Kodi kukuchekera mphini chifukwa ukudwala mutu waching'alang'ala pofuna kuti mankhwala alowelele ndizololedwa?
Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
Choyamba, Chisilamu ndi chipembedzo chimene chalimbikitsa anthu ake kuti adzisakasaka mankhwala mu njira yovomerezeka pamene iwowo adwala. Usāmah Ibn Sharīk akufotokoza kuti:[1]
قَالَتِ الأَعْرَابُ: يَا رَسُولَ اللَّهِ! أَلاَ نَتَدَاوَى؟ قَالَ: نَعَمْ، يَا عِبَادَ اللَّهِ! تَدَاوَوْا؛ فَإِنَّ اللَّهَ لَمْ يَضَعْ دَاءً إِلاَّ وَضَعَ لَهُ شِفَاءً. أَوْ قَالَ: دَوَاءً إِلاَّ دَاءً وَاحِدًا. قَالُوا: يَا رَسُولَ اللَّهِ! وَمَا هُوَ؟ قَالَ: الْهَرَمُ.
Adayankhula anthu (achi Arab) ochokera ku mudzi: ‘Eh iwe Mtumiki wa Allāh (ﷺ)! Kodi sitingasakesake mankhwala (kuti tipeze m’menemo machiritso)?’ Iye adati: “Inde, eh inu akapolo a Allāh! Sakanisakani mankhwala. Chifukwa Ndithudi Allāh sadapange nthenda, kupatula kuti adaipangiranso machiritso.” Kapena adati: “mankhwala kupatulapo nthenda imodzi.” Iwo adati; ‘Eh iwe Mtumiki wa Allāh (ﷺ)! Nthenda imeneyo ndi iti?’ Iye adati: “Ukalamba.”
Choncho, njira zimene zili zololedwa ndi Shari’ah kuti munthu apezere mankhwala zitha kutsatiridwa.
Chachiwiri, ngati amene akutema phiniyo ndi msing’anga; sizili zololedwa kupita kwa iyeyo ngakhale kukatemetsa mphini za mutu wa ching’alang’ala. Chifukwa pali chiletso kuchokera kwa Mtumiki wa Allāh (ﷺ) pa nkhani yopita kwa asing’anga, abimbi, afiti (m’menemunso muli onse olemba matalasimu) kapena amaula.
Palibe vuto kukutemani mphini munthu wina posakhala amene atchulidwawa.
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.
[1] Sunan at-Tirmidhī, #2038
