Ndili ndi akazi awiri koma ndimalandira ndalama yochepa
Download PDFLero ndi: Thursday, Safar 5, 1447 7:20 AM | Omwe awerengapo: 46
Ndimalandila K180,000 pa mwezi; kodi kwa akazi awiri ndingaigawe bwanji ndalamayi? Nanga ngati ili yochepa, ndizotheka kusiya m’modzi mwa akaziwa?
Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
Mitala siinagone pa ndalama ngati momwe ena amayankhulira. Alipo anthu achuma omwe ali pa mitala koma samachita chilungamo. Ndipo alipo anthu omwe alibe chuma ndipo ali pa mitala koma amachita chilungamo. Choncho, mwamuna akwatire akazi angapo pokhapokha ngati akudziona kuti akwanitsa kuchita chilungamo. Ngati iye akuopa kuti saatha kukwanitsa, basi akhale ndi mkazi m’modzi.
Abū Hurayrah akufotokoza kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[1]
إِذَا كَانَ عِنْدَ الرَّجُلِ امْرَأَتَانِ فَلَمْ يَعْدِلْ بَيْنَهُمَا جَاءَ يَوْمَ القِيَامَةِ وَشِقُّهُ سَاقِطٌ.
Ngati mwamuna ali ndi akazi awiri ndipo sakuchita chilungamo pakati pa iwowo, adzabwera (mwamunayu) pa Tsiku la Chiweruzo mbali yake imodzi ya thupi lake itakhwefuka.
Mu kuyankhula kwake Allāh: “Ngati iye akuopa kuti sakwanitsa kuchita chilungamo, basi akwatire mkazi m’modzi (Sūrah An-Nisā’ 4:3),” Āyah imeneyi ikutiuza kuti chilungamo ndiye phata la mitala kuti ikhale yololedwa. Ngati mwamuna akuopa kuti sadzatha kukwanitsa kuchita chilungamo pakati pa akazi ake, ndi zoletsedwa pa iyeyo kukwatira akazi awiri, atatu kapena anayi.
Apa tikuona kuti kukwatira akazi awiri kapena atatu kapena anayi ndi chinthu chabwino pa yemwe ali wa chilungamo ndipo ali ndi zomuyenereza. Tikamakamba zomuyenereza tikutanthauza kuti mwamunayo akwanitsa kuwadyetsa akaziwo, kuwaveka, kuwapatsa malo ogona komanso kusamalira ana amene angabadwe mwa akaziwa. Ndipo munthu asaope nkhani ya ma rizq chifukwa zimenezi zili m’manja mwa Allāh.
Kuchita chilungamo sikukusonyeza kuwagulira zovala zofanana, kuwadyetsa mofanana kapenanso kuwaika mnyumba zofanana. Koma mwamuna aonetsetse kuti akazi onsewa sakukhala ndi njala ndipo akudya moyenerera, sakuyenda maliseche koma akuvala moyenerera, komanso akukhala mnyumba zoyenera malinga ndi mmene akaziwo alili.
Mwachitsanzo, mwamuna amene wabereka ana asanu ndi mkazi woyamba, kenako wakwatira mkazi wachiwiri yemwe alibe naye mwana (komanso mkaziyo sanaberekepo); maperekedwe a chakudya akhala osiyana ku ma anja awiriwa. Ngati iye angapereke mofanana, pamenepo wachita chinyengo.
Ngati mkazi woyamba amakonda kudya therere lobala, sizikutanthauza kuti mkazi wachiwiri umugulirenso therere lomwelo. Ichi si chilungamo chimene Allāh akunena mu Qur’ān komanso chimene Mtumiki Wake (ﷺ) adachichita kwa akazi ake.
Kumbali yowakonda mofanana si gawo la chilungamo chimene Allāh akunena. Iye akutambasula motere:[2]
وَلَنْ تَسْتَطِيعُوا أَنْ تَعْدِلُوا بَيْنَ النِّساءِ وَلَوْ حَرَصْتُمْ، فَلا تَمِيلُوا كُلَّ الْمَيْلِ فَتَذَرُوها كَالْمُعَلَّقَةِ.
Sudzakwanitsa kuchita chilungamo pakati pa akazi (kumbali ya mtima wako kuwakonda onse mofanana) ngakhale kuti iweyo utakhumba kuti utero. Choncho, usayedzamire kwa mkazi m’modzi ndi kumusiya winayo ngati wopanda mwamuna (kumusiya yekhayekha osamulabadira).
Imām Ash-Shāfi’ī adati:[3]
سَمِعْت بَعْضَ أَهْلِ الْعِلْمِ يَقُولُ قَوْلًا مَعْنَاهُ مَا أَصِفُ {وَلَنْ تَسْتَطِيعُوا أَنْ تَعْدِلُوا} إنَّمَا ذَلِكَ فِي الْقُلُوبِ.
Ndidamva m’modzi wa anthu ophunzira (chisilamu) akuyankhula pa tanthauzo la āyah yoti: “Sudzakwanitsa kuchita chilungamo,” kuti apa zikuimira nkhani za mu mtima (chikondi).
Mu ndemanga yake Ibn Kathīr adati:[4]
أَيْ: لَنْ تَسْتَطِيعُوا أَيُّهَا النَّاسُ أَنْ تُسَاوُوا بَيْنَ النِّسَاءِ مِنْ جميع الوجوه، فإنه وإن وقع الْقَسْمُ الصُّورِيُّ لَيْلَةً وَلَيْلَةً، فَلَا بُدَّ مِنَ التَّفَاوُتِ فِي الْمَحَبَّةِ وَالشَّهْوَةِ وَالْجِمَاعِ.
Kutanthauza kuti: Eh inu amuna, simudzakwanitsa kuchita chilungamo kwambiri pakati pa akazi anu mu gawo lililonse. Angakhale mwamuna atati wagawa usiku mofanana pakati pa akazi ake, padzakhalabe kusiyana kumbali ya chikondi, chilakolako komanso kugonana.
Mwamuna ku mbali ya zinthu zina, palibe vuto osawapangira chimodzimodzi. Monga wina atha kumugulira mphatso ndipo wina osamugulira. Kapena kumukonda kwambiri wina kusiyana ndi wina. Kapena kumagonana ndi wina kwambiri kusiyana ndi winayo (malinga ndi m’mene mkazi aliyense akufunira).
Akazi ambiri amaona ngati chilungamochi ndiye kuti mwamuna amukonde mkazi aliyense chimodzimodzi, ndipo adzigonana naye chimodzimodzi ndi mmene amagonanirana ndi mkazi winayo. Izi sizoona ndipo kumeneku ndi kutanthauzira āyah molakwika.
Akufotokoza Ibn Qudāmah kuti:[5]
قَالَ عَبِيدَةُ السَّلْمَانِيُّ فِي الْحُبِّ وَالْجِمَاعِ: وَإِنْ أَمْكَنَتْ التَّسْوِيَةُ بَيْنَهُمَا فِي الْجِمَاعِ، كَانَ أَحْسَنَ وَأَوْلَى؛ فَإِنَّهُ أَبْلُغُ فِي الْعَدْلِ. وَلَا تَجِبُ التَّسْوِيَةُ بَيْنَهُنَّ فِي الِاسْتِمْتَاعِ فِيمَا دُونَ الْفَرْجِ مِنَ الْقُبَلِ، وَاللَّمْسِ، وَنَحْوِهِمَا.
‘Abīdah As-Salmānī adati pa nkhani ya chikondi ndi kugonana: Ngati mwamuna akukwanitsa kugonana nawo akaziwo mofanana, zimenezo ndi zabwino kwambiri; chifukwa ndi zinthu zosonyeza chilungamo. Koma sizili zokondedwa kuti iyeyu awapange chimodzimodzi pa zinthu zomwe sizili zofunikira kwambiri kuposa kugonana monga kuchita mofanana powapsopsona, kuwasisita ndi zina zotero (chifukwa izi zimasiyana mwa mkazi aliyense).
Choncho, zomwe akazi ena amanena sizolondola ndipo uku kumakhala kufuna kumulimbitsira mwamuna zinthu zoti sakuyenera kuchita.
Alipo ena mwa akazi amene amafuna kuti mwamuna wawo adziyenda limodzi ndi akazi ake mofanana. Ngati wapita ku nyumba ya mkazi woyamba, ndipo kumeneko onse atengana ndi kupita ku msika, akuti akachitenso chimodzimodzi ku nyumba yachiwiri. Ngati sachita izi, pamenepo amati mwamunayo ndi wa chinyengo. Bwanji akuyenda kwambiri ndi mkazi woyamba kusiyana ndi ine; kapena ndi chifukwa chiyani amayenda kwambiri ndi mkazi wachiwiriyo akapita kwawo kusiyana ndi ine?
Ena amafuna kuti mwamuna agule zovala ngati wagulira zovala mkazi mnzawoyo. Kupanda kutero, pa khomo tsiku limenelo pavuta.
Pomaliza, sizili zokuyenerani inuyo kumusiya mkazi winayo chifukwa cha ndalama yomwe mumalandira. Ngatidi muli woopa Allāh, zindikirani kuti Allāh adzakupatsani ma rizq mu njira zomwe simumayembekezera. Koma mukaopa umphawi, ndiye kuti Allāh adzakusiyani muli pa mantha omwewo.
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.
[1] Sunan At-Tirmidhī, #1141 (hadīth swahīh)
[2] Sūrah An-Nisā’, 4:129
[3] Al-Umm, Vol. 5, tsamba 203
[4] Tafsīr Ibn Kathīr, Vol. 2, tsamba 381
[5] Al-Mughnī, Vol. 10, tsamba 245