Munthu unachekeredwa mankhwala a mwayi

Download PDF

Lero ndi: Thursday, Safar 5, 1447 7:37 AM | Omwe awerengapo: 57

Funso:

11 July, 2025

Kodi munthu ngati unatemera mankhwala oti udzikhala ndi mwayi mu nthawi ya umbuli usanazindikire za kuti ndi shirk, ndiye pambuyo pozindikira tawbah yake ungatani?

Yankho:

Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
 
Choyamba, munthu azindikire kuti asing’anga onse alibe ntchito ndipo sangathandize aliyense mu njira ina iliyonse ndipo sangabweretse vuto kwa aliyense. Allāh akuyankhula kuti:[1]
 
قُلْ أَتَعْبُدُونَ مِن دُونِ اللَّهِ مَا لَا يَمْلِكُ لَكُمْ ضَرًّا وَلَا نَفْعًا
 
Nena (E iwe Muhammad), “Kodi mukupembedza posakhala Allāh omwe alibe mphamvu pa inu zokubweretserani vuto ngakhalenso phindu?”
 
Mu kuyankhula kwina, Allāh adati:[2]
 
وَلَئِن سَأَلْتَهُم مَّنْ خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ لَيَقُولُنَّ اللَّهُۚ قُلْ أَفَرَءَيْتُم مَّا تَدْعُونَ مِن دُونِ اللَّهِ إِنْ أَرَادَنِىَ اللَّهُ بِضُرٍّ هَلْ هُنَّ كَاشِفَاتُ ضُرِّهِۦٓ أَوْ أَرَادَنِى بِرَحْمَةٍ هَلْ هُنَّ مُمْسِكَاتُ رَحْمَتِهِۦۚ قُلْ حَسْبِىَ اللَّهُۖ عَلَيْهِ يَتَوَكَّلُ الْمُتَوَكِّلُونَ.
 
Ndipo ukawafunsa iwowo kuti, "Kodi ndi ndani amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi?" iwo adzakuyankha kuti ndi, "Allāh." Nena, "Kodi tsopano mumalingalira zomwe mumapembedza posakhala Allāh? Ngati Allāh wafuna pa ine vuto (kuti lindigwere), alipo amene angachotse vuto Lakeli? Kapena ngati Iye wafuna pa ine mtendere, alipo amene angauletse mtendere Wakewu (kuti usandifikire)?" Nena, "Wandikwanire ine Allāh; pa Iye [Yekha] adalire odalira."
 
Akuyankhulanso Allāh kuti:[3]
 
أَمَّن يُجِيبُ الْمُضْطَرَّ إِذَا دَعَاهُ وَيَكْشِفُ السُّوٓءَ وَيَجْعَلُكُمْ خُلَفَآءَ الْأَرْضِۗ أَءِلٰهٌ مَّعَ اللَّهِۚ قَلِيلًا مَّا تَذَكَّرُونَ.
 
Kodi si Iye (Allāh) amene amayankha yemwe wasimidwa pamene wapanga du’ā komanso amachotsa choipa ndipo amakupangani inu kukhala oliyang’anira dzikoli? Kodi palinso mulungu wina pambali pa Allāh? Pang’ono pokha ndi pomwe mumakumbukira.
 
Adayankhula 'Ā’ishah kuti:[4]
 
سَأَلَ أُنَاسٌ النَّبِيَّ صلى الله عليه وسلم عَنِ الْكُهَّانِ، فَقَالَ: ‏إِنَّهُمْ لَيْسُوا بِشَىْءٍ. ‏‏‏ فَقَالُوا: يَا رَسُولَ اللَّهِ! فَإِنَّهُمْ يُحَدِّثُونَ بِالشَّىْءِ يَكُونُ حَقًّا‏.‏ قَالَ فَقَالَ النَّبِيُّ صلى الله عليه وسلم:‏ تِلْكَ الْكَلِمَةُ مِنَ الْحَقِّ يَخْطَفُهَا الْجِنِّيُّ فَيُقَرْقِرُهَا فِي أُذُنِ وَلِيِّهِ كَقَرْقَرَةِ الدَّجَاجَةِ، فَيَخْلِطُونَ فِيهِ أَكْثَرَ مِنْ مِائَةِ كَذْبَةٍ.
 
Anthu ena adamufunsa Mtumiki wa Allāh (ﷺ) zokhudza aloseri (abimbi, asing’anga ngakhale abusa olosera), ndipo iye adati: "Alibe ntchito amenewo." Iwo (ma Swahābah) adati: "O iwe Mtumiki wa Allāh (ﷺ)! Zokamba zawo zina zimabweradi mu choonadi." Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati: "Liwu limene limakhaladi la choonadilo (kuchokera mu zokamba zawo) ndi lomwe Jinn loipa limalitenga mwa kuba (kuchokera kumwamba pamene angelo akukambirana) ndipo (Jinn limeneli) limalithira liwuli m’makutu a bwenzi lake (yemwe ali mloseriyo) kudzera mu kamvekedwe ka thazi (pamene Jinn likumuuza munthuyo limamveka ngati nkhuku yaikazi). Kenako mloseriyu amasakaniza ku liwuli bodza lokwanira zana limodzi (100)."
 
Izi ndi chisonyezo choti asing’anga sadziwa za kutsogolo ndipo ma Jinn amene amalumikizana nawowo za kutsogolo samazidziwa. Ndipo asing’anga alibe mphamvu zobweretsa vuto kwa munthu ngakhalenso kupereka phindu kwa munthu, kupatulapo kudzera mu chilolezo cha Allāh. Yemwe amabweretsa vuto kapena phindu kwa anthu ndi ziwanda ndi Allāh Yekha basi.
 
Chachiwiri, munthu amene wanamizidwa ndi asing’anga kuti achekeredwe mankhwala a mwayi kapena mangolomera, kapena achikondi ngakhalenso mankhwala ena alionsewo; iyeyu alape kwa Allāh kulapa kwenikweni. Chifukwa amakhala kuti watuluka mu chisilamu potengera hadīth ya Imran Ibn Huswayn yomwe Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adayankhulamo kuti:[5]
 
 لَيْسَ مِنَّا مَنْ تَطَيَّرَ أَوْ تُطُيِّرَ لَهُ؛ أَوْ تَكَهَّنَ أَوْ تُكُهِّنَ لَهُ؛ أَوْ سَحَرَ أَوْ سُحِرَ لَهُ.
 
Sali mwa ife yemwe amachita Tatwayyar[6] kapena kuchitiridwa Tatwayyar; kapena amachita maula kapena kuchitiridwa maula; kapena kuchita ufiti kapena kuchitiridwa ufiti (kukautenga ufiti kwa omwe amauchitawo).
 
Pambuyo polapa, sakuyeneranso kubwerera kwa asing’angawo kuti akamuchotse zomwe anamuchekerazo. Allāh ndi Yemwe ali ndi mphamvu yochotsa zimenezo ndipo Iyeyo ndi Wakutha.
 
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.


[1] Sūrah Al-Mā’dah 5:76


[2] Sūrah Az-Zumar 39:38


[3] Sūrah An-Naml 27:62


[4] Swahīh Al-Bukhārī, #7561


[5] Musnad al-Bazzār, #3578 (Swahīh li ghayrihi – Silsilat As-Swahīhah, #2195)


[6] Tatwayyar ndi mchitidwe wokhulupirira kuti mbalame zimabweretsa mwayi kapena tsoka

Funsoli lakuthandizani?