Kumwa mkaka wa m'mawere a mkazi wako

Download PDF

Lero ndi: Thursday, Rabi' Al-Awwal 25, 1447 5:30 AM | Omwe awerengapo: 550

Funso:

15 September, 2025

Ndimamva kuti mwamuna akamwa mkaka wa m’mawere a mkazi wake ndiye kuti basi pamenepo mkaziyo amakhala harām kwa iyeyo. Kodi izizi ndi zoona?

Yankho:

Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
 
Ngati mkazi ali woyamwitsa mu nthawi yomwe awiriwa akuseweretsana ndipo mawere a mkaziyo akutuluka mkaka, palibe vuto mwamuna wake kuumwa.
 
Anthu ena amayankhula kuti kumwa mkaka wa m’mawere a mkazi wako ndi harām ndipo iwo amagwiritsa ntchito hadīth ya Sālim imene ‘Ā’ishah akufotokoza kuti:[1]
 
أَنَّ سَالِمًا مَوْلَى أَبِي حُذَيْفَةَ كَانَ مَعَ أَبِي حُذَيْفَةَ وَأَهْلِهِ فِي بَيْتِهِمْ، فَأَتَتْ - تَعْنِي ابْنَةَ سُهَيْلٍ - النَّبِيَّ صَلَّى اللهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ، فَقَالَتْ: إِنَّ سَالِمًا قَدْ بَلَغَ مَا يَبْلُغُ الرِّجَالُ، وَعَقَلَ مَا عَقَلُوا، وَإِنَّهُ يَدْخُلُ عَلَيْنَا، وَإِنِّي أَظُنُّ أَنَّ فِي نَفْسِ أَبِي حُذَيْفَةَ مِنْ ذَلِكَ شَيْئًا، فَقَالَ لَهَا النَّبِيُّ صَلَّى اللهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ: ‌أَرْضِعِيهِ ‌تَحْرُمِي ‌عَلَيْهِ، ‌وَيَذْهَبِ ‌الَّذِي ‌فِي ‌نَفْسِ ‌أَبِي ‌حُذَيْفَةَ. فَرَجَعَتْ، فَقَالَتْ: إِنِّي قَدْ أَرْضَعْتُهُ، فَذَهَبَ الَّذِي فِي نَفْسِ أَبِي حُذَيْفَةَ.
 
Sālim adali kapolo woomboredwa ndi Abū Hudhayfah ndipo amakhala naye pamodzi ndi banja lake mnyumba mwake (mwa Abū Hudhayfah). Mkazi wa Abū Hudhayfah adabwera kwa Mtumiki wa Allāh (ﷺ) ndipo adati: “Sālim watha msinkhu ngati momwe amuna amachitira, ndipo akudziwa zomwe amunawo amadziwa. Amalowa mnyumba mwathu mopanda vuto, koma ndikuona kuti izi sizikumusangalatsa Abū Hudhayfah.” Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati: “Mumwetseni mkaka wa m’mawere (ako) ndipo iye adzakhala woletsedwa kukukwatira iweyo, ndipo izi zidzachotsa chomwe chili mu mtima mwa Abū Hudhayfah.” Choncho, mkazi wa Abū Hudhayfah adabweranso (pambuyo pochita izi) ndipo adati: “Ndamupatsa mkaka wa m’mawere, ndipo kunyasidwa kumene kudali mu mtima mwa Abū Hudhayfah kwatha.”
 
Tizindikire kuti Sālim sanamukhudze mkazi wa Abū Hudhayfah. Iye adamwa mkakawo kuchokera mu chikho (kapu). Ibn Hajar akuchitira ndemanga pa hadīth imeneyi motere:[2]
 
فَإِنَّ عِيَاضًا أَجَابَ عَنِ الْإِشْكَالِ بِاحْتِمَالِ أَنَّهَا حَلَبَتْهُ ثُمَّ شَرِبَهُ مِنْ غَيْرِ أَنْ يَمَسَّ ثَدْيَهَا قَالَ النَّوَوِيُّ وَهُوَ احْتِمَالٌ حَسَنٌ.
 
Al-Qādhwī ‘Iyādhw adayankha funso pomasulira kuti mkaka umenewo udaikidwa mu chikho ndipo iye (Sālim) sadamwe kuchokera ku bere la mkaziyo. An-Nawawī adati: Tanthauzo ili ndi limene lili labwino.
 
Ndipo tizindikirenso kuti chigamulo chimenechi chidali cha pakati pa Sālim ndi Abū Hudhayfah basi. Sichidaperekedwe kwa aliyense malinga ndi momwe akuyankhulira ‘Ā’ishah kuti:[3]
 
وَاللَّهِ مَا نَرَى هَذَا إِلَّا رُخْصَةً أَرْخَصَهَا رَسُولُ اللَّهِ صَلَّى اللَّهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ لِسَالِمٍ خَاصَّةً فَمَا هُوَ بِدَاخِلٍ عَلَيْنَا أَحَدٌ بِهَذِهِ الرَّضَاعَةِ وَلَا رَائِينَا.
 
Ndikulumbira mwa Allāh, sitimaitenga nkhani imeneyi kupatulapo kuti ndi chilolezo chimene Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adachipereka kwa Sālim yekha basi. Palibe mwamuna aliyense amene wayamwitsidwa mu njira yotereyi tingamulole kulowa mnyumba zathu, ndipo zimenezo si zomwe tidagwiritsa (kuti mwamuna wa mkulu adzimwa mkaka wa m’mawere ndi cholinga choti akhale mahram).
 
Choncho, mupeza kuti omwe adali ophunzira pakati pa ma Swahābah sadalole kuti anthu akutenge kuyamwitsa munthu wa mkulu (pomupatsa mkaka wa m’mawere) kukhala njira yopangitsa woyamwayo kukhala mahram. Abū ‘Atwiyyah Al-Wādi’ī akufotokoza kuti:[4]
 
جَاءَ رَجُلٌ إِلَى ابْنِ مَسْعُودٍ، فَقَالَ: إِنَّهَا كَانَتْ مَعِي امْرَأَتِي، فَحُصِرَ لَبَنُهَا فِي ثَدْيِهَا، فَجَعَلْتُ أَمَصُّهُ ثُمَّ أَمَجُّهُ، فَأَتَيْتُ أَبَا مُوسَى فَسَأَلْتُهُ، فَقَالَ: حَرُمَتْ عَلَيْكَ. قَالَ: فَقَامَ وَقُمْنَا مَعَهُ، حَتَّى انْتَهَى إِلَى أَبِي مُوسَى، فَقَالَ: مَا أَفْتَيْتَ هَذَا، فَأَخْبَرَهُ بِالَّذِي أَفْتَاهُ. فَقَالَ ابْنُ مَسْعُودٍ، وَأَخَذَ بِيَدِ الرَّجُلِ: «أَرِضِيعًا تَرَى هَذَا إِنَّمَا الرَّضَاعُ مَا أَنْبَتَ اللَّحْمَ وَالدَّمَ». فَقَالَ أَبُو مُوسَى: لَا تَسْأَلُونِي عَنْ شَيْءٍ مَا كَانَ هَذَا الْحَبْرُ بَيْنَ أَظْهُرِكُمْ .
 
Mwamuna wina anabwera kwa Ibn Mas’ūd ndipo adati kwa iye: “Mkazi wanga anali ndi ine ndipo mawere ake anadzadza ndi mkaka (kutupa chifukwa cha kuchuluka kwa mkaka). Choncho, ndinayamba kuuyamwa (mkakawo) kenako ndi kumaulavula. Ndiye ndinapita kwa Abū Mūsā (Al-‘Ash’arī) ndipo ndidamufunsa.” Ibn Mas’ūd adati (kwa Abū Mūsā): “Unamuyankha chani munthuyu?” Choncho, iye (Abū Mūsā) adafotokoza zomwe adamuyankhazo. Kenako Ibn Mas’ūd adaimirira, natenga dzanja la mwamuna uja ndi kufunsa kuti: “Kodi dzanja ili likuoneka ngati ndi la khanda? Kuyamwa (kumene kumapangitsa kuti mwamuna akhale woletsedwa kwa mkaziyo) ndi kumene kumakulitsa minofu ndi kuchulukitsa magazi mthupi.” Abū Mūsā adati (kwa mwamuna uja): “Osadzandifunsanso mukakhala ndi wophunzira uyu pakati panu (kunena Ibn Mas’ūd)”
 
'Abdullāh Ibn ‘Umar akufotokoza kuti:[5]
 
جَاءَ رَجُلٌ إِلَى عُمَرَ بْنِ الْخَطَّابِ، فَقَالَ: إِنِّي كَانَتْ لِي وَلِيدَةٌ، وَكُنْتُ أَطَؤُهَا فَعَمَدَتِ امْرَأَتِي إِلَيْهَا فَأَرْضَعَتْهَا، فَدَخَلْتُ عَلَيْهَا، فَقَالَتْ: دُونَكَ، فَقَدْ وَاللَّهِ أَرْضَعْتُهَا، فَقَالَ عُمَرُ: ‌أَوْجِعْهَا، ‌وَأْتِ ‌جَارِيَتَكَ، ‌فَإِنَّمَا الرَّضَاعَةُ رَضَاعَةُ الصَّغِيرِ.
 
Mwamuna wina anabwera kwa ‘Umar Ibnil Khattwāb ndipo adati kwa iye: “Ndili ndi mzakazi yemwe ndimakonda kugonana naye; koma mkazi wanga adapita kwa iye kukamupatsa mkaka wa m’mawere ake ndipo pamene ine ndidapita kwa mzakaziyu, iye adati: ‘Siya (usalowetse maliseche ako kwa ine), ndikulumbira mwa Allāh, ndapatsidwa mkaka (ndi mkazi wako choncho sindilinso wololedwa pa iwe).’” ‘Umar adati kwa mwamunayu: “Pereka chilango kwa mkazi wakoyo, ndipo pitiriza kupita kwa mzakaziyo (udzikagonana nayebe); chifukwa kuyamwa (komwe kumachititsa kuti munthu akhale wosaloledwa kuchita naye nikāh komanso kugonana naye) kumagwira ntchito pa makanda okha basi (pamene ayamwitsidwa ndi mayi kodutsa kasanu asanakwanitse zaka ziwiri ndipo apa amakhala mahram).” 
 
Pa chifukwa ichi, sizili zoona kunena kuti ndi harām mwamuna kumwa mkaka wa m’mawere a mkazi wake ngati momwe amayankhulira anthu ena. Ndipo ena amati ndi makrūh (zosakondedwa); koma izizi sizoona.
 
Shaykh Ibn ‘Uthaymīn adafunsidwapo za nkhaniyi ndipo iwo adati:[6]
 
رضاع الكبير لا يؤثّر؛ لأنّ الرضاع المؤثّر هو ما كان خمس رضعات فأكثر في الحولين قبل الفطام، وعلى هذا فلو قُدِّر أنّ أحدا رضع من زوجته أو شرب من لبنها فإنه لا يكون ابنا لها.
 
Kuyamwitsa munthu wa mkulu kulibe vuto (sizingatheke kuti iyeyo asanduke mahram); chifukwa kuyamwitsa komwe kuli vuto (kumene kumampangitsa munthu kuti akhale mahram) ndi uko kumene mwana amayamwa kokwana kasanu kapena kupyolera apo mu zaka ziwiri zoyambirira (pambuyo pa kubadwa mwanayo), ndipo iye ayamwe mkaka usanaume (asanasiitsidwe kuyamwa). Potengera izi, ngati mwamuna wapezeka kuti wayamwa mkaka wa mkazi wake, iyeyu sasanduka mwana wake (wa mkaziyu).
 
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.


[1] Swahīh Muslim, #1453


[2] Fat-hul Bārī, Vol. 9, tsamba 148


[3] Swahīh Muslim, #1454


[4] Al-Muswannaf ya ‘Abdur-Razzāq, Vol. 7, tsamba 463, #13895


[5] Muwattwa’ Mālik, Vol. 2, tsamba 606, #13


[6] Fatāwā Islāmiyyah, Vol. 3, tsamba 338

Funsoli lakuthandizani?