Kuyamwa maliseche a mwamuna wako

Download PDF

Lero ndi: Thursday, Rabi' Al-Awwal 25, 1447 5:29 AM | Omwe awerengapo: 1051

Funso:

14 September, 2025

Kodi chisilamu chikuti bwanji pa nkhani ya kuyamwa maliseche a mwamuna wako?

Yankho:

Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
 
Tizindikire kuti chilichonse pa mkazi ndi chololedwa kupatulapo haydhw (magazi amene amatuluka mu nthawi yomwe iye ali pa masiku ake), kapena nifās (magazi amene amatuluka pamene iye wabereka kumene), njira yotulukira chimbudzi, kugonana naye pamene muli mu ihrām (mukuchita mapemphero a Hajj kapena ‘Umrah), kapena mu nthawi ya kusala.
 
Pa chifukwa choti nkhani yokhudza kunyambitana maliseche siikupezeka mu Qur'ān komanso mu Sunnah, ma ulamā’ adagawanikana mu magulu atatu:
 
a)     Gulu loyamba limafotokoza kuti; ndizoletsedwa kuika maliseche mkamwa chifukwa kamwa ndi chiwalo chowerengera Qur'ān, kuchitira dhikr komanso kudyera chakudya ndi kumwera chakumwa. Choncho, sizili zololedwa kuti mwamuna amupemphe mkazi wake kuti aike maliseche ake mkamwa, kapena mkazi kumupempha mwamuna wake kuti anyambite maliseche ake kapena kulowetsa lilime mkati mwa maliseche ake. Gawo ili si lolondola chifukwa palibe umboni womwe ukuletsa.
 
Ndidawamva Shaykh As-Suhaymī pamene adafunsidwa zokhudza kuchita banja ndi mkazi kudzera pa kamwa lake komanso ndi kotulukira chimbudzi akuyankha kuti: “Ikakhala nkhani yokhudza kuchita banja ndi mkazi kudzera malo ochitira chimbudzi, izo ndi zodziwika kuti ndi harām. Pomwe ikakhala nkhani yolowetsa maliseche mkamwa mwa mkaziyo, izizi ndi zotsatira za kuonera ma filimu a azungu komanso anthu aku India, Iran ndi mayiko a mbali imeneyi. Sizili zololedwa kuwatsatira mu zimenezi chifukwa zikugwera mu At-Tashabbuh (kutsanzira komwe kuli koletsedwa).”
 
b)    Gulu lachiwiri limati; ndizololedwa mwamuna kunyambita maliseche a mkazi wake ngati sananyowe. Chifukwa madzi amene amatuluka pamene mkazi wamema ndi nyasi ndipo sizili zofunikira kuika nyasi mkamwa. Izinso zili chimodzimodzi pa mkazi kuika maliseche a mwamuna wake mkamwa pamene akutuluka timadzi tosonyeza kuti wamema. Iwo adati izi ndi makrūh (zonyasa) chabe osati harām. Iwo adagwiritsira ntchito āyah yoti:[1]
 
وَلَقَدْ كَرَّمْنَا بَنِىٓ ءَادَمَ وَحَمَلْنَاهُمْ فِى الْبَرِّ وَالْبَحْرِ وَرَزَقْنَاهُم مِّنَ الطَّيِّبَاتِ وَفَضَّلْنَاهُمْ عَلَىٰ كَثِيرٍ مِّمَّنْ خَلَقْنَا تَفْضِيلًا.
 
Ndipo tidawalemekeza Ana a Ādam komanso tidawanyamula pa nthaka ndi pa nyanja; komanso tidawapatsa kuchokera mu zinthu zabwino; komanso tidawalemekeza kuposa zambiri mu zomwe Tidalenga, kulemekeza kopambana.
 
Mu kufotokoza kwawo, iwo amati chilengedwe cha munthu ndi chopambana kuposa chilengedwe cha nyama. Kunyambitana maliseche amachita ndi agalu, ndipo munthu kutsatira zimenezi ndiye kuti akudzifananizira ndi zolengedwa zomwe Allāh sadazipambanitse. Choncho, zili makrūh kupanga zimenezi.
 
c)     Gulu lomaliza limati ndi zololedwa mu njira iliyonse; kaya mkazi kapena mwamuna wamema kapena sanameme. Ndipo iwo amati, zinthu zonse zokhudza kugonana ndi zololedwa kupatulapo zomwe zili ndi umboni kuti zaletsedwa. Ndipo palibe umboni ulionse umene ukuletsa nkhani imeneyi.
 
Ma ulamā’ ambiri amati zili zololedwa kunyambitana maliseche a wina ndi mnzake ndipo nthawi zina zili makrūh.
 
Mu Fatāwā Al-Hindiyyah tipeza mwafotokozedwa kuti:[2]
 
‌إذَا ‌أَدْخَلَ ‌الرَّجُلُ ‌ذَكَرَهُ ‌فِي ‌فَمِ ‌امْرَأَتِهِ قد قيل ‌يَكْرَهُ، ‌وَقَدْ ‌قِيلَ ‌بِخِلَافِهِ كذا في ‌الذُّخَيْرَةِ.
 
Ngati mwamuna walowetsa maliseche ake mkamwa mwa mkazi wake, zimanenedwa kuti ndi makrūh (zonyasa); ndipo mukufotokoza kwina ndi zololedwa (mubāh). 
 
Zaynuddīn Al-Malibarī, yemwe adali wophunzira wa Ibn Hajar Al-Haytamī, adati:[3]
 
يَجُوزُ لِلزَّوْجِ كُلُّ تَمَتُّعٍ مِنْهَا بِمَا سِوَى حَلْقَةِ دُبُرِهَا وَلَوْ بِمَصِّ بَظَرِها أو استمناء بيدها لا بيده.
 
Ndizololedwa kwa mwamuna kuti asangalale ndi thupi lonse la mkazi wake, kupatulapo njira yotulukira chimbudzi; iye atha mpaka kuyamwa mutu wa maliseche a mkaziyo (clitoris), kapena mkazi atha kuseweretsa maliseche a mwamunayo ndi dzanja lake koma mwamunayo sakuyenera kudziseweretsa ndi dzanja lake.
 
Al-Fanānī, yemwe ali wotsatira madh-hab a Imām Ash-Shāf’ī, adati:[4]
 
وَصَرَّحَ الْحَنَابِلَةُ بِجَوَازِ تَقْبِيل الْفَرْجِ قَبْل الْجِمَاعِ، وَكَرَاهَتِهِ بَعْدَهُ.
 
Ophunzira a Imām Ahmad adanenetsa momveka bwino kuti zili zololedwa mwamuna kupsopsona maliseche a mkazi wake asanayambe kugonana, ndipo zili makrūh kuwapsopsona akamaliza kugonanako.
 
Ndipo Al-Hattwāb adati:[5]
 
قَدْ رُوِيَ عَنْ مَالِكٍ أَنَّهُ قَال: لَا بَأْسَ أَنْ يَنْظُرَ إِلَى الْفَرْجِ فِي حَال الْجِمَاعِ، وَزَادَ فِي رِوَايَةٍ: وَيَلْحَسَهُ بِلِسَانِهِ.
 
Zidafotokozedwa kuchokera kwa Mālik (Ibn Anas) kuti iye adati: “Palibe vuto mwamuna kuyang’ana maliseche a mkazi wake pamene akugonana.” Ndipo mu kuyankhula kwina iye adaonjezera kuti: “Komanso kunyambita maliseche a mkazi wakeyo ndi lilime lake.”
 
Kusonyeza kuti madzi amene amatuluka ku maliseche a mkazi sanganenedwe kuti ndi nyasi (najis) pokhapokha pabwere umboni. Abū Hanīfah, Ahmad Ibn Hanbal komanso Ash-Shāf’ī adatsutsa zoti madzi ochokera ku maliseche a mkazi ndi najis. Shaykh Ibn ‘Uthaymīn (pogwirizana ndi zimenezi) adati:[6]
 
وإذا كانت - يعني هذه الإفرازات - من مسلك الذكر فهي طاهرة، لأنها ليست من فضلات الطعام والشراب، فليست بولاً، والأصل عدم النجاسة حتى يقوم الدليل على ذلك، ولأنه لا يلزمه إذا جامع أهله أن يغسل ذكره، ولا ثيابه إذا تلوثت به، ولو كانت نجسة للزم من ذلك أن ينجس المني، لأنه يتلوث بها.
 
Ngati madzi amenewa akutuluka (kuchokera mkati mwa maliseche a mkazi) chifukwa cha kugonana amenewo ndi a ukhondo, koma osati chifukwa choti ndi zotsarira za kudya ndi kumwa; kutanthauza kuti si mikodzo. Tsinde ndi lakuti palibe nyasi pokhapokha pabwere umboni wonena kuti chinthucho ndi nyasi. Chifukwa mwamuna sali wokakamizidwa kutsuka maliseche ake pambuyo poti wagonana ndi mkazi wake, kapenanso kutsuka chovala chake ngati chikazi chagwerapo; zikanati ndi nyasi, ndiye kuti nawonso maniy (umuna) ukanakhalanso nyasi. 
 
Pa chifukwa ichi, mwamuna amene akunyambita chikazi, iyeyu sakunyambita najis chifukwa choti mkati mwa maliseche a mkazi ndi twāhir (moyera), chifukwa choti palibe umboni womwe umanena kuti ndi monyasa. Choncho, mfundo yolondola kwambiri ndi yakuti madzi alionse amene amatuluka kuchokera mmenemo ndi oyera kupatulapo ngati pali umboni wosonyeza kuti ndi nyasi, monga magazi a pa masiku ake (menstrual blood).
 
Zomwe zili zolondola kwambiri ndi zakuti kuyamwana komanso kunyambitana maliseche ndi kololedwa. Titati tivomereze kuti ndi makrūh, chilamulochi chitha kunyamulidwa (osagwiritsidwa ntchito) chifukwa cha kufunikira kwa machitidwewa. Ndipo nzosakaikitsa kuti kufunikiraku apa kukuonekera poyera.
 
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.


[1] Sūrah Al-Isrā’ 17:70


[2] Fatāwā Al-Hindiyyah, Vol. 5, tsamba 372


[3] Fat-hul Mu’īn, tsamba 482


[4] Kash-shāful Qinā, Vol. 5, tsamba 16-17; Al-Mawsū’ah Al-Fiqhiyyah Al-Kuwaytiyyah, Vol. 32, tsamba 16


[5] Mawāhibul Jalīl, Vol.  3, tsamba 406; Al-Mawsū’ah Al-Fiqhiyyah Al-Kuwaytiyyah, Vol. 32, tsamba 90


[6] Ash-Sharh Al-Mumti’, Vol. 1, tsamba 457

Funsoli lakuthandizani?