Makolo anga akuti ndidzitolere kaye panopa sindili wokonzeka kukwatira
Download PDFLero ndi: Thursday, Safar 5, 1447 7:30 AM | Omwe awerengapo: 225
As-Salam alaikum warahmatu llahi wabarakatu. Kodi mnyamata watha msinkhu ndipo ali wokonzeka kuti akhonza kumusamala mkazi. Iyeyu wawauza makolo ake mwa ubwno koma amukaniza akuti azitolere kaye zina ndi zina komanso katundu wa mnyumba. Kodi pamenepo munthu kupanga wekha ngakhale kholo lakaniza pa chislamu si mwano kwa makolo?
Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
Ukwati sichinakhalepo chinthu chotsekereza munthu kuti akwaniritse zokhumba zake, koma m’malo mwake ndi chinthu chomwe chimamuthandizanso iyeyo kuti zokhumba zake zija azikwaniritse mosavuta kudzera mu thandizo la Allāh. Shaytwān ndi amene amawanong’oneza anthu kuti asachite kaye nikāh asanakwaniritse zomwe iwowo akuziona kuti ndi zabwino ndipo m’malo mwake, iyeyu (Shaytwān) amawaitanira ku njira yoipa imene imawagwetsera ambiri mu uchimo. Mutha kuona kuti izi ndi zomwe zachuluka masiku ano pamene mwamuna akuchedwetsa ukwati, kapena makolo kuwaletsa ana awo kuti asakwatire kapena kukwatiwa asanamalize sukulu, kapena asanapeze ntchito; ndipo izi zabweretsa masautso pa achinyamata amene ngakhale achedwetsedwa choncho, zokhumba zawozo sizimakwaniritsidwabe.
Anthu ambiri amayesa kuti nikāh imafunikira kukonzekera mokwanira pokhala ndi katundu wambiri komanso chuma. Izi sizoona. Rabī’ Ibn Ka’b adafotokoza kuti:[1]
كُنْتُ أَخْدُمُ النَّبِيَّ صلى الله عليه وسلم، فَقَالَ ذَاتَ يَوْمٍ: يَا رَبِيعَةُ، أَلَا تَتَزَوَّجُ؟، قَالَ: قُلْتُ: يَا رَسُولَ اللهِ، وَاللهِ مَا عِنْدِي مَا يُقِيمُ امْرَأَةً، وَمَا أُحِبُّ أَنْ يَشْغَلَنِي عَنْ خِدْمَتِكَ شَيْءٌ. ثُمَّ قَالَ لِي يَوْمًا آخَرَ: يَا رَبِيعَةُ، أَلَا تَتَزَوَّجُ؟، فَقُلْتُ لَهُ مِثْلَ ذَلِكَ، قَالَ: ثُمَّ قُلْتُ فِي نَفْسِي: وَاللهِ لَرَسُولُ اللهِ أَعْلَمُ بِمَا يُصْلِحُنِي مِنْ أَمْرِ دُنْيَايَ وَآخِرَتِي مِنِّي، وَاللهِ لَئِنْ قَالَ لِي رَسُولُ اللهِ صلى الله عليه وسلم الثَّالِثَةَ لَأَقُولَنَّ نَعَمْ، فَقَالَ لِيَ الثَّالِثَةَ: يَا رَبِيعَةُ، أَلَا تَزَوَّجُ؟، قَالَ: قُلْتُ: لِيَصْنَعْ رَسُولُ اللهِ مَا شَاءَ، فَقَالَ: انْطَلِقْ إِلَى آلِ فُلَانٍ - نَاسٌ مِنَ الْأَنْصَارِ - فَقُلْ: رَسُولُ اللهِ أَرْسَلَنِي يُقْرِئُ السَّلَامَ وَيَأْمُرُكُمْ أَنْ تُزَوِّجُونِي فُلَانَةً، فَأَتَيْتُهُمْ فَقُلْتُ: إِنَّ رَسُولَ اللهِ صلى الله عليه وسلم يَأْمُرُكُمْ أَنْ تُزَوِّجُونِي فُلَانَةً. فَقَالُوا: مَرْحَبًا بِرَسُولِ اللهِ وَبِرَسُولِ رَسُولِ اللهِ، وَاللهِ لَا يَرْجِعُ رَسُولُ رَسُولِ اللهِ الْيَوْمَ إِلَّا بِحَاجَتِهِ. قَالَ: فَزَوَّجُونِي وَأَكْرَمُونِي.
Ndidali womuthandiza Mtumiki wa Allāh (ﷺ) ndipo tsiku lina adati: “Eh iwe Rabī’! Kodi sungakwatire?” Ine ndidati: ‘Eh iwe Mtumiki wa Allāh (ﷺ)! Ndikulumbira mwa Allāh, ine ndilibe zondiyenereza kuti ndisamalire mkazi komanso sindikukonda kuti china chilichonse chinditangwanitse mu kukusamalira iwe.’ Kenako adandiyankhulanso tsiku lina kuti: “Eh iwe Rabī’! Kodi sungakwatire?” Choncho ndidamuyankha zofanana ndi zimene ndidayankha tsiku loyambalo. Kenako pambuyo pake ndidalingalira mu mtima kuti: ‘Ndikulumbira mwa Allāh kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) ndi wodziwa bwino zomwe zili zabwino ku umoyo wanga wa padziko pano komanso ku Ākhirah kuposa mwini wakene. Ndikulumbira mwa Allāh! Ngati angandiyankhulenso ine Mtumiki wa Allāh (ﷺ) kachitatu, ndidzamuyankha kuti eya.’ Choncho adandiyankhulanso kachitatu kuti: “Eh iwe Rabī’! Kodi sungakwatire?” Ine ndidati: ‘Amachita Mtumiki wa Allāh (ﷺ) chomwe wafuna (kutanthauza kuti zomwe Mtumiki wa Allāh (ﷺ) amalangiza apa zinali zabwino).’ Apa Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati: “Pita ku banja lakuti-lakuti la anthu achi Answārī ndipo ukayankhule (kwa iwowo) kuti: ‘Mtumiki wa Allāh (ﷺ) wanditumiza ine ndipo akukupatsani As-Salām ndipo akukulamulani inu kuti mundikwatitse kwa mkazi wakuti uja.” Iwo adati: ‘Walandiridwa Mtumiki wa Allāh (ﷺ) komanso mtumiki wa Mtumiki wa Allāh (ﷺ). Tikulumbira mwa Allāh kuti sangabwerere mtumiki wa Mtumiki Allāh (ﷺ) tsiku la lero kupatula zokhumba zake zikwaniritsidwe.’ Rabī’ adati: “Choncho adandikwatitsa ndi kundilemekeza.”
Mu hadīth imeneyi tikuphunziramo kuti pamene munthu akuopa kuti akwatire chifukwa cha kupereweredwa, iyeyu aganizire za Allāh Yemwe ali wosamalira akapolo Ake. ‘Abdullāh Ibn Mas’ūd adati:[2]
الْتَمِسُوا الْغِنَى فِي النِّكَاحِ.
“Funanifunani kulemera kudzera mu ukwati.”
Umar Ibnil Khattwāb adati:[2]
عَجَبِي مِمَّنْ لَا يَطْلُبُ الْغِنَى فِي النِّكَاحِ، وَقَدْ قَالَ اللَّهُ تَعَالَى: إِنْ يَكُونُوا فُقَراءَ يُغْنِهِمُ اللَّهُ مِنْ فَضْلِهِ.
Amandidabwitsa yemwe safunafuna kulemera kudzera mu ukwati, chikhalirecho Allāh adati: “Ngati ali osauka, Allāh adzawalemeretsa kuchokera mu chuma Chake.”
Mu kuyankhula kwina, ‘Abdullāh Ibn Mas’ūd adati:[3]
لَوْ لَمْ يَبْقَ مِنْ أَجْلِي إِلاّ عَشَرَةُ أَيَّامٍ وَأَعْلَمُ أَنِّي أَمُوتُ فِي آخِرِهَا يَوْمًا وَلِي طَوْل النِّكَاحِ فِيهِنَّ لَتَزَوَّجْتُ مَخَافَةَ الْفِتْنَةِ.
“Nditati ndatsala ndi masiku khumi mu umoyo wanga, ndipo ndikudziwa kuti pamapeto pa masikuwa ndimwalira, ndipo ndinali ndi kuthekera kuti nditha kukwatira, ndikanakwatira poopa mayesero.”
Uku kudali kumva kwa ma Swahābah pa nkhani ya ukwati. Tsopano lero makolo akuwatsekereza ana kuti asakwatire msanga chifukwa chowaopera umphawi?
Inu akhī kwatirani ndipo makolo anuwo simuwanyoza mukapanga zimenezi. Zindikiraninso izi: 'Ā’ishah akufotokoza kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[4]
مَنِ الْتَمَسَ رِضَاءَ اللَّهِ بِسَخَطِ النَّاسِ كَفَاهُ اللَّهُ مُؤْنَةَ النَّاسِ وَمَنِ الْتَمَسَ رِضَاءَ النَّاسِ بِسَخَطِ اللَّهِ وَكَلَهُ اللَّهُ إِلَى النَّاسِ.
Aliyense amene wapata chisangalalo cha Allāh kudzera mu kuwakwiitsa anthu, Allāh adzamukwanira ku zomwe anthu angamukonzere. Ndipo yemwe wapata chisangalalo cha anthu kudzera mu kumukwiyitsa Allāh, Allāh adzamusiira chilichonse kwa anthuwo.
Pangani zosangalatsa Allāh osati makolo anu amene akutsutsana ndi zomwe Allāh adalamula.
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.
[1] Musnad Abī Dāwūd At-Twayālisī, #1269
[2] Tafsīr Al-Qurtwubī, Vol. 12, tsamba 241; komanso Tafsīr Ibn Kathīr, Vol. 6, tsamba 51
[3] Al-Mawsū’al Fiqhiyyah Al-Kawniyyah, Vol. 41, tsamba 214
[4] Sunan At-Tirmidhī, #2414