘azl ndi kondomu). Pakufunika kupeza ulangizi wokwanira kuchokera kwa anamwino pamene mkazi wafuna kutenga njira ya kulera kudzera mu chilolezo cha mwamuna wake.
 
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.

Funsoli lakuthandizani?