Mlingo wa Mahr

Download PDF

Lero ndi: Thursday, Rabi' Al-Awwal 25, 1447 5:31 AM | Omwe awerengapo: 384

Funso:

15 September, 2025

As-Salam aleykum warahmatullah wabarakatuuh! Sheikh ndili ndifunso pa nkhani ya nikāh; sheikh kodi mkazi akatchaja ndalama ya mahari, kodi pali kunena kuti yachepa nikah palibe kumangitsa chifukwa ndalama yachepa koma iziyambila mwakuti-mwakuti.

Yankho:

Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
 
Sitikupezamo mu chiphunzitso cha Mtumiki wa Allāh (ﷺ) kuti iyeyo adawakhazikitsira asilamu mulingo wa mahr. Palibe vuto mkazi kutchula mahr yokwererako kapena yotsikirako. Koma mahr yomwe ili ndi madalitso pamaso pa Allāh ndi yomwe imakhala yochepa yoti mwamunayo samavutika kaperekedwe kake. Ma walī ena amakweza mahr ya mwana wawo wa mkazi ndipo izi zimachititsa kuti mwamuna alephere kumukwatira mwanayo.
 
Chiphunzitso ichi tikuchipeza mu hadīth ya Uqbah Ibn ‘Āmir ndipo iye akunena kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[1]
 
‌خَيْرُ ‌الصَّدَاقِ ‌أَيْسَرُهُ.
 
“Mahr yabwino ndi imene imakhala yophweka kuperekedwa (yochepa).”
 
Ndidayendetsapo mwambo wa nikāh umene mkazi adatchula mahr imene idaimitsa tsitsi langa. Mahr imeneyi ambiri atha kuganiza kuti idali yochuluka kwambiri. Koma sichoncho. Mahr imeneyi idali yotsika kufikira kuti ndidafunsa walī wa mkaziyu kuti atchulenso. Ndipo iye adandiuzadi kuti ndi momwemo ndipo anakamufunsanso mkaziyo ngati sadalakwitse matchulidwewo koma mkaziyo adanenetsa kuti ndi momwemo. Iye adatchula mahr ya K50 basi. Walī poyankhula m'malo mwa mkaziyo adati: “Iyeyo sakukwatiwa kwa ndalama koma kwa mwamuna.”
 
Mu kuyankhula kwake ‘Umar Ibnil Khattwāb adafotokoza kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[2]
 
خَيْرُ النِّكَاحِ أَيْسَرُهُ.
 
“Nikāh yabwino ndi yomwe ili yofewa (yosakhala ya mtengo wapatali).”
 
‘Ā`ishah adapereka uthenga woti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[3]
 
إِنَّ مِنْ يُمْنِ الْمَرْأَةِ: تَيْسِيرَ خِطْبَتِهَا، وَتَيْسِيرَ صَدَاقِهَا، وَتَيْسِيرَ رَحِمِهَا.
 
“Zina mwa zizindikiro zoti mkazi ndi wodalitsika: kumutomera kwake sikumakhala kovuta, mahr imene amatchula imakhala yofewa, komanso amabereka ana mosavutikira.”
 
Abī Al-Ajfā’ī As-Sulamī adati:[4]
 
قَالَ عُمَرُ بْنُ الْخَطَّابِ: أَلاَ! لاَ تُغَالُوا صَدُقَةَ النِّسَاءِ فَإِنَّهَا لَوْ كَانَتْ مَكْرُمَةً فِي الدُّنْيَا أَوْ تَقْوَى عِنْدَ اللَّهِ، لَكَانَ أَوْلاَكُمْ بِهَا نَبِيُّ اللَّهِ صلى الله عليه وسلم. مَا عَلِمْتُ رَسُولَ اللَّهِ صلى الله عليه وسلم نَكَحَ شَيْئًا مِنْ نِسَائِهِ وَلاَ أَنْكَحَ شَيْئًا مِنْ بَنَاتِهِ عَلَى أَكْثَرَ مِنْ ثِنْتَىْ عَشْرَةَ أُوقِيَّةً.‏ وَإِنَّ الرَّجُلَ لَيُثَقِّلُ صَدَقَةَ امْرَأَتِهِ حَتَّى يَكُونَ لَهَا عَدَاوَةٌ فِي نَفْسِهِ وَيَقُولُ قَدْ كَلِفْتُ إِلَيْكِ عَلَقَ الْقِرْبَةِ أَوْ عَرَقَ الْقِرْبَةِ.
 
‘Umar Ibnil Khattwāb adati: “Zindikirani! Simukuyenera kupyola malire pa nkhani ya mahr ya akazi. Chifukwatu zikadati ndi zolemekezeka padziko pano (kuchulutsa mahr) kapena kukhala chizindikiro chosonyeza kuopa Allāh, amene akadakhala woyambirira mwa inu kuchita zimenezo akanakhala Mtumiki wa Allāh (ﷺ). Koma sindidamvepo kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adapereka mahr kwa m’modzi wa akazi ake kapena kulandira mahr ya m’modzi wa ana ake chilichonse choposera ma ūqiyyah 12. Ndipo mwamuna atha kumaonjezera (kupereka) mahr yambiri pa mkazi wake mpaka kufikira pomamuda mkaziyo ndi kumayankhula kuti: “Unanditengera chili chonse chomwe ndinali nacho.” Kapena, “Unandibweretsera chipsinjo chachikulu (kudzera mu mahr yomwe udandilamula).”
 
Mu hadīth ya ‘Ā`ishah, tipeza kuti Abī Salamah Ibn Abdur-Rahmān akunena kuti:[5]
 
سَأَلْتُ عَائِشَةَ: ‌كَمْ ‌كَانَ ‌صَدَاقُ ‌رَسُولِ اللهِ صَلَّى اللهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ؟ قَالَتْ: كَانَ صَدَاقُهُ لِأَزْوَاجِهِ اثْنَتَيْ عَشْرَةَ أُوقِيَّةً وَنَشًّا، قَالَتْ: أَتَدْرِي مَا النَّشُّ؟ قُلْتُ: لَا، قَالَتْ: نِصْفُ أُوقِيَّةٍ، فَتِلْكَ خَمْسُ مِائَةِ دِرْهَمٍ، فَهَذَا صَدَاقُ رَسُولِ اللهِ صَلَّى اللهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ لِأَزْوَاجِهِ.
 
Ndinamufunsa ‘Ā`ishah: “Kodi mahr ya Mtumiki wa Allāh (ﷺ) idali yochuluka bwanji?” Iye adati: “Iye adali kuwapatsa akazi ake ma ūqiyyah okwanira 12 ndi Nash-sh.” ‘Ā`ishah adati: “Kodi ukuidziwa An-Nash-sh kuti ndi chani?” Ndidati: “Ayi.” Iye adati: “Theka la ūqiyyah (imodzi). Ndipo zonse pamodzi zimakwana 500 darāhim. Ndipo imeneyo idali mahr ya Mtumiki wa Allāh (ﷺ) pa azikazi ake.”
 
Ma ūqiyyah 12 akukwanira 480 darāhim zomwe pafupifupi zikukwanira ma riyāl a siliva 135 (riyāl ndi ndalama ya ku Saudi Arabia). Mu ma dollar, itha kukwana pafupifupi $36. Ndalama imeneyi ikhonza kuoneka ngati yochuluka mu nthawi yathu ino, koma mu nthawi imeneyo siidali ndalama yambiri kwa iwowo.
 
Apa mwamuna kuyankhula kwa mkazi wake kuti: “Unandibweretsera chipsinjo chachikulu,” zikutanthauza kuti mwamuna uja kumamudandaula wa mkaziyu mu nthawi yomwe akuperekabe mahr chifukwa choti idali yochuluka. Kapena ngati adakwanitsa kupereka koma pambuyo pake nkukhala mu ngongole kapena kukhaliratu opanda kalikonse kumene.
 
Shaykh Al-Islām Ibn Taymiyyah adati:[6]
 
لَا يَزِيدُ عَلَى مَهْرِ أَزْوَاجِ النَّبِيِّ صَلَّى اللَّهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ وَلَا بَنَاتِهِ وَكَانَ مَا بَيْنَ أَرْبَعِ مِائَةٍ إلَى خَمْسِ مِائَةٍ بِالدَّرَاهِمِ. فَهَذِهِ سُنَّةُ رَسُولِ اللَّهِ صَلَّى اللَّهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ مَنْ فَعَلَ ذَلِكَ فَقَدْ اسْتَنَّ بِسُنَّةِ رَسُولِ اللَّهِ صَلَّى اللَّهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ فِي الصَّدَاقِ. فَمَنْ دَعَتْهُ نَفْسُهُ إلَى أَنْ يَزِيدَ صَدَاقَ ابْنَتِهِ عَلَى صَدَاقِ بَنَاتِ رَسُولِ اللَّهِ صَلَّى اللَّهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ اللَّوَاتِي هُنَّ خَيْرُ خَلْقِ اللَّهِ فِي كُلِّ فَضِيلَةٍ وَهُنَّ أَفْضَلُ نِسَاءِ الْعَالَمِينَ فِي كُلِّ صِفَةٍ: فَهُوَ جَاهِلٌ أَحْمَقُ. وَكَذَلِكَ صَدَاقُ أُمَّهَاتِ الْمُؤْمِنِينَ. وَهَذَا مَعَ الْقُدْرَةِ وَالْيَسَارِ فَأَمَّا الْفَقِيرُ وَنَحْوُهُ فَلَا يَنْبَغِي لَهُ أَنْ يُصْدِقَ الْمَرْأَةَ إلَّا مَا يَقْدِرُ عَلَى وَفَائِهِ مِنْ غَيْرِ مَشَقَّةٍ.
 
Sidaonjezeredwe mahr ya Mtumiki (ﷺ) pa akazi ake angakhalenso pa ana ake aakazi kupatula kuti idali pakati pa 400 ndi 500 darāhim. Iyi ndiyo idali Sunnah ya Mtumiki wa Allāh (ﷺ), ndipo aliyense amene wachita izi, iyeyo watsatira Sunnah ya Mtumiki wa Allāh (ﷺ) pa nkhani ya mahr. Ndipo aliyense amene ataganize zokweza mahr ya mwana wake wa mkazi ndi kuchulutsa kuposa yomwe ana aakazi a Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adapatsidwa – pomwe iwowo adali akazi abwino kwambiri padziko pano pa chilichonse, komanso iwowo nkukhala akazi opambana mu mbiri zawo zonse; ameneyo ndi mbuli yotheratu. Izinso zili chimodzimodzi mahr ya amayi a okhulupirira (omwe ali akazi ake a Mtumiki ﷺ). Sizikutengera kuti kapena mwamunayo ndi wolemera kuti atha kukwanitsa. Tsopano akakhala kuti mwamunayo ndi wosauka, sizili zoyenera kupereka mahr kwa mkazi kupatula yomwe iyeyu angakwanitse komanso atha kupereka mopanda chipsinjo.
 
Choncho, ndi mustahabb kutchula mahr ya pakati pa 400 ndi 500 darāhim kwa mwamuna amene angakwanitse. Ndipo zili bwino kwambiri kumuchepetseranso pamenepo. Mahr yabwino ndi imene imakhala yofewa kwa mwamunayo kupereka.
 
Sizilinso zokondedwa kuti mwamuna apereke ndendende mmene Mtumiki (ﷺ) ankaperekera kwa azikazi ake kapena mmene ankalandirira mahr ya ana ake aakazi, ngati iyeyo sangakwanitse. Abū Hurayrah akufotokoza kuti:[7]
 
جَاءَ رَجُلٌ إِلَى النَّبِيِّ صلى الله عليه وسلم فَقَالَ إِنِّي تَزَوَّجْتُ امْرَأَةً مِنَ الأَنْصَارِ.‏ فَقَالَ لَهُ النَّبِيُّ صلى الله عليه وسلم:‏‏ هَلْ نَظَرْتَ إِلَيْهَا فَإِنَّ فِي عُيُونِ الأَنْصَارِ شَيْئًا.‏ قَالَ قَدْ نَظَرْتُ إِلَيْهَا‏.‏ قَالَ: عَلَى كَمْ تَزَوَّجْتَهَا‏.‏ قَالَ عَلَى أَرْبَعِ أَوَاقٍ.‏ فَقَالَ لَهُ النَّبِيُّ صلى الله عليه وسلم:‏ عَلَى أَرْبَعِ أَوَاقٍ؟ كَأَنَّمَا تَنْحِتُونَ الْفِضَّةَ مِنْ عُرْضِ هَذَا الْجَبَلِ مَا عِنْدَنَا مَا نُعْطِيكَ وَلَكِنْ عَسَى أَنْ نَبْعَثَكَ فِي بَعْثٍ تُصِيبُ مِنْهُ‏.‏ قَالَ: فَبَعَثَ بَعْثًا إِلَى بَنِي عَبْسٍ بَعَثَ ذَلِكَ الرَّجُلَ فِيهِمْ.‏
 
Mwamuna anabwera kwa Mtumiki wa Allāh (ﷺ) ndipo adati: “Ndakwatira mkazi kuchokera mu mtundu wa ma Answāri.” Apa Mtumiki (ﷺ) adati: “Kodi wamuona kale mkaziyo? Chifukwa m’maso mwa ma Answāri muli kenakake (muli nsanje).” Mwamuna uja adati: “Eya ndamuona mkaziyo.” Kenako Mtumiki (ﷺ) adati: “Wapereka mahr yochuluka bwanji?” Iye adati: “Ma ūqiyyah okwana anayi.” Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati: “Ma ūqiyyah okwanira anayi? Zikukhala ngati kuti akuona ngati umakumba siliva m’mbali mwa phiri (nchifukwa chake ukuoneka wokonzekera choncho kuti upereke mahr yochuluka choncho?). Ife tilibe kalikonse koti tikupatse iwe. Koma pali kuthekera koti titha kukutumiza (limodzi ndi gulu la nkhondo) komwe utha kukapeza kenakake (kuchokera mu katundu wopezedwa ku nkhondoko).” Choncho, Mtumiki (ﷺ) adamutumiza iye pamodzi ndi gulu la nkhondo lomwe limapita ku Bani ‘Abs.
 
Zolinga zochepetsera mahr ndi zakuti: zimakhala zophweka kwa amuna kuti akwatire, ndipo izi zimapangitsa iwowo kuti asatenge njira za chidule zimene zaononga mtundu wa anthu.
 
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.


[1] As-Sunan Al-Kubrā lil Bayhaqī, Vol. 7, tsamba 379, hadīth #14332


[2] Sunan Abī Dāwūd, #2117


[3] Musnad Ahmad, #23957; Ibn Hibbān, #4095


[4] Jāmi’at Tirmidhī, #1114b; Sunan Ibn Mājah, #1886


[5] Musnad Ahmad, #24626; Swahīh Muslim, #1426


[6] Majmū’ Al-Fatāwā (Vol. 31, tsamba)


[7] Swahīh Muslim, #1424

Funsoli lakuthandizani?