Tingasiyanitse bwanji pakati pa Qadar ndi chisankho chathu (free will).

Download PDF

Lero ndi: Thursday, Safar 5, 1447 7:23 AM | Omwe awerengapo: 89

Funso:

12 July, 2025

As-salam alaykum wa rahamatullah wa barakatuh. Kodi timati Allāh anatipatsa free will komanso timati zinthu zomwe zimatichitikira ndi Qadari; kodi tingasiyanitse bwanji?

Yankho:

Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
 
Ndi zoona ndithu kuti anthu ali ndi chisankho chochita zomwe akufuna. Ndipo Allāh adaloleza zimenezi pa aliyense mwa ife kuti akhale ndi chisankho. Zikadati sizili choncho, kuti anthu alibe kuthekera kusankha, ndiye kuti aliyense kuchokera mwa omwe adalandira atumiki akadayankhula pa Tsiku la Chiweruzo kuti: “Tinalibe chisankho pa nkhani imeneyi – tidakana chifukwa ndi zomwe mudatilembera.”
 
Choncho, anthu ali ndi chisankho ngati m’mene Allāh akuyankhulira mu ma āyāt ambiri monga:[1]
 
وَقُلِ ٱلْحَقُّ مِن رَّبِّكُمْۖ فَمَن شَآءَ فَلْيُؤْمِن وَمَن شَآءَ فَلْيَكْفُرْۚ إِنَّآ أَعْتَدْنَا لِلظَّٰلِمِينَ نَارًا أَحَاطَ بِهِمْ سُرَادِقُهَا
 
Ndipo nena: "Chilungamo ndi chochokera kwa Mbuye wanu, choncho yemwe akufuna – akhulupirire; ndipo yemwe akufuna – akanire." Ndithudi, Tawakonzera onse ochita zoipa Moto womwe makoma ake adzawazungulire iwowo.
 
Izinso ndi zomwe opembedza mafano amayankhula mu nthawi ya Mtumiki wa Allāh (ﷺ). Allāh akutiuza motere:[2]
 
وَقَالَ الَّذِينَ أَشْرَكُوا۟ لَوْ شَآءَ اللَّهُ مَا عَبَدْنَا مِن دُونِهِۦ مِن شَىْءٍ نَّحْنُ وَلَآ ءَابَآؤُنَا وَلَا حَرَّمْنَا مِن دُونِهِۦ مِن شَىْءٍۚ كَذٰلِكَ فَعَلَ الَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْۚ فَهَلْ عَلَى الرُّسُلِ إِلَّا الْبَلَاغُ الْمُبِينُ
 
Ndipo omwe amamuphatikizira Allāh ndi mafano amati, "Allāh akadafuna, sitikadapembedza milungu ena posakhala Iyeyo, ife ngakhalenso makolo athu. Ndipo sitikadaletsa chilichonse kupatulapo kudzera mwa Iye." Umotu ndi m’menenso adachitira omwe adadza m’mbuyo mwawo. Choncho, palinso pa atumiki ntchito ina kupatulapo kugawa uthenga mosabisa?
 
Pa āyah imeneyi, Ibn Kathīr adati:[3]
 
وَمَضْمُونُ كَلَامِهِمْ ‌أَنَّهُ ‌لَوْ ‌كَانَ ‌تَعَالَى ‌كَارِهًا ‌لما ‌فعلنا ‌لأنكره ‌علينا ‌بالعقوبة ولما أمكننا منه، قال تعالى رَادًّا عَلَيْهِمْ شُبْهَتَهُمْ: {فَهَلْ عَلَى الرُّسُلِ إِلَاّ الْبَلَاغُ الْمُبِينُ} أَيْ لَيْسَ الْأَمْرُ كَمَا تَزْعُمُونَ أنه لم ينكره عليكم، بَلْ قَدْ أَنْكَرَهُ عَلَيْكُمْ أَشَدَّ الْإِنْكَارِ وَنَهَاكُمْ عَنْهُ آكَدَ النَّهْيِ، وَبَعَثَ فِي كُلِّ أُمَّةٍ في كل قرن وطائفة من الناس رسولاً، فَلَمْ يَزَلْ تَعَالَى يُرْسِلُ إِلَى النَّاسِ الرُّسُلَ بِذَلِكَ مُنْذُ حَدَثَ الشِّرْكُ فِي بَنِي آدَمَ فِي قَوْمِ نُوحٍ الَّذِينَ أُرْسِلَ إِلَيْهِمْ نُوحٌ، وَكَانَ أَوَّلَ رَسُولٍ بَعَثَهُ اللَّهُ إِلَى أَهْلِ الْأَرْضِ، إِلَى أَنْ خَتَمَهُمْ بِمُحَمَّدٍ صلى الله عليه وسلم الَّذِي طَبَّقَتْ دَعْوَتُهُ الْإِنْسَ وَالْجِنَّ في المشارق والمغارب.
 
Tsinde la mawu awo linali loti: “Akanati Allāh akunyasidwa ndi zomwe timachitazi (zopembedza mafanozi), akadatiimitsa potipatsa chilango, ndipo sakadatipatsa kuthekera koichita ntchito imeneyi (yopembedza mafanoyi).” Potsutsa zoyankhula zawozi, Allāh adati: “Choncho, palinso pa atumiki ntchito ina kupatulapo kugawa uthenga mosabisa?” kutanthauza kuti, nkhani siili m’mene inuyo mukuyankhulira. Sikuti Allāh sanakutsutseni mchitidwe wanu; koma Iye adakuletsani kale, mu chiletso chokhwima kwambiri. Ndipo adatsindika za chiletso chimenechi pa inu. Ku Ummah ulionse – m’badwo ulionse, gulu lililonse la anthu – adatumizako Mtumiki wa Allāh (ﷺ). Allāh sadasiye kubweretsa kwa anthu atumiki pa chifukwa chimenechi (chaletsa Shirk) kuyambira pamene adaipanga Shirk kukhala Hadath (choononga ntchito za munthu) pa Ana a Adam mu m’badwo wa Nuh omwe adatumiziridwa Nuh. Ndipo Nuh adali woyambirira mwa atumiki amenewa kutumizidwa ndi Allāh kwa anthu a pa dziko lapansi, mpaka kufikira pa womalizira mwa iwo yemwe ndi Muhammad, yemwe da’wah yake idali yopita kwa anthu ndi ziwanda zomwe, kuyambira ku mmawa mpaka kufikira ku madzulo.
 
Apapa tikuona kuti sizoona zoti munthu alibe kusankha. Aliyense adapatsidwa kusankha kochivomereza chilungamo kapena kuchikana.
 
Chimodzimodzinso yemwe wasankha kuvomereza chilungamo, ameneyo wachita zimenezo mwa kufuna kwake. Ndipo ngati munthu wasankha kuchita tchimo, ameneyo wachita zimenezo mwa kufuna kwake.  Adayankhulapo za nkhaniyi Shaykhul Islām Ibn Taymiyyah kuti:[4]
 
و‌‌ليس لأحد أن يحتج بالقدر على الذنب باتفاق المسلمين وسائر أهل الملل وسائر العقلاء؛ فإن هذا لو كان مقبولا لأمكن كل أحد أن يفعل ما يخطر له من قتل النفوس وأخذ الأموال وسائر أنواع الفساد في الأرض ويحتج بالقدر. ونفس المحتج بالقدر إذا اعتدي عليه واحتج المعتدي بالقدر لم يقبل منه بل يتناقض وتناقض القول يدل على فساده؛ فالاحتجاج بالقدر معلوم الفساد في بداية العقول.
 
Ndipo sizili pa aliyense kuti adzigwiritsira ntchito Al-Qadar kukhala umboni wochimwira potengera mgwirizano wa asilamu (ma ‘ulamā’), komanso ndi ena onse otsatira zipembedzo zina, ngakhalenso ndi omwe ali ndi nzeru. Zikanati izizi ndi zovomerezeka, ndiye kuti aliyense akamachita zomwe zamudzera mmutu mwake kumbali ya kupha, kulanda chuma cha anthu, ndi ntchito zina zobweretsa chisokonezo pa dziko, ndipo akanalozera Al-Qadar ngati pothawira pake. Ngati munthu amene akunamizira Al-Qadar atati afikiridwe ndi munthu wina mosakhala bwino (kaya kumenyedwa) ndipo winayonso akunamizira Al-Qadar pa zomwe wachitazo, iyeyu sakadavomereza zimenezo; ndipo pamenepa akadakhalanso akudzitsutsa yekha, zomwe zikutitsimikizira kuti kaganizidwe kameneka ndi kabodza. Choncho, kugwiritsira ntchito Al-Qadar ngati chida (chochitira zoipa zathu) ndi bodza kwa munthu amene ali kaganizidwe kolondola.
 
Shaykh Muhammad Ibn Swālih Al-‘Uthaymīn adatchulapo za nkhani ya wakuba mu ulamuliro wa ‘Umar Ibnil Khattwāb kuti:[5]
 
ولمَّا أَمَرَ عُمرُ بْنُ الخطَّابِ رضي الله عنه أَنْ تُقطَعَ يَدُ السَّارِقِ قَال: ‌مَهْلًا ‌يَا ‌أمِيرَ ‌المُؤمِنِينَ، واللهِ ‌مَا ‌سرَقْتُ ‌إلَّا ‌بقَدَرِ اللهِ. قَال: ونحْنُ لَا نَقْطَعُ يَدَكَ إلا بقَدَرِ اللهِ.
 
Ndi pamene adalamula ‘Umar Ibnul Khattwāb (chisangalalo cha Allāh chikhale pa iye) kuti lidulidwe dzanja la wakuba, iye (wakubayo) adati: “Dikirani kaye, eh inu mtsogoleri wa Okhulupirira! Ndikulumbira mwa Allāh, ine sindinabe kupatulapo kudzera mu Qadar ya Allāh.” ‘Umar adati: “Ndipo ife sitikudula dzanja lako kupatula kudzera mu Qadar ya Allāh.”
 
Choncho, Allāh amachita zomwe Iyeyo wafuna; ndipo ife pambuyo poti tasankha zomwe tikufuna kuchitazo, Iyeyo (Allāh) ndi amene amapereka chilolezo kuti zimenezo zitheke.
 
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.


[1] Sūrah Al-Kahf 18:29


[2] Sūrah An-Nahl 16:35


[3] Tafsīr Ibn Kathīr, Vol. 4, tsamba 680


[4] Majmū’ Al-Fatāwā, Vol. 8, tsamba 179


[5] Tafsīr Al-‘Uthaymīn, Sūrah Az-Zukhruf, tsamba 94

Funsoli lakuthandizani?